< 1 Chroniques 12 >
1 Voici ceux qui vinrent vers David à Siceleg, lorsqu'il devait encore se tenir éloigné de la face de Saül, fils de Cis; ils étaient parmi les vaillants qui le secoururent pendant la guerre.
Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo.
2 C'étaient des archers, exercés à lancer des pierres de la main droite et de la main gauche, et à tirer des flèches avec leur arc; ils étaient d'entre les frères de Saül, de Benjamin.
Iwo anali ndi mauta ndipo amadziwa kuponya mivi komanso miyala, ndipo amatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwo anali abale ake a Sauli ochokera ku fuko la Benjamini.
3 A leur tête Ahiéser, puis Joas, tous deux fils de Samaa, de Gabaa; Jaziel et Phallet, fils d'Azmoth; Baracha; Jéhu, d'Anatoth;
Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri ndi Yowasi ana a Semaya wa ku Gibeya; Yezieli ndi Peleti ana a Azimaveti; Beraka, Yehu wa ku Anatoti,
4 Samaïas, de Gabaon, vaillant parmi les Trente et chef des Trente; Jérémie; Jéhéziel; Johanan; Jézabad, de Gédéra;
ndi Isimaiya wa ku Gibiyoni, munthu wamphamvu mʼgulu la anthu makumi atatu aja, yemwenso anali mtsogoleri wawo; Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gederi,
5 Eluzaï; Jérimuth; Baalia; Samaria; Saphatia, de Haruph;
Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya Mharufi;
6 Elcana, Jésia, Azaréel, Joéser et Jesbaam, fils de Coré;
Elikana, Isiya, Azareli, Yowezeri ndi Yasobeamu a ku banja la Kora;
7 Joéla et Zabadia, fils de Jéroham, de Gédor.
ndi Yowela ndi Zebadiya ana a Yerohamu wa ku Gedori.
8 Parmi les Gadites, des hommes vaillants passèrent auprès de David, dans les lieux forts, au désert: guerriers exercés au combat, sachant manier le bouclier et la lance, ayant un aspect de lions, aussi agiles que des gazelles sur les montagnes.
Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri.
9 Ezer était le chef; Obdias, le second; Eliab, le troisième;
Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wotsatana naye anali Obadiya, wachitatu anali Eliabu,
10 Masmana, le quatrième; Jérémie, le cinquième;
wachinayi anali Misimana, Yeremiya anali wachisanu,
11 Ethi, le sixième; Eliel, le septième;
wachisanu ndi chimodzi anali Atai, Elieli anali wachisanu ndi chiwiri,
12 Johanan, le huitième; Elzébad, le neuvième;
wachisanu ndi chitatu anali Yohanani, Elizabadi anali wachisanu ndi chinayi,
13 Jérémie, le dixième; Machbanaï, le onzième.
wakhumi anali Yeremiya ndipo Makibanai anali wa 11.
14 C'étaient des fils de Gad, chefs de l'armée; un seul, le plus petit, pouvait l'emporter sur cent, et le plus grand sur mille.
Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000.
15 Ce sont eux qui passèrent le Jourdain au premier mois, alors qu'il déborde sur toutes ses rives, et qui mirent en fuite tous les habitants des vallées, à l'orient et à l'occident.
Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa.
16 Des fils de Benjamin et de Juda vinrent vers David, dans les lieux forts.
Anthu ena a fuko la Benjamini ndi ena ochokera ku Yuda anabweranso kwa Davide pamene anali ku linga lake.
17 David sortit au-devant d'eux, prit la parole, et leur dit: " Si vous êtes venus à moi avec des sentiments pacifiques, pour me secourir, mon cœur se portera vers vous, en vue de nous unir; mais si c'est pour me livrer perfidement à mes ennemis, lorsque aucune violence ne s'attache à mes mains, que le Dieu de nos pères le voie et qu'il fasse justice! "
Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”
18 L'Esprit revêtit Amasaï, chef des Trente, et il dit: " A toi, David, et avec toi, fils d'Isaï! Paix, paix à toi, et paix à celui qui te secourt, car ton Dieu t'a secouru! " Et David les accueillit et les plaça parmi les chefs de la bande.
Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati: “Inu Davide, ife ndife anu! Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese! Kupambana, Kupambana kwa inu, ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.” Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo.
19 Des hommes de Manassé se joignirent à David, lorsqu'il alla avec les Philistins faire la guerre à Saül. Mais ils ne secoururent pas les Philistins; car les princes des Philistins renvoyèrent à dessein David en disant: " Au péril de nos têtes, il joindrait son maître Saül. "
Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).”
