< Ezekiel 48 >
1 And these [are] the names of the tribes: From the north end unto the side of the way of Hethlon, at the coming in to Hamath, Hazar-Enan, the border of Damascus northward, unto the side of Hamath, and they have been his — side east and west, Dan one,
“Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.
2 and by the border of Dan, from the east side unto the west side, Asher one,
“Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
3 and by the border of Asher, from the east side even unto the west side, Naphtali one,
“Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
4 and by the border of Naphtali, from the east side unto the west side, Manasseh one,
“Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
5 and by the border of Manasseh, from the east side unto the west side, Ephraim one,
“Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
6 and by the border of Ephraim, from the east side even unto the west side, Reuben one,
“Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
7 and by the border of Reuben, from the east side unto the west side, Judah one,
“Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
8 and by the border of Judah, from the east side unto the west side is the heave-offering that ye lift up, five and twenty thousand broad and long, as one of the parts, from the east side unto the west side: and the sanctuary hath been in its midst.
“Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.
9 The heave-offering that ye lift up to Jehovah [is] five and twenty thousand long, and broad ten thousand.
“Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu.
10 And of these is the holy heave-offering for the priests, northward five and twenty thousand, and westward [in] breadth ten thousand, and eastward [in] breadth ten thousand, and southward [in] length five and twenty thousand: and the sanctuary of Jehovah hath been in its midst.
Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu.
11 For the priests who are sanctified of the sons of Zadok, who have kept My charge, who erred not in the erring of the sons of Israel, as the Levites erred,
Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera.
12 even the heave-offering hath been to them, out of the heave-offering of the land, most holy, by the border of the Levites.
Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.
13 'And [to] the Levites over-against the border of the priests [are] five and twenty thousand [in] length, and [in] breadth ten thousand, all the length [is] five and twenty thousand, and the breadth ten thousand.
“Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu.
14 And they do not sell of it, nor exchange, nor cause to pass away the first-fruit of the land: for [it is] holy to Jehovah.
Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.
15 And the five thousand that is left in the breadth, on the front of the five and twenty thousand, is common — for the city, for dwelling, and for suburb, and the city hath been in its midst.
“Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati.
16 And these [are] its measures: the north side five hundred, and four thousand, and the south side five hundred, and four thousand, and on the east side five hundred, and four thousand, and the west side five hundred, and four thousand.
Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250.
17 And the suburb to the city hath been northward, fifty and two hundred, and southward, fifty and two hundred, and eastward, fifty and two hundred, and westward, fifty and two hundred.
Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125.
18 'And the residue in length over-against the heave-offering of the holy [portion is] ten thousand eastward, and ten thousand westward, and it hath been over-against the heave-offering of the holy [portion], and its increase hath been for food to the servants of the city,
Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda.
19 even [to] him who is serving the city, they serve it out of all the tribes of Israel.
Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli.
20 All the heave-offering [is] five and twenty thousand by five and twenty thousand, square do ye lift up the heave-offering of the holy [portion] with the possession of the city.
Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.
21 'And the residue [is] for the prince, on this side and on that side of the heave-offering of the holy [portion], and of the possession of the city, on the front of the five and twenty thousand of the heave-offering unto the east border, and westward, on the front of the five and twenty thousand on the west border, over-against the portions of the prince; and the heave-offering of the holy [portion], and the sanctuary of the house, hath been in its midst.
“Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu.
22 And from the possession of the Levites, from the possession of the city, in the midst of that which is to the prince, between the border of Judah and the border of Benjamin, there is to the prince.
Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.
23 'As to the rest of the tribes, from the east side unto the west side, Benjamin one,
“Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.
24 and by the border of Benjamin, from the east side unto the west side, Simeon one,
“Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
25 and by the border of Simeon, from the east side unto the west side, Issachar one,
“Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
26 and by the border of Issachar, from the east side unto the west side, Zebulun one,
“Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
27 and by the border of Zebulun, from the east side unto the west side, Gad one,
“Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
28 and by the border of Gad, at the south side southward, the border hath been from Tamar [to] the waters of Meriboth-Kadesh, the stream by the great sea.
“Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
29 This [is] the land that ye separate by inheritance to the tribes of Israel, and these [are] their portions — an affirmation of the Lord Jehovah.
“Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
30 'And these [are] the outgoings of the city on the north side, five hundred, and four thousand measures.
“Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250,
31 And the gates of the city [are] according to the names of the tribes of Israel; three gates northward: the gate of Reuben one, the gate of Judah one, the gate of Levi one.
kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.
32 And on the east side five hundred, and four thousand, and three gates: the gate of Joseph one, the gate of Benjamin one, the gate of Dan one.
“Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.
33 And the south side five hundred, and four thousand measures, and three gates: the gate of Simeon one, the gate of Issachar one, the gate of Zebulun one.
“Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.
34 The west side five hundred, and four thousand, their gates three: the gate of Gad one, the gate of Asher one, the gate of Naphtali one.
“Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.
35 Round about [is] eighteen thousand, and the renown of the city [is] from the day Jehovah [is] there.'
“Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000. “Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala: Yehova Ali Pano.”