< Lévitique 16 >

1 Après que les deux fils d'Aaron eurent expiré pendant qu'ils offraient au Seigneur un feu étranger, le Seigneur parla à Moïse,
Atafa ana awiri a Aaroni amene anaphedwa atapita pamaso pa Yehova mosayenera, Yehova anayankhula ndi Mose.
2 Et lui dit: Fais savoir à Aaron ton frère qu'il ne doit point entrer à toute heure dans le Saint des saints, à l'intérieur du voile du sanctuaire, devant le propitiatoire qui est sur l'arche du témoignage, afin qu'il ne meure pas; car j'apparaîtrai dans une nuée au-dessus du propitiatoire.
Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.
3 Aaron entrera dans le sanctuaire de la manière suivante: il amènera un veau, pris parmi les bœufs, pour le péché, et un bélier pour l'holocauste;
“Aaroni azilowa Malo Wopatulika Kwambiri motere: azitenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza.
4 Il revêtira la tunique de lin sanctifiée, il aura sur la chair un caleçon de lin, il ceindra une ceinture de lin, et il posera sur sa tête une tiare aussi de lin; ce sont les vêtements saints dont il se revêtira après s'être lavé tout le corps avec de l'eau.
Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi.
5 Et il se fera donner, par la synagogue des fils d'Israël, deux jeunes boucs, pris parmi les chèvres, pour le péché, et un bélier pour l'holocauste.
Kuchokera pa gulu la Aisraeli, Aaroni azitenga mbuzi zazimuna ziwiri kuti zikhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza.
6 Aaron fera, pour son propre péché, l'offrande du veau, et il priera pour lui-même et pour toute sa maison.
“Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale yopepesera machimo a iye mwini kuti achite mwambo wopepesera machimo ake pamodzi ndi a banja lake.
7 Puis, il prendra les deux boucs et les placera en présence du Seigneur, devant la porte du tabernacle du témoignage.
Kenaka atenge mbuzi ziwiri zija ndipo aziyimike pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
8 Et Aaron jettera sur les deux boucs deux sorts: un sort pour le bouc du Seigneur, un sort pour le bouc émissaire.
Aaroni ndiye achite maere pa mbuzi ziwirizo kuti imodzi ikhale ya Yehova, ndipo inayo ikhale ya Azazele.
9 Ensuite, Aaron amènera le bouc que le sort aura désigné pour le Seigneur, et il l'offrira pour le péché.
Aaroni abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Yehova, ndipo apereke kuti ikhale nsembe yopereka chifukwa cha tchimo.
10 Quant au bouc sur qui sera tombé le sort de l'émissaire, il le placera vivant devant le Seigneur, pour prier sur lui et le chasser comme émissaire, et il l'enverra dans le désert.
Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele.
11 Après cela, Aaron fera approcher le veau offert pour son propre péché, il priera pour lui-même et pour sa maison, et il égorgera le veau pour son péché.
“Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja.
12 Il prendra aussi l'encensoir, garni de charbons du feu de l'autel placé devant le Seigneur, il remplira ses mains de l'encens habilement composé, et il le portera au delà du voile intérieur.
Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani.
13 Et il mettra l'encens sur le feu devant le Seigneur, et la vapeur de l'encens enveloppera le propitiatoire qui est sur l'arche du témoignage; ainsi Aaron ne mourra pas.
Athire lubani pa moto pamaso pa Yehova kuti utsi wa lubaniyo uphimbe chivundikiro chimene chili pamwamba pa Bokosi la Chipangano, kuti Aaroniyo asafe.
14 Il prendra du sang du veau, et il aspergera du doigt le propitiatoire du côté de l'orient; il fera ainsi avec le doigt sept aspersions de sang devant le propitiatoire.
Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.
15 Puis, il égorgera le bouc pour le péché, celui qui est pour le peuple devant le Seigneur; il portera de son sang à l'intérieur du voile, et en fera, comme avec le sang du veau, des aspersions devant le propitiatoire.
“Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho.
16 Et il purifiera le saint de toutes les impuretés des fils d'Israël, de tous leurs péchés et iniquités. Ainsi fera-t-il pour le tabernacle du témoignage, élevé parmi eux, au milieu de leur impureté.
Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika chifukwa cha kudetsedwa ndi kuwukira kwa Aisraeli pa machimo ena aliwonse amene achita. Achite chimodzimodzi ndi tenti ya msonkhano imenenso ili yodetsedwa chifukwa cha machimo awo.
17 Nul homme ne demeurera dans le tabernacle du témoignage, à partir du moment où il y sera entré pour prier dans le saint, jusqu'à ce qu'il en sorte. Et il priera pour lui et pour sa maison, et pour toute la synagogue des fils d'Israël.
