< Juges 14 >

1 Et Samson descendit en Thamnatha, ou il vit une femme parmi les filles des Philistins.
Samsoni anapita ku Timna ndipo kumeneko anaonako mtsikana wa Chifilisiti.
2 Il s'en retourna, et il l'apprit à son père et à sa mère, et il dit: J'ai vu, en Thamnatha, une femme parmi les filles des Philistins; maintenant, prenez-la, et me la donnez pour femme.
Atabwerera kwawo, anawuza abambo ndi amayi ake kuti, “Ine ndaona mtsikana wa Chifilisiti ku Timna, tsono mukanditengere ameneyo kuti akhale mkazi wanga.”
3 Son père et sa mère lui répondirent: N'y a-t-il point de filles de tes frères? n'est-il point une seule femme parmi tout notre peuple, pour que tu ailles prendre femme chez des étrangers incirconcis? Et Samson dit à son père: Prends-la pour moi, parce qu'elle est à mes yeux celle qui me convient.
Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?” Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.”
4 Son père et sa mère ne savaient pas qu'il agissait par la volonté du Seigneur, et qu'il cherchait un sujet de vengeance contre les Philistins; car, en ce temps-là, les Philistins dominaient sur Israël.
(Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli).
5 Samson descendit donc avec son père et sa mère en Thamnatha, et il alla seul jusqu'à la vigne de Thamnatha, et voici venir à sa rencontre un jeune lion rugissant.
Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye.
6 L'Esprit du Seigneur s'élança sur Samson, qui broya le lionceau comme il eut broyé une jeune chèvre; or, il n'avait rien dans les mains, et il ne raconta ce qu'il avait fait ni à son père ni à sa mère.
Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo.
7 Ils reprirent leur route, et ils parlèrent à la femme; et, aux yeux de Samson, elle était celle qui lui convenait.
Kenaka Samsoni anapita kukakambirana ndi mkaziyo, ndipo anamukonda mtsikanayo.
8 Quelque temps après, il y alla de nouveau, afin de l'épouser, et il se détourna pour voir le cadavre du lion, et voilà qu'il y avait dans sa gueule un essaim d'abeilles et du miel.
Patapita nthawi, Samsoni anabwerera kukatenga mtsikana uja. Panjira anapatuka kukaona mkango unawupha uja, ndipo anangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake.
9 Il prit du miel dans ses mains, et il s'en alla en mangeant. Quand il eut rejoint son père et sa mère, il leur en donna, et ils en mangèrent; mais il ne dit point qu'il l'avait pris dans la gueule du lion.
Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa.
10 Son père descendit auprès de la femme; et là, Samson prépara un festin pour sept jours, parce qu'ainsi font les jeunes gens.
Tsopano Samsoni anapita ku nyumba kwa mtsikanayo. Ndipo kumeneko Samsoni anakonza phwando monga ankachitira anyamata.
11 Quand les gens le virent, ils invitèrent trente convives, et ceux-ci se tinrent auprès de lui.
Makolo a mkwatibwiyo atamuona, anasankha anyamata makumi atatu kuti akhale naye.
12 Et Samson leur dit: Je vous propose une énigme; si vous la devinez très-bien, pendant ces sept jours de festin, et si vous l'expliquez, je vous donnerai trente suaires et trente tuniques pour vous vêtir.
Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero.
13 Si vous ne pouvez me l'expliquer, vous me donnerez trente vêtements de lin et trente tuniques changeantes. Et ils répondirent: Propose ton énigme, que nous l'entendions.
Koma ngati simutha kundiwuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa zovala makumi atatu zabafuta ndi zina za tsiku la chikondwerero.” Iwo anamuyankha kuti, “Tiwuze mwambi wakowo tiwumve.”
14 Et il leur dit: L'aliment a été tiré du mangeur; la douceur de la force. Or, ils passèrent trois jours sans pouvoir expliquer l'énigme.
Iye anati, “Chakudya chinatuluka mu chinthu chodya chinzake; ndipo chozuna chinatuluka mu chinthu champhamvu.” Panapita masiku atatu anthuwo akulephera kumasulira mwambiwo.
15 Le quatrième jour, ils dirent à la femme de Samson: Trompe ton mari, et qu'il t'explique l'énigme; sinon nous te livrerons aux flammes, toi et la maison de ton père. Est-ce que vous nous avez invités pour nous extorquer nos biens?
Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?”
16 Alors, la femme de Samson pleura auprès de lui, et elle lui dit: Sans doute tu me hais; tu ne m'aimes point, puisque tu ne m'as pas expliqué l'énigme que tu as proposée aux enfants de mon peuple. Samson répondit: Si je ne l'ai expliqué ni a mon père ni a ma mère, te l'expliquerai-je à toi?
Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.” Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?”
17 Et elle pleura auprès de lui pendant le reste des sept jours que dura le festin; le septième jour, il lui expliqua l'énigme, parce qu'elle ne cessait de le troubler; et elle l'expliqua aux enfants de son peuple.
Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo.
18 Les hommes de la ville lui dirent donc le septième jour, avant le lever du soleil: Qu'y a-t-il de plus doux que le miel? Qu'y a-t-il de plus fort que le lion? Et Samson leur dit: Si vous n'aviez point labouré avec ma génisse, vous ne sauriez point mon énigme.
Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti, “Chozuna nʼchiyani choposa uchi? Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?” Samsoni anawawuza kuti, “Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono, simukanatha kumasulira mwambi wangawu.”
19 Aussitôt, l'Esprit du Seigneur s'élança sur lui; il alla en Ascalon, il y tua trente hommes, il prit leurs vêtements, et il donna leurs tuniques changeantes à ceux qui avaient expliqué l'énigme. Et Samson fut courroucé, et il revint à la maison de son père.
Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu.
20 Et la femme de Samson épousa l'un des amis qu'il aimait.
Ndipo mkazi wa Samsoniyo anamukwatitsa kwa amene anali mnzake womuperekeza pa ukwati paja.

< Juges 14 >