< Ézéchiel 35 >
1 La parole de l’Éternel me fut adressée, en ces mots:
Yehova anandiyankhula kuti:
2 Fils de l’homme, tourne ta face vers la montagne de Séir, Et prophétise contre elle!
“Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo
3 Tu lui diras: Ainsi parle le Seigneur, l’Éternel: Voici, j’en veux à toi, montagne de Séir! J’étends ma main sur toi, Et je fais de toi une solitude et un désert.
awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu.
4 Je mettrai tes villes en ruines, Tu deviendras une solitude, Et tu sauras que je suis l’Éternel.
Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5 Parce que tu avais une haine éternelle, Parce que tu as précipité par le glaive les enfants d’Israël, Au jour de leur détresse, Au temps où l’iniquité était à son terme,
“Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake.
6 Je suis vivant! Dit le Seigneur, l’Éternel, Je te mettrai à sang, et le sang te poursuivra; Puisque tu n’as pas haï le sang, Le sang te poursuivra.
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola.
7 Je ferai de la montagne de Séir une solitude et un désert, Et j’en exterminerai les allants et les venants.
Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko.
8 Je remplirai de morts ses montagnes; Sur tes collines, dans tes vallées, dans tous tes ravins, Tomberont ceux qui seront frappés par l’épée.
Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse.
9 Je ferai de toi des solitudes éternelles, Tes villes ne seront plus habitées, Et vous saurez que je suis l’Éternel.
Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
10 Parce que tu as dit: Les deux nations, les deux pays seront à moi, Et nous en prendrons possession, Quand même l’Éternel était là,
“Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo.
11 Je suis vivant! Dit le Seigneur, l’Éternel, J’agirai avec la colère et la fureur Que tu as montrées, dans ta haine contre eux; Et je me ferai connaître au milieu d’eux, Quand je te jugerai.
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo.
12 Tu sauras que moi, l’Éternel, J’ai entendu tous les outrages Que tu as proférés contre les montagnes d’Israël, En disant: Elles sont dévastées, Elles nous sont livrées comme une proie.
Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’
13 Vous vous êtes élevés contre moi par vos discours, Vous avez multiplié vos paroles contre moi: J’ai entendu.
Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva.
14 Ainsi parle le Seigneur, l’Éternel: Lorsque tout le pays sera dans la joie, Je ferai de toi une solitude.
Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja.
15 A cause de la joie que tu as éprouvée Parce que l’héritage de la maison d’Israël était dévasté, Je te traiterai de la même manière; Tu deviendras une solitude, montagne de Séir, Toi, et Édom tout entier. Et ils sauront que je suis l’Éternel.
Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”