20 Comme il revenait à Siceleg, des hommes de Manassé se joignirent à lui: Ednas, Jozabad, Jédihel, Michaël, Jozabad, Eliu et Salathi, chefs des milliers de Manassé.
Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase.
21 Ils secoururent David contre les bandes, car ils étaient tous des vaillants, et ils furent chefs dans l'armée.
Iwowa anathandiza Davide kulimbana ndi magulu achifwamba, pakuti onsewa anali asilikali olimba mtima ndipo anali atsogoleri mʼgulu lake la ankhondo.
22 Et de jour en jour des hommes arrivaient auprès de David pour le secourir, jusqu'à ce qu'il eût une grande armée, comme une armée de Dieu.
Tsiku ndi tsiku anthu amabwera kudzathandiza Davide, mpaka anakhala ndi gulu lalikulu la ankhondo, ngati gulu la ankhondo a Mulungu.
23 Voici le nombre des chefs des hommes armés pour la guerre qui vinrent auprès de David à Hébron, pour lui transférer la royauté de Saül, selon l'ordre de Yahweh.
Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova:
24 Fils de Juda, portant le bouclier et la lance, six mille huit cents, armés pour la guerre. —
Anthu a fuko la Yuda onyamula chishango ndi mkondo analipo 6,800;
25 Des fils de Siméon, hommes vaillants à la guerre, sept mille cent. —
Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100;
26 Des fils de Lévi, quatre mille six cents;
Anthu a fuko la Levi analipo 4,600,
27 et Joïada, chef de la famille d'Aaron, et avec lui trois mille sept cents;
mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700,
28 et Sadoc, jeune homme vaillant, et la maison de son père, vingt-deux chefs. —
ndi Zadoki, mnyamata wankhondo wolimba mtima, anabwera ndi akuluakulu 22 ochokera mʼbanja lake;
29 Des fils de Benjamin, frères de Saül, trois mille; car jusqu'alors la plus grande partie d'entre eux gardaient fidélité à la maison de Saül. —
Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi;
30 Des fils d'Ephraïm, vingt mille huit cents, hommes vaillants et renommés dans les maisons de leurs pères. —
Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800;
31 De la demi-tribu de Manassé, dix-huit mille, qui furent nominativement désignés pour aller établir David roi. —
Anthu a fuko latheka la Manase amene anawayitana kuti adzakhazikitse nawo ufumu wa Davide analipo 18,000;
32 Des fils d'Issachar, ayant l'intelligence des temps pour savoir ce que devait faire Israël, deux cents chefs, et tous leurs frères sous leurs ordres. —
Anthu a fuko la Isakara amene ankazindikira nthawi ndipo amadziwa zimene Israeli ankayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi abale awo onse amene amawatsogolera.
33 De Zabulon, cinquante mille, en état d'aller à l'armée, prêts à la guerre et en parfait équipement de guerre, pour se ranger en bataille d'un cœur résolu. —
Anthu a fuko la Zebuloni, analipo 5,000. Iwowa anali asilikali odziwa bwino nkhondo, okhala ndi zida za mtundu uliwonse, okonzekera kudzathandiza Davide ndi mtima umodzi.
34 De Nephthali, mille chefs, et avec eux trente-sept mille, portant le bouclier et la lance. —
Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo;
35 Des Danites prêts à la guerre, vingt-huit mille six cents. —
Anthu a fuko la Dani, okonzekera nkhondo analipo 28,600.
36 D'Aser, en état d'aller à l'armée et prêts à la guerre, quarante mille. —
Anthu a fuko la Aseri, asilikali odziwa bwino nkhondo, okonzekeradi nkhondo analipo 40,000;
37 Et de l'autre coté du Jourdain, des Rubenites, des Gadites et de la demi-tribu de Manassé, en parfait équipement d'armes de guerre, cent vingt mille.
Ndipo kuchokera kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase, amene anali ndi zida za mtundu uliwonse analipo 120,000.
38 Tous ces hommes de guerre, sachant se ranger en bataille, vinrent d'un cœur sincère à Hébron pour établir David roi sur tout Israël; et tout le reste d'Israël n'avait également qu'un cœur pour établir David roi.
Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu.
39 Ils furent là trois jours avec David, mangeant et buvant, car leurs frères leur avaient préparé des provisions.
Anthuwa anakhala ndi Davide masiku atatu akudya ndi kumwa pakuti mabanja awo anawapatsa zakudya.
40 Et même ceux qui habitaient près d'eux, jusqu'à Issachar, à Zabulon et à Nephthali, apportaient des vivres sur des ânes, sur des chameaux, sur des mulets et sur des bœufs, des provisions de farine, des masses de figues sèches et des raisins secs, du vin, de l'huile, des bœufs et des brebis en abondance; car il y avait joie en Israël.
Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.