< Ézéchiel 46 >
1 Ainsi parle le Seigneur Yahweh: " Le portique du parvis intérieur, qui regarde l'orient, restera fermé les six jours ouvriers, mais il sera ouvert le jour du sabbat; il sera aussi ouvert le jour de la nouvelle lune.
“Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano.
2 Le prince arrivera du dehors vers le vestibule du portique et se tiendra à côté du poteau du portique; les prêtres offriront son holocauste et ses sacrifices pacifiques. Il se prosternera sur le seuil du portique, et se retirera; et le portique ne sera pas fermé jusqu'au soir.
Mfumu izilowa podzera mʼkhonde la mʼkati la chipata pochokera kunja, nʼkudzayima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pa chiwundo cha pa chipatacho kenaka nʼkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo.
3 Le peuple du pays se prosternera à l'entrée de ce portique, aux sabbats et aux nouvelles lunes, devant Yahweh.
Anthu a mʼdziko azipembedza pamaso pa Yehova pa khomo la chipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa tsiku la mwezi watsopano.
4 L'holocauste que le prince offrira à Yahweh sera, le jour du sabbat, de six agneaux sans défaut et d'un bélier sans défaut;
Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Yehova ikhale motere: pa tsiku la Sabata izipereka ana ankhosa aamuna asanu ndi mmodzi wopanda chilema, ndiponso nkhosa yayima yopanda chilema.
5 et, comme oblation, il offrira un épha de farine pour le bélier; et, comme oblation pour les agneaux, ce qu'il voudra donner, avec un hin d'huile par épha.
Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu.
6 Le jour de la nouvelle lune, ce sera un jeune taureau, sans défaut, six agneaux et un bélier sans défaut.
Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema.
7 Et il donnera comme oblation un épha par bélier, et pour les agneaux, ce qu'il pourra donner, avec un hin d'huile par épha.
Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta.
8 Lorsque le prince entrera, il entrera par le vestibule du portique et sortira par le même chemin.
Pamene mfumu ikulowa, izidzera mʼkhonde lamʼkati la chipata chakummawa, izitulukiranso pomwepo.
9 Lorsque le peuple du pays entrera devant Yahweh dans les solennités, celui qui entrera par le portique du septentrion pour se prosterner, sortira par le portique du midi, et celui qui entrera par le portique du midi sortira par le portique du septentrion; on ne retournera pas par le portique par lequel on sera entré; mais on sortira par celui qui est en face de lui.
“Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho.
10 Le prince aussi entrera parmi eux quand ils entreront, et sortira comme ils sortiront.
Mfumu izidzakhala pakati pawo. Anthu akamadzalowa mfumu idzalowa nawo. Anthu akamadzatuluka mfumu idzatuluka nawo.
11 Aux fêtes et aux solennités, l'oblation sera d'un épha pour le taureau et d'un épha pour le bélier, et, pour les agneaux, ce que le prince voudra donner, avec un hin d'huile par épha.
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse.
12 Quand le prince offrira une offrande volontaire, holocauste ou sacrifices pacifiques, offrande volontaire à Yahweh, on lui ouvrira le portique qui regarde l'orient. Il offrira son holocauste ou ses sacrifices pacifiques, comme il le fait le jour du sabbat, et il sortira; et l'on fermera la porte après qu'il sera sorti.
Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.
13 Tu offriras un agneau d'un an sans défaut comme holocauste quotidien à Yahweh; tu l'offriras chaque matin.
“Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi.
14 Tu offriras avec lui chaque matin une oblation, savoir un sixième d'épha, et le tiers d'un hin d'huile pour arroser la fleur de farine, comme oblation à Yahweh; ce sont des lois permanentes, pour toujours.
Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo.
15 On offrira chaque matin l'agneau, l'oblation avec l'huile; c'est l'holocauste perpétuel. "
Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku.
16 Ainsi parle le Seigneur Yahweh: " Si le prince fait un don à quelqu'un de ses fils, ce don sera l'héritage de ses fils; ils le posséderont comme un héritage.
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo.
17 Mais s'il fait à l'un de ses serviteurs un don pris sur son héritage, ce don appartiendra au serviteur jusqu'à l'année de la libération; puis il retournera au prince; c'est à ses fils seulement que restera son héritage.
Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake.
18 Le prince ne prendra l'héritage de personne en l'expulsant violemment de sa propriété; c'est de sa propriété qu'il donnera un héritage à ses fils, afin que mon peuple ne soit pas chassé, chacun de sa possession. "
Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’”
19 Il me conduisit, par l'entrée qui est sur le côté du portique, dans les chambres saintes destinées aux prêtres, celles qui regardent le septentrion; et voici qu'il y avait là une place dans le fond, du côté de l'occident.
Kenaka munthu uja anandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandilowetsa ku zipinda za ansembe zoyangʼana kumpoto. Ndipo ndinaona kumeneko malo chakumadzulo kwa zipindazo.
20 Il me dit: " C'est l'endroit où les prêtres feront bouillir les victimes offertes pour le délit et pour le péché, et feront cuire l'oblation, afin de ne pas les transporter dans le parvis extérieur pour sanctifier le peuple. "
Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”
21 Puis il me fit sortir dans le parvis extérieur et me fit passer vers les quatre angles du parvis et voici qu'à chaque angle du parvis il y avait une cour.
Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina.
22 Aux quatre angles du parvis, il y avait des cours fermées, longues de quarante coudées et larges de trente: une même dimension pour ces quatre cours aux angles.
Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu.
23 Une enceinte les entourait toutes les quatre, et des foyers à cuire étaient établis au bas de ces enceintes, tout autour.
Kuzungulira mabwalo anayi angʼonoangʼono aja panali mpanda wamiyala, ndi malo asonkhapo moto omangidwa mʼmunsi mwa mpandawo mozungulira.
24 Il me dit: " Ce sont ici les cuisines où les serviteurs de la maison feront bouillir la chair des sacrifices du peuple. "
Munthuyo anandiwuza kuti, “Izi ndi zipinda zophikiramo. Mʼmenemu anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzaphikiramo nyama za nsembe za anthu.”