< Job 27 >
1 Job prit de nouveau la parole sous forme sentencieuse et dit:
Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
2 Dieu qui me refuse justice est vivant! Le Tout-Puissant qui remplit mon âme d’amertume est vivant!
“Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama, Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
3 Aussi longtemps que j’aurai ma respiration, Et que le souffle de Dieu sera dans mes narines,
nthawi zonse pamene ndili ndi moyo, mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
4 Mes lèvres ne prononceront rien d’injuste, Ma langue ne dira rien de faux.
pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa, lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
5 Loin de moi la pensée de vous donner raison! Jusqu’à mon dernier soupir je défendrai mon innocence;
Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona; mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
6 Je tiens à me justifier, et je ne faiblirai pas; Mon cœur ne me fait de reproche sur aucun de mes jours.
Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere; chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.
7 Que mon ennemi soit comme le méchant, Et mon adversaire comme l’impie!
“Mdani wanga akhale ngati woyipa, wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
8 Quelle espérance reste-t-il à l’impie, Quand Dieu coupe le fil de sa vie, Quand il lui retire son âme?
Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu achotsa moyo wake?
9 Est-ce que Dieu écoute ses cris, Quand l’angoisse vient l’assaillir?
Kodi Mulungu amamva kulira kwake pamene zovuta zamugwera?
10 Fait-il du Tout-Puissant ses délices? Adresse-t-il en tout temps ses prières à Dieu?
Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse? Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
11 Je vous enseignerai les voies de Dieu, Je ne vous cacherai pas les desseins du Tout-Puissant.
“Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
12 Mais vous les connaissez, et vous êtes d’accord; Pourquoi donc vous laisser aller à de vaines pensées?
Inu mwadzionera nokha zonsezi. Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?
13 Voici la part que Dieu réserve au méchant, L’héritage que le Tout-Puissant destine à l’impie.
“Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa, cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
14 S’il a des fils en grand nombre, c’est pour le glaive, Et ses rejetons manquent de pain;
Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
15 Ceux qui échappent sont enterrés par la peste, Et leurs veuves ne les pleurent pas.
Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri, ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 S’il amasse l’argent comme la poussière, S’il entasse les vêtements comme la boue,
Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, ndi kukundika zovala ngati mchenga,
17 C’est lui qui entasse, mais c’est le juste qui se revêt, C’est l’homme intègre qui a l’argent en partage.
zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale, ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
18 Sa maison est comme celle que bâtit la teigne, Comme la cabane que fait un gardien.
Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche, ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19 Il se couche riche, et il meurt dépouillé; Il ouvre les yeux, et tout a disparu.
Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko; akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
20 Les terreurs le surprennent comme des eaux; Un tourbillon l’enlève au milieu de la nuit.
Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula; mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
21 Le vent d’orient l’emporte, et il s’en va; Il l’arrache violemment de sa demeure.
Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo imamuchotsa pamalo pake.
22 Dieu lance sans pitié des traits contre lui, Et le méchant voudrait fuir pour les éviter.
Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni, pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
23 On bat des mains à sa chute, Et on le siffle à son départ.
Mphepoyo imamuwomba ndithu ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”