< 1 Korintanoj 11 >

1 Vi estu imitantoj de mi, kiel mi ankaŭ estas imitanto de Kristo.
Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.
2 Mi laŭdas vin, ke vi min memoras en ĉio, kaj ke vi firme tenas la tradiciojn, ĝuste kiel mi transdonis ilin al vi.
Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani.
3 Sed mi volas sciigi vin, ke la kapo de ĉiu viro estas Kristo; kaj la kapo de virino estas viro; kaj la kapo de Kristo estas Dio.
Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu.
4 Ĉiu viro, preĝanta aŭ profetanta kun kapo kovrita, malhonoras sian kapon.
Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo.
5 Sed ĉiu virino, preĝanta aŭ profetanta kun kapo senvuala, malhonoras sian kapon; ĉar tio estas tia sama, kvazaŭ ŝi estus razita.
Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake.
6 Ĉar se virino ne estas vualita, ŝi ankaŭ tondiĝu; sed se estas hontinde por virino esti kun haroj tonditaj aŭ razitaj, ŝi estu vualita.
Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.
7 Ĉar viro devas ne havi la kapon vualita, pro tio, ke li estas la bildo kaj gloro de Dio; sed virino estas la gloro de viro.
Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.
8 Ĉar viro ne estas el virino, sed virino el viro;
Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna.
9 ĉar ankaŭ viro ne estas kreita por virino, sed virino por viro;
Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.
10 pro tio virino devas havi sur la kapo signon de aŭtoritato, pro la anĝeloj.
Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake.
11 Tamen ne ekzistas virino sen viro, nek viro sen virino, en la Sinjoro.
Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi.
12 Ĉar kiel virino estas el viro, tiel same ankaŭ estas viro per virino; sed ĉio estas el Dio.
Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.
13 Juĝu en vi mem: ĉu decas, ke virino preĝu al Dio nevualite?
Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu?
14 Ĉu eĉ la naturo mem ne instruas vin, ke se viro havas longajn harojn, tio estas por li malhonoro?
Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali,
15 Sed se virino havas longajn harojn, tio estas por ŝi gloro; ĉar ŝiaj haroj estas donitaj al ŝi kiel kovraĵo.
koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu.
16 Sed se iu ŝajnas esti disputema, ni ne havas tian kutimon, nek la eklezioj de Dio.
Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.
17 Sed ordonante al vi jene, mi ne laŭdas vin, ke vi kunvenas ne por pliboniĝo, sed por malpliboniĝo.
Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino.
18 Ĉar unue mi aŭdas, ke kiam vi kunvenas en la eklezio, ekzistas inter vi skismoj; kaj mi parte kredas tion.
Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona.
19 Ĉar necese estas, ke ankaŭ herezoj estu inter vi, por ke la aprobitoj evidentiĝu inter vi.
Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu.
20 Kiam do vi kunvenas, estas neeble manĝi la Sinjoran vespermanĝon;
Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye.
21 ĉar en via manĝado ĉiu antaŭ alia prenas sian propran vespermanĝon; kaj unu malsatas, kaj alia drinkas.
Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera.
22 Kio? ĉu vi ne havas domojn, en kiuj vi povas manĝi kaj trinki? aŭ ĉu vi malestimas la eklezion de Dio, kaj hontigas la nehavantojn? Kion mi diros? ĉu mi vin laŭdos en tio? Mi ja vin ne laŭdas.
Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.
23 Ĉar mi ricevis de la Sinjoro tion, kion mi ankaŭ transdonis al vi, ke la Sinjoro Jesuo en la nokto, en kiu li estis perfidata, prenis panon;
Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi.
24 kaj doninte dankon, li dispecigis ĝin, kaj diris: Ĉio tio estas mia korpo, kiu estas por vi; ĉi tion faru por memorigo pri mi.
Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
25 Tiel same ankaŭ la kalikon post la vespermanĝo, dirante: Ĉi tiu kaliko estas la nova interligo en mia sango; ĉi tion faru ĉiufoje, kiam vi trinkos, por memorigo pri mi.
Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.”
26 Ĉar ĉiufoje, kiam vi manĝos ĉi tiun panon kaj trinkos la kalikon, vi proklamos la morton de la Sinjoro, ĝis li venos.
Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.
27 Tial ĉiu, kiu neinde manĝos la panon aŭ trinkos la kalikon de la Sinjoro, kulpiĝos pri la korpo kaj la sango de la Sinjoro.
Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye.
28 Sed oni sin provu, kaj tiele manĝu el la pano kaj trinku el la kaliko.
Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi.
29 Ĉar la manĝanto kaj trinkanto manĝas kaj trinkas juĝon al si mem, se li ne pripensas la korpon.
Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe.
30 Pro tio multaj inter vi estas malfortaj kaj malsanaj, kaj ne malmultaj dormas.
Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo.
31 Sed se ni pripensus nin mem, ni ne estus juĝitaj.
Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso.
32 Sed kiam ni estas juĝataj, ni estas punataj de la Sinjoro, por ke ni ne estu kondamnitaj kune kun la mondo.
Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
33 Tial, miaj fratoj, kiam vi kunvenas por manĝi, atendu unu la alian.
Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane.
34 Se iu malsatas, li manĝu hejme, por ke via kunvenado ne enkonduku juĝon. Kaj la ceteron mi ordigos, kiam mi venos.
Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo. Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.

< 1 Korintanoj 11 >