< Jérémie 42 >
1 Et tous les chefs des forces, et Jokhanan, fils de Karéakh, et Jezania, fils de Hoshahia, et tout le peuple, depuis le petit jusqu’au grand, s’approchèrent
Atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya ndi Azariya mwana wa Hosayia, ndiponso anthu onse, ana ndi akuluakulu omwe, anapita
2 et dirent à Jérémie le prophète: Que notre supplication soit reçue devant toi, et prie l’Éternel, ton Dieu, pour nous, pour tout ce reste; car, de beaucoup [que nous étions], nous sommes restés peu, selon que tes yeux nous voient;
kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala.
3 et que l’Éternel, ton Dieu, nous montre le chemin par lequel nous devons marcher, et ce que nous devons faire.
Mupemphere kuti Yehova Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi chimene tiyenera kuchita.”
4 Et Jérémie le prophète, leur dit: J’ai entendu; voici, je prierai l’Éternel, votre Dieu, selon vos paroles; et il arrivera que, tout ce que l’Éternel vous répondra, je vous le déclarerai: je ne vous cacherai rien.
Mneneri Yeremiya anawayankha kuti, “Ndamva zimene mwanenazi. Ndithu ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga momwe mwandipemphera. Ndidzakuwuzani chilichonse chimene Yehova anene ndipo sindidzakubisirani kanthu kalikonse.”
5 Et ils dirent à Jérémie: L’Éternel soit entre nous un témoin véritable et fidèle, si nous ne faisons selon toute la parole pour laquelle l’Éternel, ton Dieu, t’enverra vers nous!
Ndipo iwo anawuza Yeremiya kuti, “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ife ngati sitichita mogwirizana ndi chilichonse chimene Yehova Mulungu adzakutumani kuti mutiwuze.
6 Soit bien, soit mal, nous écouterons la voix de l’Éternel notre Dieu, vers qui nous t’envoyons, afin qu’il nous arrive du bien, quand nous écouterons la voix de l’Éternel, notre Dieu.
Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.”
7 Et il arriva, au bout de dix jours, que la parole de l’Éternel vint à Jérémie.
Patapita masiku khumi, Yehova anayankhula ndi Yeremiya.
8 Et il appela Jokhanan, fils de Karéakh, et tous les chefs des forces qui étaient avec lui, et tout le peuple, depuis le petit jusqu’au grand,
Choncho Yeremiya anayitana Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye ndiponso anthu onse, ana ndi akulu omwe.
9 et leur dit: Ainsi dit l’Éternel, le Dieu d’Israël, vers qui vous m’avez envoyé pour présenter votre supplication devant lui:
Yehova, Mulungu wa Israeli amene munanditumako kuti ndikapereke madandawulo mʼdzina lanu akuti,
10 Si vous continuez à habiter dans ce pays, je vous bâtirai, et je ne vous renverserai pas, et je vous planterai, et je ne vous arracherai pas; car je me repens du mal que je vous ai fait.
“Ngati mukhala mʼdziko muno, ndiye kuti ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani. Inde ndidzakudzalani osakuchotsani pakuti ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha mavuto amene ndabweretsa pa inu.
11 Ne craignez point le roi de Babylone, dont vous avez peur; ne le craignez pas, dit l’Éternel; car je suis avec vous pour vous sauver et pour vous délivrer de sa main;
Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake.
12 et j’userai de miséricorde envers vous, et il aura pitié de vous, et vous fera retourner dans votre terre.
Ndidzakuchitirani chifundo, ndipo mfumuyonso idzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale mʼdziko mwanumwanu.
13 Mais si vous dites: Nous n’habiterons pas dans ce pays, et que vous n’écoutiez pas la voix de l’Éternel, votre Dieu,
“Koma mwina simudzamvera Yehova Mulungu wanu nʼkumanena kuti, ‘Ayi ife sitidzakhala mʼdziko muno,
14 disant: Non, mais nous irons dans le pays d’Égypte, où nous ne verrons pas la guerre, et où nous n’entendrons pas le son de la trompette, et où nous n’aurons pas disette de pain; et nous habiterons là; …
ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’
15 et maintenant, à cause de cela, écoutez la parole de l’Éternel, vous, le reste de Juda: Ainsi dit l’Éternel des armées, le Dieu d’Israël: Si vous tournez vos faces pour aller en Égypte, et que vous y alliez pour y demeurer,
Tsono, inu otsala a ku Yuda, imvani mawu a Yehova. Iye akuti, ngati mutsimikiza zopita ku Igupto, nʼkupitadi kukakhala kumeneko,
16 il arrivera que l’épée dont vous avez peur vous atteindra là, dans le pays d’Égypte, et la famine que vous craignez vous suivra de près, là, en Égypte, et vous y mourrez.
ndiye nkhondo imene mukuyiopayo idzakugonjetsani ku Igupto komweko. Njala imene mukuyiopayo idzakupezani ku Igupto komweko ndipo mudzafera kumeneko.
17 Et il arrivera que tous les hommes qui auront tourné leur face pour aller en Égypte afin d’y séjourner, mourront par l’épée, par la famine, et par la peste; et il n’y aura pour eux ni reste ni réchappé de devant le mal que je fais venir sur eux.
Kunena zoona, onse amene atsimikiza zopita ku Igupto kuti akakhale kumeneko adzafa ndi nkhondo njala ndi mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumuke kapena kuthawa mavuto amene ndidzawagwetsera.’
18 Car ainsi dit l’Éternel des armées, le Dieu d’Israël: Comme ma colère et ma fureur ont été versées sur les habitants de Jérusalem, ainsi ma fureur sera versée sur vous si vous allez en Égypte; et vous serez une exécration, et une désolation, et une malédiction, et un opprobre; et vous ne verrez plus ce lieu.
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’
19 L’Éternel vous a dit, reste de Juda: N’allez pas en Égypte. Sachez certainement que je vous ai avertis aujourd’hui;
“Inu otsala a ku Yuda, Yehova wakuwuzani kuti, ‘Musapite ku Igupto.’ Dziwani chinthu ichi: Ine lero ndikukuchenjezani
20 car vous vous êtes séduits vous-mêmes dans vos âmes quand vous m’avez envoyé vers l’Éternel, votre Dieu, disant: Prie l’Éternel, notre Dieu, pour nous, et selon tout ce que l’Éternel, notre Dieu, dira, ainsi déclare-nous, et nous le ferons.
kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’
21 Et je vous l’ai déclaré aujourd’hui; et vous n’avez pas écouté la voix de l’Éternel, votre Dieu, ni tout ce avec quoi il m’a envoyé vers vous.
Ine lero ndakuwuzani, koma inu simukumverabe zonse zimene Yehova Mulungu anandituma kuti ndikuwuzeni.
22 Et maintenant, sachez certainement que vous mourrez par l’épée, par la famine, et par la peste, dans le lieu où vous avez désiré d’aller pour y séjourner.
Tsono dziwani ichi: mudzafadi ndi nkhondo, njala ndi mliri kumalo kumene mukufuna mukakhaleko.”