< Psalms 88 >
1 A Song, a Psalm, by sons of Korah, to the Overseer, 'Concerning the Sickness of Afflictions.' — An instruction, by Heman the Ezrahite. O Jehovah, God of my salvation, Daily I have cried, nightly before Thee,
Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara. Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
2 My prayer cometh in before Thee, Incline Thine ear to my loud cry,
Pemphero langa lifike pamaso panu; tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.
3 For my soul hath been full of evils, And my life hath come to Sheol. (Sheol )
Pakuti ndili ndi mavuto ambiri ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda. (Sheol )
4 I have been reckoned with those going down [to] the pit, I have been as a man without strength.
Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje; ndine munthu wopanda mphamvu.
5 Among the dead — free, As pierced ones lying in the grave, Whom Thou hast not remembered any more, Yea, they by Thy hand have been cut off.
Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
6 Thou hast put me in the lowest pit, In dark places, in depths.
Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni, mʼmalo akuya a mdima waukulu.
7 Upon me hath Thy fury lain, And [with] all Thy breakers Thou hast afflicted. (Selah)
Ukali wanu ukundipsinja kwambiri, mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse. (Sela)
8 Thou hast put mine acquaintance far from me, Thou hast made me an abomination to them, Shut up — I go not forth.
Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo. Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;
9 Mine eye hath grieved because of affliction, I called Thee, O Jehovah, all the day, I have spread out unto Thee my hands.
maso anga ada ndi chisoni. Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse; ndimakweza manja anga kwa Inu.
10 To the dead dost Thou do wonders? Do Rephaim rise? do they thank Thee? (Selah)
Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa? Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu? (Sela)
11 Is Thy kindness recounted in the grave? Thy faithfulness in destruction?
Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda, za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?
12 Are Thy wonders known in the darkness? And Thy righteousness in the land of forgetfulness?
Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima, kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?
13 And I, unto Thee, O Jehovah, I have cried, And in the morning doth my prayer come before Thee.
Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo; mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.
14 Why, O Jehovah, castest Thou off my soul? Thou hidest Thy face from me.
Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana ndi kundibisira nkhope yanu?
15 I [am] afflicted, and expiring from youth, I have borne Thy terrors — I pine away.
Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa; ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.
16 Over me hath Thy wrath passed, Thy terrors have cut me off,
Ukali wanu wandimiza; zoopsa zanu zandiwononga.
17 They have surrounded me as waters all the day, They have gone round against me together,
Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula; zandimiza kwathunthu.
18 Thou hast put far from me lover and friend, Mine acquaintance [is] the place of darkness!
Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga; mdima ndiye bwenzi langa lenileni.