< Amos 7 >
1 Le Seigneur, l’Éternel, m’envoya cette vision. Voici, il formait des sauterelles, Au moment où le regain commençait à croître; C’était le regain après la coupe du roi.
Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene.
2 Et comme elles dévoraient entièrement l’herbe de la terre, Je dis: Seigneur Éternel, pardonne donc! Comment Jacob subsistera-t-il? Car il est si faible!
Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
3 L’Éternel se repentit de cela. Cela n’arrivera pas, dit l’Éternel.
Kotero Yehova anakhululuka. Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”
4 Le Seigneur, l’Éternel, m’envoya cette vision. Voici, le Seigneur, l’Éternel, proclamait le châtiment par le feu; Et le feu dévorait le grand abîme Et dévorait le champ.
Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko.
5 Je dis: Seigneur Éternel, arrête donc! Comment Jacob subsistera-t-il? Car il est si faible!
Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
6 L’Éternel se repentit de cela. Cela non plus n’arrivera pas, dit le Seigneur, l’Éternel.
Kotero Yehova anakhululuka. Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”
7 Il m’envoya cette vision. Voici, le Seigneur se tenait sur un mur tiré au cordeau, Et il avait un niveau dans la main.
Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma.
8 L’Éternel me dit: Que vois-tu, Amos? Je répondis: Un niveau. Et le Seigneur dit: Je mettrai le niveau au milieu de mon peuple d’Israël, Je ne lui pardonnerai plus;
Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?” Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.” Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.
9 Les hauts lieux d’Isaac seront ravagés; Les sanctuaires d’Israël seront détruits, Et je me lèverai contre la maison de Jéroboam avec l’épée.
“Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja; ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”
10 Alors Amatsia, prêtre de Béthel, fit dire à Jéroboam, roi d’Israël: Amos conspire contre toi au milieu de la maison d’Israël; le pays ne peut supporter toutes ses paroles.
Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo.
11 Car voici ce que dit Amos: Jéroboam mourra par l’épée, et Israël sera emmené captif loin de son pays.
Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi: “‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’”
12 Et Amatsia dit à Amos: Homme à visions, va-t-en, fuis dans le pays de Juda; manges-y ton pain, et là tu prophétiseras.
Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa.
13 Mais ne continue pas à prophétiser à Béthel, car c’est un sanctuaire du roi, et c’est une maison royale.
Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”
14 Amos répondit à Amatsia: Je ne suis ni prophète, ni fils de prophète; mais je suis berger, et je cultive des sycomores.
Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu.
15 L’Éternel m’a pris derrière le troupeau, et l’Éternel m’a dit: Va, prophétise à mon peuple d’Israël.
Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’
16 Écoute maintenant la parole de l’Éternel, toi qui dis: Ne prophétise pas contre Israël, et ne parle pas contre la maison d’Isaac.
Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti, “‘Usanenere zotsutsa Israeli, ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’”
17 A cause de cela, voici ce que dit l’Éternel: Ta femme se prostituera dans la ville, tes fils et tes filles tomberont par l’épée, ton champ sera partagé au cordeau; et toi, tu mourras sur une terre impure, et Israël sera emmené captif loin de son pays.
“Tsono zimene akunena Yehova ndi izi: “‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu, ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa, ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu. Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’”