< 1 Samuel 12 >

1 Samuel dit à tout Israël: Voici, j’ai écouté votre voix dans tout ce que vous m’avez dit, et j’ai établi un roi sur vous.
Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani.
2 Et maintenant, voici le roi qui marchera devant vous. Pour moi, je suis vieux, j’ai blanchi, et mes fils sont avec vous; j’ai marché à votre tête, depuis ma jeunesse jusqu’à ce jour.
Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero.
3 Me voici! Rendez témoignage contre moi, en présence de l’Éternel et en présence de son oint. De qui ai-je pris le bœuf et de qui ai-je pris l’âne? Qui ai-je opprimé, et qui ai-je traité durement? De qui ai-je reçu un présent, pour fermer les yeux sur lui? Je vous le rendrai.
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”
4 Ils répondirent: Tu ne nous as point opprimés, et tu ne nous as point traités durement, et tu n’as rien reçu de la main de personne.
Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”
5 Il leur dit encore: L’Éternel est témoin contre vous, et son oint est témoin, en ce jour, que vous n’avez rien trouvé dans mes mains. Et ils répondirent: Ils en sont témoins.
Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.”
6 Alors Samuel dit au peuple: C’est l’Éternel qui a établi Moïse et Aaron, et qui a fait monter vos pères du pays d’Égypte.
Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto.
7 Maintenant, présentez-vous, et je vous jugerai devant l’Éternel sur tous les bienfaits que l’Éternel vous a accordés, à vous et à vos pères.
Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu.
8 Après que Jacob fut venu en Égypte, vos pères crièrent à l’Éternel, et l’Éternel envoya Moïse et Aaron, qui firent sortir vos pères d’Égypte et les firent habiter dans ce lieu.
“Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.
9 Mais ils oublièrent l’Éternel, leur Dieu; et il les vendit entre les mains de Sisera, chef de l’armée de Hatsor, entre les mains des Philistins, et entre les mains du roi de Moab, qui leur firent la guerre.
“Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu.
10 Ils crièrent encore à l’Éternel, et dirent: Nous avons péché, car nous avons abandonné l’Éternel, et nous avons servi les Baals et les Astartés; délivre-nous maintenant de la main de nos ennemis, et nous te servirons.
Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’
11 Et l’Éternel envoya Jerubbaal, Bedan, Jephthé et Samuel, et il vous délivra de la main de vos ennemis qui vous entouraient, et vous demeurâtes en sécurité.
Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere.
12 Puis, voyant que Nachasch, roi des fils d’Ammon, marchait contre vous, vous m’avez dit: Non! Mais un roi régnera sur nous. Et cependant l’Éternel, votre Dieu, était votre roi.
“Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu.
13 Voici donc le roi que vous avez choisi, que vous avez demandé; voici, l’Éternel a mis sur vous un roi.
Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu.
14 Si vous craignez l’Éternel, si vous le servez, si vous obéissez à sa voix, et si vous n’êtes point rebelles à la parole de l’Éternel, vous vous attacherez à l’Éternel, votre Dieu, vous et le roi qui règne sur vous.
Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.
15 Mais si vous n’obéissez pas à la voix de l’Éternel, et si vous êtes rebelles à la parole de l’Éternel, la main de l’Éternel sera contre vous, comme elle a été contre vos pères.
Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe.
16 Attendez encore ici, et voyez le prodige que l’Éternel va opérer sous vos yeux.
“Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu!
17 Ne sommes-nous pas à la moisson des blés? J’invoquerai l’Éternel, et il enverra du tonnerre et de la pluie. Sachez alors et voyez combien vous avez eu tort aux yeux de l’Éternel de demander pour vous un roi.
Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”
18 Samuel invoqua l’Éternel, et l’Éternel envoya ce même jour du tonnerre et de la pluie. Tout le peuple eut une grande crainte de l’Éternel et de Samuel.
Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.
19 Et tout le peuple dit à Samuel: Prie l’Éternel, ton Dieu, pour tes serviteurs, afin que nous ne mourions pas; car nous avons ajouté à tous nos péchés le tort de demander pour nous un roi.
Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.”
20 Samuel dit au peuple: N’ayez point de crainte! Vous avez fait tout ce mal; mais ne vous détournez pas de l’Éternel, et servez l’Éternel de tout votre cœur.
Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse.
21 Ne vous en détournez pas; sinon, vous iriez après des choses de néant, qui n’apportent ni profit ni délivrance, parce que ce sont des choses de néant.
Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe.
22 L’Éternel n’abandonnera point son peuple, à cause de son grand nom, car l’Éternel a résolu de faire de vous son peuple.
Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake.
23 Loin de moi aussi de pécher contre l’Éternel, de cesser de prier pour vous! Je vous enseignerai le bon et le droit chemin.
Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo.
24 Craignez seulement l’Éternel, et servez-le fidèlement de tout votre cœur; car voyez quelle puissance il déploie parmi vous.
Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani.
25 Mais si vous faites le mal, vous périrez, vous et votre roi.
Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.”

< 1 Samuel 12 >