< Job 13 >

1 Voilà que mon œil a vu tout cela, mon oreille l’a entendu et compris.
“Ndaziona ndi maso anga zonsezi, ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.
2 Ce que vous savez, moi aussi je le sais, je ne vous suis en rien inférieur.
Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa; ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
3 Mais je veux parler au Tout-Puissant, je veux plaider ma cause avec Dieu.
Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.
4 Car vous n’êtes que des charlatans, vous êtes tous des médecins inutiles.
Koma inu mukundipaka mabodza; nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!
5 Que ne gardiez-vous le silence! Il vous eût tenu lieu de sagesse.
Achikhala munangokhala chete nonsenu! Apo mukanachita zanzeru.
6 Ecoutez, je vous prie, ma défense, soyez attentifs au plaidoyer de mes lèvres.
Tsopano imvani kudzikanira kwanga; imvani kudandaula kwa pakamwa panga.
7 Parlerez-vous mensonge en faveur de Dieu, pour lui, parlerez-vous tromperie?
Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu? Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?
8 Ferez-vous pour Dieu acception de personnes, vous constituerez-vous avocats?
Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera? Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?
9 Vous en saura-t-il gré, s’il sonde vos cœurs? Le tromperez-vous comme on trompe un homme?
Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa? Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?
10 Certainement il vous condamnera, si vous faites en secret acception de personnes.
Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani ngati muchita zokondera mseri.
11 Oui, sa majesté vous épouvantera, ses terreurs tomberont sur vous.
Kodi ulemerero wake sungakuopseni? Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?
12 Vos arguments sont des raisons de poussière, vos forteresses sont des forteresses d’argile.
Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo; mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.
13 Taisez-vous, laissez-moi, je veux parler; il m’en arrivera ce qu’il pourra.
“Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule; tsono zimene zindichitikire zichitike.
14 Je veux prendre ma chair entre les dents, je veux mettre mon âme dans ma main.
Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
15 Quand il me tuerait, que je n’aurais rien à espérer, je défendrai devant lui ma conduite.
Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira; ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
16 Mais il sera mon salut, car l’impie ne saurait paraître en sa présence.
Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
17 Ecoutez donc mes paroles, prêtez l’oreille à mon discours.
Mvetserani mosamala mawu anga; makutu anu amve zimene ndikunena.
18 Voici que j’ai préparé ma cause, je sais que je serai justifié.
Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga, ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
19 Est-il quelqu’un qui veuille plaider contre moi? A l’instant même je veux me taire et mourir.
Kodi alipo wina amene angatsutsane nane? ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.
20 Seulement épargne-moi deux choses, ô Dieu, et je ne me cacherai pas devant ta face:
“Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi, ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:
21 éloigne ta main de dessus moi, et que tes terreurs ne m’épouvantent plus.
Muchotse dzanja lanu pa ine, ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.
22 Après cela, appelle, et je répondrai; ou bien je parlerai d’abord, et tu me répondras.
Tsono muyitane ndipo ndidzayankha, kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.
23 Quel est le nombre de mes iniquités et de mes péchés? Fais-moi connaître mes transgressions et mes offenses.
Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati? Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.
24 Pourquoi cacher ainsi ton visage, et me regarder comme ton ennemi!
Chifukwa chiyani mukundifulatira ndi kundiyesa ine mdani wanu?
25 Veux-tu donc effrayer une feuille agitée par le vent, poursuivre une paille desséchée,
Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo? Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?
26 pour que tu écrives contre moi des choses amères, pour que tu m’imputes les fautes de ma jeunesse,
Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.
27 pour que tu mettes mes pieds dans les ceps, que tu observes toutes mes démarches, que tu traces une limite à la plante de mes pieds,
Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo. Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.
28 alors que mon corps se consume comme un bois vermoulu, comme un vêtement que dévore la teigne.
“Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.

< Job 13 >