< Ézéchiel 31 >

1 La onzième année, au troisième mois, le premier du mois, la parole de Yahweh me fut adressée en ces termes:
Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 « Fils de l’homme, dis à Pharaon, roi d’Égypte, et à sa multitude: À qui ressembles-tu dans ta grandeur?
“Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti, “‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3 Voilà qu’Assur était un cèdre sur le Liban, à la belle ramure, à l’ombrage épais, à la taille élevée, et ayant sa cime dans les nues.
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango. Unali wautali, msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4 Les eaux l’avaient fait croître, l’abîme l’avait fait grandir, en faisant couler ses fleuves autour du lieu où il était planté et en envoyant ses ruisseaux à tous les arbres des champs.
Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo, akasupe ozama ankawutalikitsa. Mitsinje yake inkayenda mozungulira malo amene unaliwo ndipo ngalande zake zinkafika ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5 C’est pourquoi sa taille s’élevait, plus haute que les arbres des champs; ses branches avaient grandi, ses rameaux s’étaient allongés, grâce aux eaux abondantes du temps de sa croissance.
Choncho unatalika kwambiri kupambana mitengo yonse ya mʼmunda. Nthambi zake zinachuluka ndi kutalika kwambiri, chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6 Dans ses branches tous les oiseaux du ciel nichaient; sous ses rameaux mettaient bas tous les animaux des champs, et à son ombre étaient assises des nations nombreuses.
Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.
7 Il était beau par sa grandeur, par la longueur de ses branches, car ses racines plongeaient dans des eaux abondantes.
Unali wokongola kwambiri, wa nthambi zake zotambalala, chifukwa mizu yake inazama pansi kumene kunali madzi ochuluka.
8 Les cèdres ne l’obscurcissaient pas dans le jardin de Dieu, les cyprès n’égalaient pas ses branches, et les platanes n’étaient pas comme ses rameaux; aucun arbre dans le jardin de Dieu ne l’égalait en beauté.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanana nawo, kapena mitengo ya payini ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake. Munalibenso mtengo wa mkuyu nthambi zofanafana ndi zake. Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9 Je l’avais rendu beau par la multitude de ses rameaux; tous les arbres d’Éden lui portaient envie, tous ceux qui sont dans le jardin de Dieu.
Ine ndinawupanga wokongola wa nthambi zochuluka. Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa Mulungu inawuchitira nsanje.
10 C’est pourquoi ainsi parle le Seigneur Yahweh: Parce qu’il s’est élevé en hauteur, parce qu’il a porté sa cime jusque dans les nues; et que son cœur s’est enorgueilli de son élévation,
“‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake,
11 je l’ai livré aux mains du dieu des nations, qui le traitera à sa guise; à cause de sa méchanceté, je l’ai chassé.
ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake.
12 Des étrangers l’ont coupé, — nation féroce entre toutes, — et laissé là; sur les montagnes et dans toutes les vallées; ses branches sont tombées; ses rameaux brisés gisent dans tous les ravins du pays; tous les peuples de la terre se sont éloignés de son ombre et l’ont abandonné.
Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
13 Sur ses débris tous les oiseaux du ciel viennent se poser, et dans ses rameaux se sont retirés tous les animaux des champs:
Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake.
14 afin qu’aucun arbre planté sur les eaux ne s’élève en hauteur et ne porte sa cime jusque dans les nues, et qu’aucun de ceux qui s’abreuvent d’eau ne s’appuie sur lui-même dans son orgueil. Car ils sont tous voués à la mort, aux profondeurs de la terre, mêlés aux enfants des hommes; à ceux qui descendent dans la fosse.
Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15 Ainsi parle le Seigneur Yahweh: Le jour où il descendit au schéol, j’ai fait mener le deuil; à cause de lui j’ai voilé l’abîme, j’ai retenu le cours de ses fleuves, et les grandes eaux se sont arrêtées; à cause de lui, j’ai assombri le Liban, et à cause de lui, tous les arbres des champs ont langui. (Sheol h7585)
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. (Sheol h7585)
16 Au bruit de sa chute, j’ai fait trembler les nations, quand je l’ai fait descendre au schéol, avec ceux qui descendent dans la fosse. Ils se sont consolés dans les profondeurs de la terre, tous les arbres d’Éden, les plus beaux et les plus magnifiques du Liban, tous ceux que les eaux abreuvaient. (Sheol h7585)
Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. (Sheol h7585)
17 Ceux-là aussi sont descendus avec lui au schéol, vers les victimes de l’épée, qui étaient son bras et étaient assises à son ombre au milieu des nations. (Sheol h7585)
Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu. (Sheol h7585)
18 Ainsi à qui ressembles-tu en gloire et en grandeur, parmi les arbres d’Éden? Tu seras précipité avec les arbres d’Éden, dans les profondeurs de la terre, pour être couché au milieu d’incirconcis, avec ceux que l’épée a transpercés. Tel sera le sort de Pharaon et de toute sa multitude; — oracle du Seigneur Yahweh. »
“‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo. “‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’”

< Ézéchiel 31 >