< 1 Chroniques 14 >
1 Et Hiram, roi de Tyr, envoya à David des messagers, des maçons et des charpentiers, avec des bois de cèdre, pour lui bâtir une maison.
Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu.
2 Et David reconnut que le Seigneur l'avait préparé pour être roi d'Israël; car son royaume s'était élevé et agrandi pour le bien être du peuple d'Israël.
Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza kwambiri ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.
3 Et David prit encore des femmes à Jérusalem; elles lui enfantèrent des fils et des filles.
Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri.
4 Voici les noms de ceux qui naquirent à Jérusalem: Samaa, Sobab, Nathan, Salomon,
Mayina a ana amene anaberekera ku Yerusalemu anali awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni,
5 Baar (Ebeher), Elisa (Elisua), Eliphaleth,
Ibihari, Elisua, Elipeleti,
6 Nageth (Naged), Naphath (Naphec), Japhia,
Noga, Nefegi, Yafiya,
7 Elisama, Eliada et Eliphalat.
Elisama, Beeliada ndi Elifeleti.
8 Cependant, les Philistins apprirent que David avait été sacré roi de tout Israël; et ils se mirent tous en campagne pour l'attaquer; mais lui, l'ayant su, sortit à leur rencontre.
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo.
9 Et ils s'avancèrent, et ils s'entassèrent dans le val des Géants.
Ndipo Afilisti anabwera ndi kulanda zinthu mʼChigwa cha Refaimu.
10 Et David consulta Dieu, disant: Dois-je marcher contre les Philistins? me les livrerez-vous? Et le Seigneur lui répondit: Marche, car je te les livrerai.
Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.”
11 Et il alla à Baal-Pharasin, où il les battit, et il s'écria: Dieu, par mes mains, a brisé mes ennemis comme brisent les eaux des torrents. A cause de cela, il donna à ce lieu le nom de Brisement d'en haut.
Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu.
12 Or, les Philistins avaient abandonné là leurs dieux, et David dit: Livrez-les aux flammes.
Afilisti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide analamulira kuti itenthedwe ndi moto.
13 Et les Philistins continuèrent la guerre, et ils se réunirent encore dans le val des Géants.
Nthawi inanso Afilisti anadzalanda katundu mu Chigwamo.
14 Et David consulta derechef le Seigneur, et le Seigneur lui dit: Ne les suis pas, fais un détour, et tu les aborderas près des poiriers.
Choncho Davide anafunsa Mulungu ndipo Mulunguyo anayankha kuti, “Usapite molunjika, koma uzungulire kumbuyo kwawo. Ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku.
15 Et ceci arrivera: Lorsque tu entendras, de la colline des Poiriers, le bruit sourd de l'ébranlement qu'ils donneront au sol, tu engageras la bataille; car alors le Seigneur marchera devant toi pour frapper le camp des Philistins.
Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukapite kukamenyana nawo, chifukwa izi zikasonyeza kuti Mulungu ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.”
16 David fit ce que lui avait prescrit le Seigneur, et il tailla en pièces les Philistins, depuis Gabaon jusqu'à Gazara.
Kotero Davide anachita zimene Mulungu anamulamulira ndipo anakantha ankhondo a Afilisti njira yonse kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.
17 Et le nom de David se répandit sur toute la terre, et le Seigneur inspira à tous les peuples la crainte de David.
Choncho mbiri ya Davide inafalikira dziko lonse, ndipo Yehova anachititsa kuti mayiko ena azimuopa.