Mu tenti ya msonkhano musakhale munthu ndi mmodzi yemwe nthawi imene Aaroni akupita kukachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika mpaka atatulukako. Musakhale munthu mu tenti ya msonkhano mpaka atachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake, banja lake ndi gulu lonse la Aisraeli.
18 Ensuite, il reviendra vers l'autel qui est devant le Seigneur, il priera sur lui, et il prendra du sang du veau et du bouc, et il en mettra sur les cornes de l'autel, tout autour.
“Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe.
19 Puis, il fera du doigt sept aspersions de sang sur l'autel, et il purifiera l'autel des impuretés du peuple et le sanctifiera.
Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli.
20 Il achèvera ainsi la purification du sanctuaire du tabernacle du témoignage et de l'autel, et celle des prêtres; après cela, il fera approcher le bouc vivant.
“Aaroni akatsiriza mwambo wopepesera Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa, azibwera ndi mbuzi yamoyo kudzayipereka nsembe.
21 Aaron imposera les mains sur sa tête, il confessera sur lui tous les dérèglements des fils d'Israël, toutes leurs iniquités, tous leurs péchés; il les mettra sur la tête du bouc vivant, et il le chassera, à l'aide d'un homme préparé pour cette fin, jusque dans le désert;
Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu.
22 Et le bouc emportera sur lui dans la terre sans chemins tous les péchés d'Israël. Aaron chassera le bouc dans le désert;
Mbuziyo isenze machimo awo onse ndi kupita nawo kutali ndipo munthuyo aleke mbuziyo kuti ipite ku chipululuko.
23 Après quoi, il entrera dans le tabernacle du témoignage, il ôtera la robe de lin qu'il aura revêtue pour entrer dans le sanctuaire, et il l'y déposera.
“Pambuyo pake Aaroni alowe mu tenti ya msonkhano ndi kuvula zovala zosalala zija zimene anavala polowa ku Malo Wopatulika ndi kuzisiya komweko.
24 Il lavera son corps avec de l'eau en lieu saint; il revêtira sa robe, puis étant sorti, il brûlera son holocauste et celui du peuple, et il priera pour lui-même et pour sa maison, pour le peuple et pour les prêtres.
Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu.
25 Il portera sur l'autel la graisse des victimes pour le péché.
Mafuta a nyama yopepesera machimo awatenthe pa guwa lansembe.
26 L'homme qui aura emmené le bouc émissaire lavera aussi ses vêtements et son corps avec de l'eau, et il rentrera dans le camp.
“Tsono munthu amene anaperekeza mbuzi yosenza machimo ija achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe ku msasa.
27 Quant au veau et au bouc qui sont pour le péché et dont le sang a été introduit pour intercéder dans le sanctuaire, on les portera hors du camp et on les consumera par le feu avec leurs peaux, leurs chairs et leur fiente.
Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe.
28 Celui qui les aura brûlés lavera ses vêtements et son corps avec de l'eau, et il rentrera dans le camp.
Munthu amene azitenthe achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe mu msasa.
29 Voici encore pour vous une loi perpétuelle: dans la septième lune, le dixième jour de la lune, vous humilierez vos âmes; vous ne ferez aucune œuvre, ni l'indigène, ni le prosélyte venu parmi vous.
“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu,
30 Car, en ce jour-là, on priera pour vous afin de vous purifier de tous vos péchés, devant le Seigneur, et vous serez purifiés.
chifukwa tsiku limeneli kudzachitika mwambo wopepesera machimo anu, kukuyeretsani kuti mukhale oyeretsedwa ku machimo anu pamaso pa Yehova.
31 Ce repos sera le sabbat du sabbat pour vous, et vous humilierez vos âmes: c'est une loi perpétuelle.
Limeneli ndi tsiku lanu la Sabata lopumula, ndipo muzigonja pamaso pa Yehova. Limeneli ndi lamulo lanu la muyaya.
32 Le prêtre qui aura reçu l'onction, et dont les mains auront été consacrées pour exercer le sacerdoce après son père, priera, et il revêtira la robe de lin, la robe sainte.
Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika.
33 Il purifiera le Saint des saints, le tabernacle du témoignage, l'autel, ainsi que les prêtres et toute la synagogue.
Adzachite mwambo wopepesera machimo Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Adzachitenso mwambo wopepesera anzake ndi gulu lonse la anthu.
34 Et ce sera pour vous une loi perpétuelle de purifier les fils d'Israël de tous leurs péchés une fois par an; on le fera comme le Seigneur l'a ordonné à Moïse.
“Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.” Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.

< Lévitique 16 >