< Jérémie 39 >
1 qu’en la neuvième année de Sédécias, roi de Juda, au dixième mois, Nebucadretsar, roi de Babylone, vint, et toute son armée, contre Jérusalem, et ils l’assiégèrent.
Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo.
2 En la onzième année de Sédécias, au quatrième mois, le neuvième [jour] du mois, la brèche fut faite à la ville.
Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa.
3 Et tous les princes du roi de Babylone entrèrent, et s’assirent dans la porte intérieure: Nergal-Sharétser, Samgar-Nebu, Sarsekim, chef des eunuques, Nergal-Sharétser, chef des mages, et tout le reste des princes du roi de Babylone.
Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni.
4 Et il arriva que, quand Sédécias, roi de Juda, et tous les hommes de guerre les eurent vus, ils s’enfuirent, et sortirent de nuit de la ville, par le chemin du jardin du roi, par la porte qui était entre les deux murailles; et il sortit par le chemin de la plaine.
Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.
5 Et l’armée des Chaldéens les poursuivit, et ils atteignirent Sédécias dans les plaines de Jéricho, et ils le prirent, et le firent monter vers Nebucadnetsar, roi de Babylone, à Ribla, dans le pays de Hamath; et il prononça son jugement.
Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake.
6 Et le roi de Babylone égorgea les fils de Sédécias, à Ribla, devant ses yeux; et le roi de Babylone égorgea tous les nobles de Juda;
Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda.
7 et il creva les yeux à Sédécias, et le lia avec des chaînes d’airain, pour le mener à Babylone.
Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni.
8 Et les Chaldéens brûlèrent par le feu la maison du roi et les maisons du peuple, et ils abattirent les murailles de Jérusalem.
Ababuloni anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu, ndiponso anagwetsa malinga a Yerusalemu.
9 Et le reste du peuple qui était demeuré de reste dans la ville, et les transfuges qui étaient allés se rendre à lui, et le reste du peuple, ceux qui étaient de reste, Nebuzaradan, chef des gardes, les transporta à Babylone.
Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye.
10 Mais d’entre le peuple, Nebuzaradan, chef des gardes, laissa les pauvres, ceux qui n’avaient rien, dans le pays de Juda; et en ce jour-là il leur donna des vignes et des champs.
Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.
11 Et Nebucadretsar, roi de Babylone, avait commandé par Nebuzaradan, chef des gardes, touchant Jérémie, disant:
Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati:
12 Prends-le, et aie les yeux sur lui, et ne lui fais aucun mal; mais selon ce qu’il te dira, ainsi agis avec lui.
“Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.”
13 Et Nebuzaradan, chef des gardes, envoya, et Nebushazban, chef des eunuques, et Nergal-Sharétser, chef des mages, et tous les chefs du roi de Babylone,
Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni
14 envoyèrent, et prirent Jérémie de la cour de la prison, et le remirent à Guedalia, fils d’Akhikam, fils de Shaphan, pour le mener dehors, à la maison. Et il demeura au milieu du peuple.
anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake.
15 Et la parole de l’Éternel vint à Jérémie, pendant qu’il était enfermé dans la cour de la prison, disant:
Yeremiya ali mʼndende ku bwalo la alonda, Yehova anayankhula naye:
16 Va, et tu parleras à Ébed-Mélec, l’Éthiopien, disant: Ainsi dit l’Éternel des armées, le Dieu d’Israël: Voici, je fais venir mes paroles sur cette ville pour le mal, et non pour le bien; et elles auront lieu devant toi, en ce jour-là.
“Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona.
17 Et je te délivrerai en ce jour-là, dit l’Éternel, et tu ne seras point livré en la main des hommes dont tu as peur;
Koma ndidzakupulumutsa pa tsiku limenelo, akutero Yehova; sudzaperekedwa kwa anthu amene umawaopa.
18 car certainement je te sauverai, et tu ne tomberas pas par l’épée; et tu auras ta vie pour butin; car tu as eu confiance en moi, dit l’Éternel.
Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’”