< Jérémie 34 >

1 La parole qui fut adressée à Jérémie de la part de l’Éternel, en ces mots, lorsque Nebucadnetsar, roi de Babylone, avec toute son armée, et tous les royaumes des pays sous sa domination, et tous les peuples, faisaient la guerre à Jérusalem et à toutes les villes qui en dépendaient:
Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi gulu lake lonse lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankawalamulira ndiponso anthu a mitundu yonse ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yonse yozungulira Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti,
2 Ainsi parle l’Éternel, le Dieu d’Israël: Va, et dis à Sédécias, roi de Juda, dis-lui: Ainsi parle l’Éternel: Voici, je livre cette ville entre les mains du roi de Babylone, et il la brûlera par le feu.
“Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto.
3 Et toi, tu n’échapperas pas à ses mains, mais tu seras pris et livré entre ses mains, tes yeux verront les yeux du roi de Babylone, et il te parlera bouche à bouche, et tu iras à Babylone.
Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni.
4 Seulement écoute la parole de l’Éternel, Sédécias, roi de Juda! Ainsi parle l’Éternel sur toi: Tu ne mourras point par l’épée.
“Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo;
5 Tu mourras en paix; et comme on a brûlé des parfums pour tes pères, les anciens rois qui t’ont précédé, ainsi on en brûlera pour toi, et l’on te pleurera, en disant: Hélas, seigneur! Car j’ai prononcé cette parole, dit l’Éternel.
udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.”
6 Jérémie, le prophète, dit toutes ces paroles à Sédécias, roi de Juda, à Jérusalem.
Ndipo mneneri Yeremiya anawuza zonsezi Zedekiya mfumu ya Yuda, mu Yerusalemu.
7 Et l’armée du roi de Babylone combattait contre Jérusalem et contre toutes les autres villes de Juda, contre Lakis et Azéka, car c’étaient des villes fortes qui restaient parmi les villes de Juda.
Nthawi imeneyi nʼkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda ina yotsala ya Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiye inali mizinda yotetezedwa yotsala ya ku Yuda.
8 La parole fut adressée à Jérémie de la part de l’Éternel, après que le roi Sédécias eut fait un pacte avec tout le peuple de Jérusalem, pour publier la liberté,
Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya. Nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Zedekiya atachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo awo adzawamasule.
9 afin que chacun renvoyât libres son esclave et sa servante, l’Hébreu et la femme de l’Hébreu, et que personne ne tînt plus dans la servitude le Juif, son frère.
Aliyense amene anali ndi akapolo a Chihebri, aamuna kapena aakazi awamasule; palibe amene ayenera kusunga mu ukapolo Myuda mnzake.
10 Tous les chefs et tout le peuple, qui étaient entrés dans le pacte, s’engagèrent à renvoyer libres chacun son esclave et sa servante, afin de ne plus les tenir dans la servitude; ils obéirent, et les renvoyèrent.
Choncho akuluakulu pamodzi ndi anthu onse amene anachita pangano ili anagwirizana kuti amasule akapolo awo aamuna ndi aakazi ndi kuti asawasungenso mu ukapolo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anawamasuladi.
11 Mais ensuite ils changèrent d’avis; ils reprirent les esclaves et les servantes qu’ils avaient affranchis, et les forcèrent à redevenir esclaves et servantes.
Koma pambuyo pake anasintha maganizo awo ndi kuwatenganso amuna ndi akazi amene anawamasula aja ndipo anawasandutsanso akapolo.
12 Alors la parole de l’Éternel fut adressée à Jérémie de la part de l’Éternel, en ces mots:
Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti:
13 Ainsi parle l’Éternel, le Dieu d’Israël: J’ai fait une alliance avec vos pères, le jour où je les ai fait sortir du pays d’Égypte, de la maison de servitude; et je leur ai dit:
“Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati,
14 Au bout de sept ans, chacun de vous renverra libre son frère hébreu qui se vend à lui; il te servira six années, puis tu le renverras libre de chez toi. Mais vos pères ne m’ont point écouté, ils n’ont point prêté l’oreille.
‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse.
15 Vous, vous aviez fait aujourd’hui un retour sur vous-mêmes, vous aviez fait ce qui est droit à mes yeux, en publiant la liberté chacun pour son prochain, vous aviez fait un pacte devant moi, dans la maison sur laquelle mon nom est invoqué.
Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi.
16 Mais vous êtes revenus en arrière, et vous avez profané mon nom; vous avez repris chacun les esclaves et les servantes que vous aviez affranchis, rendus à eux-mêmes, et vous les avez forcés à redevenir vos esclaves et vos servantes.
Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu.
17 C’est pourquoi ainsi parle l’Éternel: Vous ne m’avez point obéi, en publiant la liberté chacun pour son frère, chacun pour son prochain. Voici, je publie contre vous, dit l’Éternel, la liberté de l’épée, de la peste et de la famine, et je vous rendrai un objet d’effroi pour tous les royaumes de la terre.
“Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
18 Je livrerai les hommes qui ont violé mon alliance, qui n’ont pas observé les conditions du pacte qu’ils avaient fait devant moi, en coupant un veau en deux et en passant entre ses morceaux;
Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo.
19 je livrerai les chefs de Juda et les chefs de Jérusalem, les eunuques, les sacrificateurs, et tout le peuple du pays, qui ont passé entre les morceaux du veau;
Amene ankadutsa pakati pa zigawozo anali atsogoleri a Yuda ndi Yerusalemu, akuluakulu a bwalo, ansembe ndi anthu onse a mʼdzikomo.
20 je les livrerai entre les mains de leurs ennemis, entre les mains de ceux qui en veulent à leur vie, et leurs cadavres serviront de pâture aux oiseaux du ciel et aux bêtes de la terre.
Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi.
21 Je livrerai Sédécias, roi de Juda, et ses chefs, entre les mains de leurs ennemis, entre les mains de ceux qui en veulent à leur vie, entre les mains de l’armée du roi de Babylone, qui s’est éloignée de vous.
“Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo.
22 Voici, je donnerai mes ordres, dit l’Éternel, et je les ramènerai contre cette ville; ils l’attaqueront, ils la prendront, et la brûleront par le feu. Et je ferai des villes de Juda un désert sans habitants.
Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”

< Jérémie 34 >