< Jérémie 15 >

1 L’Éternel me dit: Quand Moïse et Samuel se présenteraient devant moi, Je ne serais pas favorable à ce peuple. Chasse-le loin de ma face, qu’il s’en aille!
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite!
2 Et s’ils te disent: Où irons-nous? Tu leur répondras: Ainsi parle l’Éternel: A la mort ceux qui sont pour la mort, A l’épée ceux qui sont pour l’épée, A la famine ceux qui sont pour la famine, A la captivité ceux qui sont pour la captivité!
Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti, “‘Oyenera kufa adzafa; oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga; oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala; oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
3 J’enverrai contre eux quatre espèces de fléaux, dit l’Éternel, L’épée pour les tuer, Les chiens pour les traîner, Les oiseaux du ciel et les bêtes de la terre Pour les dévorer et les détruire.
“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.
4 Je les rendrai un objet d’effroi pour tous les royaumes de la terre, A cause de Manassé, fils d’Ézéchias, roi de Juda, Et de tout ce qu’il a fait dans Jérusalem.
Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
5 Qui aura pitié de toi, Jérusalem, Qui te plaindra? Qui ira s’informer de ton état?
“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu? Kodi adzakulira ndani? Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
6 Tu m’as abandonné, dit l’Éternel, tu es allée en arrière; Mais j’étends ma main sur toi, et je te détruis, Je suis las d’avoir compassion.
Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova. “Inu mukubwererabe mʼmbuyo. Choncho Ine ndidzakukanthani. Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
7 Je les vanne avec le vent aux portes du pays; Je prive d’enfants, je fais périr mon peuple, Qui ne s’est pas détourné de ses voies.
Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
8 Ses veuves sont plus nombreuses que les grains de sable de la mer; J’amène sur eux, sur la mère du jeune homme, Le dévastateur en plein midi; Je fais soudain tomber sur elle l’angoisse et la terreur.
Ndinachulukitsa amayi awo amasiye kupambana mchenga wa kunyanja. Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna dzuwa lili pamutu. Mwadzidzidzi ndinawagwetsera kuwawa mtima ndi mantha.
9 Celle qui avait enfanté sept fils est désolée, Elle rend l’âme; Son soleil se couche quand il est encore jour; Elle est confuse, couverte de honte. Ceux qui restent, je les livre à l’épée devant leurs ennemis, Dit l’Éternel.
Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka ndipo akupuma wefuwefu. Dzuwa lake lalowa ukanali usana; anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru. Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,” akutero Yehova.
10 Malheur à moi, ma mère, de ce que tu m’as fait naître Homme de dispute et de querelle pour tout le pays! Je n’emprunte ni ne prête, Et cependant tous me maudissent.
Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine, munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse! Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu, komatu aliyense akunditemberera.
11 L’Éternel dit: Certes, tu auras un avenir heureux; Certes, je forcerai l’ennemi à t’adresser ses supplications, Au temps du malheur et au temps de la détresse.
Yehova anati, “Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino. Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka ndi ya mavuto awo.
12 Le fer brisera-t-il le fer du septentrion et l’airain?
“Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo, makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.
13 Je livre gratuitement au pillage tes biens et tes trésors, A cause de tous tes péchés, sur tout ton territoire.
Anthu ako ndi chuma chako ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu onse a mʼdziko lanu lonse.
14 Je te fais passer avec ton ennemi dans un pays que tu ne connais pas, Car le feu de ma colère s’est allumé, Il brûle sur vous.
Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu mʼdziko limene inu simulidziwa, chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto umene udzakutenthani.”
15 Tu sais tout, ô Éternel, souviens-toi de moi, ne m’oublie pas, Venge-moi de mes persécuteurs! Ne m’enlève pas, tandis que tu te montres lent à la colère! Sache que je supporte l’opprobre à cause de toi.
Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse; kumbukireni ndi kundisamalira. Ndilipsireni anthu ondizunza. Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga. Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
16 J’ai recueilli tes paroles, et je les ai dévorées; Tes paroles ont fait la joie et l’allégresse de mon cœur; Car ton nom est invoqué sur moi, Éternel, Dieu des armées!
Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.
17 Je ne me suis point assis dans l’assemblée des moqueurs, afin de m’y réjouir; Mais à cause de ta puissance, je me suis assis solitaire, Car tu me remplissais de fureur.
Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera, sindinasangalale nawo anthu amenewo. Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.
18 Pourquoi ma souffrance est-elle continuelle? Pourquoi ma plaie est-elle douloureuse, et ne veut-elle pas se guérir? Serais-tu pour moi comme une source trompeuse, Comme une eau dont on n’est pas sûr?
Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Bwanji chilonda changa sichikupola? Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe, kapena ngati kasupe wopanda madzi?”
19 C’est pourquoi ainsi parle l’Éternel: Si tu te rattaches à moi, je te répondrai, et tu te tiendras devant moi; Si tu sépares ce qui est précieux de ce qui est vil, tu seras comme ma bouche. C’est à eux de revenir à toi, Mais ce n’est pas à toi de retourner vers eux.
Tsono Yehova anandiyankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso ndipo udzakhalanso mtumiki wanga. Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe, udzakhalanso mneneri wanga. Anthu adzabwera kwa iwe ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
20 Je te rendrai pour ce peuple comme une forte muraille d’airain; Ils te feront la guerre, mais ils ne te vaincront pas; Car je serai avec toi pour te sauver et te délivrer, Dit l’Éternel.
Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba ngati mkuwa kwa anthu awa. Adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, pakuti Ine ndili nawe kukulanditsa ndi kukupulumutsa,” akutero Yehova.
21 Je te délivrerai de la main des méchants, Je te sauverai de la main des violents.
“Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”

< Jérémie 15 >