< Actes 21 >

1 Nous nous embarquâmes, après nous être séparés d’eux, et nous allâmes directement à Cos, le lendemain à Rhodes, et de là à Patara.
Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara.
2 Et ayant trouvé un navire qui faisait la traversée vers la Phénicie, nous montâmes et partîmes.
Kumeneko tinapeza sitima yapamadzi yopita ku Foinike. Choncho tinalowamo nʼkunyamuka.
3 Quand nous fûmes en vue de l’île de Chypre, nous la laissâmes à gauche, poursuivant notre route du côté de la Syrie, et nous abordâmes à Tyr, où le bâtiment devait décharger sa cargaison.
Tinaona chilumba cha Kupro ndipo tinadutsa kummwera kwake nʼkupita ku Siriya. Tinakayima ku Turo chifukwa sitima yathuyo imayenera kusiya katundu kumeneko.
4 Nous trouvâmes les disciples, et nous restâmes là sept jours. Les disciples, poussés par l’Esprit, disaient à Paul de ne pas monter à Jérusalem.
Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.
5 Mais, lorsque nous fûmes au terme des sept jours, nous nous acheminâmes pour partir, et tous nous accompagnèrent avec leurs femmes et leurs enfants jusque hors de la ville. Nous nous mîmes à genoux sur le rivage, et nous priâmes.
Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera.
6 Puis, ayant pris congé les uns des autres, nous montâmes sur le navire, et ils retournèrent chez eux.
Titatsanzikana, tinalowa mʼsitima ija, iwowo anabwerera ku nyumba zawo.
7 Achevant notre navigation, nous allâmes de Tyr à Ptolémaïs, où nous saluâmes les frères, et passâmes un jour avec eux.
Ife tinapitiriza ulendo wathu wochokera ku Turo mpaka tinafika ku Ptolemayi. Kumeneko tinalonjera abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi.
8 Nous partîmes le lendemain, et nous arrivâmes à Césarée. Étant entrés dans la maison de Philippe l’évangéliste, qui était l’un des sept, nous logeâmes chez lui.
Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja.
9 Il avait quatre filles vierges qui prophétisaient.
Iye anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene anali ndi mphatso ya uneneri.
10 Comme nous étions là depuis plusieurs jours, un prophète, nommé Agabus, descendit de Judée,
Titakhala kumeneko masiku ambiri, kunabwera mneneri wina wochokera ku Yudeya dzina lake Agabu.
11 et vint nous trouver. Il prit la ceinture de Paul, se lia les pieds et les mains, et dit: Voici ce que déclare le Saint-Esprit: L’homme à qui appartient cette ceinture, les Juifs le lieront de la même manière à Jérusalem, et le livreront entre les mains des païens.
Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’”
12 Quand nous entendîmes cela, nous et ceux de l’endroit, nous priâmes Paul de ne pas monter à Jérusalem.
Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu kumeneko tinamudandaulira Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.
13 Alors il répondit: Que faites-vous, en pleurant et en me brisant le cœur? Je suis prêt, non seulement à être lié, mais encore à mourir à Jérusalem pour le nom du Seigneur Jésus.
Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”
14 Comme il ne se laissait pas persuader, nous n’insistâmes pas, et nous dîmes: Que la volonté du Seigneur se fasse!
Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”
15 Après ces jours-là, nous fîmes nos préparatifs, et nous montâmes à Jérusalem.
Pambuyo pake, ife tinakonzeka ndi kunyamuka kumapita ku Yerusalemu.
16 Quelques disciples de Césarée vinrent aussi avec nous, et nous conduisirent chez un nommé Mnason, de l’île de Chypre, ancien disciple, chez qui nous devions loger.
Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.
17 Lorsque nous arrivâmes à Jérusalem, les frères nous reçurent avec joie.
Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mwachimwemwe.
18 Le lendemain, Paul se rendit avec nous chez Jacques, et tous les anciens s’y réunirent.
Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko.
19 Après les avoir salués, il raconta en détail ce que Dieu avait fait au milieu des païens par son ministère.
Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.
20 Quand ils l’eurent entendu, ils glorifièrent Dieu. Puis ils lui dirent: Tu vois, frère, combien de milliers de Juifs ont cru, et tous sont zélés pour la loi.
Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose.
21 Or, ils ont appris que tu enseignes à tous les Juifs qui sont parmi les païens à renoncer à Moïse, leur disant de ne pas circoncire les enfants et de ne pas se conformer aux coutumes.
Iwo anawuzidwa kuti iwe umaphunzitsa Ayuda onse amene akukhala pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Mose, kuti asamachite mdulidwe kapena kutsatira miyambo.
22 Que faire donc? Sans aucun doute la multitude se rassemblera, car on saura que tu es venu.
Nanga pamenepa ife titani? Iwo adzamva ndithu kuti iwe wabwera,
23 C’est pourquoi fais ce que nous allons te dire. Il y a parmi nous quatre hommes qui ont fait un vœu;
tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu.
24 prends-les avec toi, purifie-toi avec eux, et pourvois à leur dépense, afin qu’ils se rasent la tête. Et ainsi tous sauront que ce qu’ils ont entendu dire sur ton compte est faux, mais que toi aussi tu te conduis en observateur de la loi.
Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo.
25 A l’égard des païens qui ont cru, nous avons décidé et nous leur avons écrit qu’ils eussent à s’abstenir des viandes sacrifiées aux idoles, du sang, des animaux étouffés, et de l’impudicité.
Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”
26 Alors Paul prit ces hommes, se purifia, et entra le lendemain dans le temple avec eux, pour annoncer à quel jour la purification serait accomplie et l’offrande présentée pour chacun d’eux.
Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.
27 Sur la fin des sept jours, les Juifs d’Asie, ayant vu Paul dans le temple, soulevèrent toute la foule, et mirent la main sur lui,
Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo,
28 en criant: Hommes Israélites, au secours! Voici l’homme qui prêche partout et à tout le monde contre le peuple, contre la loi et contre ce lieu; il a même introduit des Grecs dans le temple, et a profané ce saint lieu.
akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.”
29 Car ils avaient vu auparavant Trophime d’Éphèse avec lui dans la ville, et ils croyaient que Paul l’avait fait entrer dans le temple.
Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.
30 Toute la ville fut émue, et le peuple accourut de toutes parts. Ils se saisirent de Paul, et le traînèrent hors du temple, dont les portes furent aussitôt fermées.
Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata.
31 Comme ils cherchaient à le tuer, le bruit vint au tribun de la cohorte que tout Jérusalem était en confusion.
Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka.
32 A l’instant il prit des soldats et des centeniers, et courut à eux. Voyant le tribun et les soldats, ils cessèrent de frapper Paul.
Nthawi yomweyo iye anatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali ndi kuthamangira kumene kunali anthuwo. Anthuwo ataona mkuluyo ndi asilikali ake analeka kumenya Paulo.
33 Alors le tribun s’approcha, se saisit de lui, et le fit lier de deux chaînes. Puis il demanda qui il était, et ce qu’il avait fait.
Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani.
34 Mais dans la foule les uns criaient d’une manière, les autres d’une autre; ne pouvant donc rien apprendre de certain, à cause du tumulte, il ordonna de le mener dans la forteresse.
Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali.
35 Lorsque Paul fut sur les degrés, il dut être porté par les soldats, à cause de la violence de la foule;
Paulo atafika pa makwerero olowera ku malo a asilikaliwo, ananyamulidwa ndi asilikali chifukwa cha ukali wa anthuwo.
36 car la multitude du peuple suivait, en criant: Fais-le mourir!
Gulu la anthu limene linamutsatira linapitiriza kufuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi!”
37 Au moment d’être introduit dans la forteresse, Paul dit au tribun: M’est-il permis de te dire quelque chose? Le tribun répondit: Tu sais le grec?
Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?” Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki?
38 Tu n’es donc pas cet Égyptien qui s’est révolté dernièrement, et qui a emmené dans le désert quatre mille brigands?
Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”
39 Je suis Juif, reprit Paul, de Tarse en Cilicie, citoyen d’une ville qui n’est pas sans importance. Permets-moi, je te prie, de parler au peuple.
Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”
40 Le tribun le lui ayant permis, Paul, debout sur les degrés, fit signe de la main au peuple. Un profond silence s’établit, et Paul, parlant en langue hébraïque, dit:
Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri.

< Actes 21 >