< 2 Rois 24 >

1 De son temps, Nebucadnetsar, roi de Babylone, monta et Jehoïakim devint son serviteur pendant trois ans. Puis il se retourna et se rebella contre lui.
Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara.
2 Yahvé envoya contre lui des troupes de Chaldéens, des troupes de Syriens, des troupes de Moabites et des troupes d'Ammonites, et il les envoya contre Juda pour le détruire, selon la parole de Yahvé, qu'il avait prononcée par ses serviteurs les prophètes.
Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake.
3 Mais, sur l'ordre de l'Éternel, cela arriva à Juda, pour le soustraire à sa vue, à cause des péchés de Manassé, selon tout ce qu'il a fait,
Ndithu, izi zinachitikira Yuda monga momwe Yehova analamulira nʼcholinga choti awachotse pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase ndi zonse zimene anachita,
4 et aussi à cause du sang innocent qu'il a répandu, car il a rempli Jérusalem de sang innocent, et l'Éternel n'a pas voulu pardonner.
kuphatikizapo kukhetsa magazi a anthu osalakwa. Chifukwa iye anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kumukhululukira.
5 Le reste des actes de Jojakim, et tout ce qu'il a fait, cela n'est-il pas écrit dans le livre des Chroniques des rois de Juda?
Ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
6 Jehoïakim se coucha avec ses pères, et Jehoïakin, son fils, régna à sa place.
Yehoyakimu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
7 Le roi d'Égypte ne sortit plus de son pays, car le roi de Babylone avait pris, depuis le ruisseau d'Égypte jusqu'au fleuve Euphrate, tout ce qui appartenait au roi d'Égypte.
Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.
8 Jojakin avait dix-huit ans lorsqu'il devint roi, et il régna trois mois à Jérusalem. Le nom de sa mère était Nehushta, fille d'Elnathan, de Jérusalem.
Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
9 Il fit ce qui est mal aux yeux de l'Éternel, selon tout ce qu'avait fait son père.
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira abambo ake.
10 En ce temps-là, les serviteurs de Nebucadnetsar, roi de Babylone, montèrent à Jérusalem, et la ville fut assiégée.
Nthawi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ku Yerusalemu nazinga mzindawo ndi misasa ya nkhondo
11 Nebucadnetsar, roi de Babylone, arriva dans la ville pendant que ses serviteurs l'assiégeaient.
ndipo Nebukadinezara anafika ku mzindawo pamene ankhondo ake anawuzinga.
12 Jehoïachin, roi de Juda, sortit vers le roi de Babylone, lui, sa mère, ses serviteurs, ses chefs et ses officiers, et le roi de Babylone le captura la huitième année de son règne.
Yehoyakini mfumu ya Yuda pamodzi ndi amayi ake, atumiki ake, anthu ake olemekezeka ndiponso akuluakulu onse anadzipereka kwa mfumu ya ku Babuloni. Mfumu ya Babuloni inagwira Yoyakini ukapolo mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
13 Il emporta de là tous les trésors de la maison de l'Éternel et les trésors de la maison du roi, et il mit en pièces tous les vases d'or que Salomon, roi d'Israël, avait faits dans le temple de l'Éternel, comme l'Éternel l'avait dit.
Monga ananenera Yehova, Nebukadinezara anachotsa chuma chonse cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso cha mʼnyumba ya mfumu ndipo anatenga ziwiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Yehova zimene Solomoni mfumu ya Israeli anapanga.
14 Il emmena tout Jérusalem, tous les chefs et tous les vaillants hommes, dix mille captifs, et tous les artisans et les forgerons. Il ne resta plus que le peuple le plus pauvre du pays.
Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.
15 Il emmena Jehoïachin à Babylone, avec la mère du roi, les femmes du roi, ses officiers et les chefs du pays. Il les emmena en captivité de Jérusalem à Babylone.
Nebukadinezara anatenga Yehoyakini ngati kapolo kupita naye ku Babuloni. Mu Yerusalemu anatenganso amayi a mfumu, akazi ake, akuluakulu ake ndiponso anthu olemekezeka mʼdzikomo.
16 Le roi de Babylone emmena en captivité à Babylone tous les vaillants hommes, au nombre de sept mille, et les artisans et les forgerons, au nombre de mille, tous forts et aptes à la guerre.
Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000.
17 Le roi de Babylone fit régner à sa place Matthania, frère du père de Jojakin, et changea son nom en Sédécias.
Iye analonga ufumu Mataniya, malume wa Yoyakini mʼmalo mwake ndipo anasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
18 Sédécias avait vingt et un ans lorsqu'il devint roi, et il régna onze ans à Jérusalem. Le nom de sa mère était Hamutal, fille de Jérémie, de Libna.
Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
19 Il fit ce qui est mal aux yeux de l'Éternel, selon tout ce qu'avait fait Jehoïakim.
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Yehoyakimu.
20 Car, par la colère de l'Éternel, cela arriva à Jérusalem et en Juda, jusqu'à ce qu'il les eût chassés de sa présence. Sédécias s'est alors rebellé contre le roi de Babylone.
Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake. Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.

< 2 Rois 24 >