< Jérémie 20 >
1 Et Paschor, fils d'Emmer le prêtre, qui était établi intendant du temple du Seigneur, entendit Jérémie comme il prophétisait en ses discours.
Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi.
2 Et il le frappa, et il le jeta dans un cachot, à la porte haute d'une maison séparée dans le temple de Dieu.
Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova.
3 Puis Paschor fit sortir Jérémie du cachot, et Jérémie lui dit: Le Seigneur ne t'appelle plus Paschor, mais l'exilé.
Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse.
4 Car ainsi dit le Seigneur: Voilà que je vais faire emmener en exil toi et tes proches; et ceux-ci tomberont sous le glaive de leurs ennemis, et tes yeux le verront, et je livrerai toi et tout Juda au roi de Babylone, et il vous transportera au loin, et il vous frappera du glaive.
Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo.
5 Et je livrerai aux mains de ses ennemis toute la richesse de cette ville, tout le fruit de ses travaux, et tous les trésors des rois de Juda, pour les emporter à Babylone.
Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni.
6 Et toi et tous ceux qui résident en ta maison, vous irez en captivité, et tu mourras à Babylone, et tu y seras enseveli avec tes proches, à qui tu as prophétisé le mensonge.
Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’”
7 Vous m'avez trompé, Seigneur, et j'ai été séduit. Vous avez prévalu, car vous avez la force; je suis devenu pour eux un sujet de dérision, et chaque jour ils ne cessent de me railler.
Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi; Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana. Anthu akundinyoza tsiku lonse. Aliyense akundiseka kosalekeza.
8 Je rirai moi-même avec amertume de mon impuissance; j'appellerai sur moi la misère, parce que la parole du Seigneur m'est devenue un opprobre, et que je suis insulté tout le jour.
Nthawi iliyonse ndikamayankhula, ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka! Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
9 Et j'ai dit: Je ne prononcerai plus le nom du Seigneur, et je ne parlerai plus en son nom. Et j'ai dans mes os comme un feu ardent; tout mon corps est défaillant; je ne puis plus supporter
Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,” mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga, amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga. Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa, koma sindingathe kupirirabe.
10 De m'entendre outrager par tous ceux qui s'attroupent autour de moi. Conspirez, disent-ils, conspirons tous contre cet homme, nous qui étions ses amis; surveillez ses intentions, s'il peut être séduit, sur lui nous prévaudrons, et de lui nous tirerons vengeance.
Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.”
11 Mais le Seigneur est avec moi, comme un puissant homme de guerre. Aussi m'ont-ils persécuté, mais ils n'ont pu rien découvrir contre moi; et ils ont été grandement confondus, parce qu'ils n'avaient point prévu leur propre honte, qui ne sera plus jamais oubliée.
Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu. Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana. Manyazi awo sadzayiwalika konse.
12 Seigneur, qui jugez les choses justes; qui sondez les reins et les cœurs, puissé-je voir la vengeance que vous tirerez d'eux; car je vous ai expliqué ma cause.
Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu. Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
13 Chantez le Seigneur; louez-le parce qu'il a dérobé l'âme du pauvre aux mains des méchants.
Imbirani Yehova! Mutamandeni Yehova! Iye amapulumutsa wosauka mʼmanja mwa anthu oyipa.
14 Maudit soit le jour où j'ai été conçu; que le jour où ma mère m'a enfanté ne soit pas glorifié!
Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15 Maudit soit l'homme qui est venu annoncer à mon père une bonne nouvelle, en disant: Il t'est né un fils!
Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga ndi uthenga woti: “Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16 Que cet homme se réjouisse comme les villes que le Seigneur, sans pitié, a renversées dans sa colère; qu'il entende des clameurs le matin, et des cris de guerre à midi;
Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova anayiwononga mopanda chisoni. Amve mfuwu mmawa, phokoso la nkhondo masana.
17 Parce qu'il ne m'a point tué dans le sein de ma mère; car ma mère eût été mon sépulcre, et sa conception eût duré toujours.
Chifukwa sanandiphere mʼmimba, kuti amayi anga asanduke manda anga, mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18 Fallait-il que je sortisse de ses entrailles, pour ne voir que peines et douleurs, tandis que mes jours s'écoulent dans la honte?
Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni kuti moyo wanga ukhale wamanyazi wokhawokha?