< 2 Kings 20 >
1 In those days hath Hezekiah been sick unto death, and come unto him doth Isaiah son of Amoz the prophet, and saith unto him, 'Thus said Jehovah: Give a charge to thy house, for thou art dying, and dost not live.'
Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.”
2 And he turneth round his face unto the wall, and prayeth unto Jehovah, saying,
Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti,
3 'I pray Thee, O Jehovah, remember, I pray Thee, how I have walked habitually before Thee in truth, and with a perfect heart, and that which [is] good in Thine eyes I have done;' and Hezekiah weepeth — a great weeping.
“Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.
4 And it cometh to pass — Isaiah hath not gone out to the middle court — that the word of Jehovah hath been unto him, saying,
Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti,
5 'Turn back, and thou hast said unto Hezekiah, leader of My people: Thus said Jehovah, God of David thy father, I have heard thy prayer, I have seen thy tear, lo, I give healing to thee, on the third day thou dost go up to the house of Jehovah;
“Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.
6 and I have added to thy days fifteen years, and out of the hand of the king of Asshur I deliver thee and this city, and have covered over this city for Mine own sake, and for the sake of David My servant.'
Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’”
7 And Isaiah saith, 'Take ye a cake of figs;' and they take and lay [it] on the boil, and he reviveth.
Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira.
8 And Hezekiah saith unto Isaiah, 'What [is] the sign that Jehovah doth give healing to me, that I have gone up on the third day to the house of Jehovah?'
Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”
9 And Isaiah saith, 'This [is] to thee the sign from Jehovah, that Jehovah doth the thing that He hath spoken — The shadow hath gone on ten degrees, or it doth turn back ten degrees?'
Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”
10 And Hezekiah saith, 'It hath been light for the shadow to incline ten degrees: nay, but let the shadow turn backward ten degrees.'
Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”
11 And Isaiah the prophet calleth unto Jehovah, and He bringeth back the shadow by the degrees that it had gone down in the degrees of Ahaz — backward ten degrees.
Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga.
12 At that time hath Berodach-Baladan son of Baladan king of Babylon sent letters and a present unto Hezekiah, for he heard that Hezekiah had been sick;
Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo.
13 and Hezekiah hearkeneth unto them, and sheweth them all the house of his treasury, the silver, and the gold, and the spices, and the good ointment, and all the house of his vessels, and all that hath been found in his treasuries; there hath not been a thing that Hezekiah hath not shewed them, in his house, and in all his dominion.
Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.
14 And Isaiah the prophet cometh in unto king Hezekiah, and saith unto him, 'What said these men? and whence come they unto thee?' And Hezekiah saith, 'From a land afar off they have come — from Babylon.'
Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
15 And he saith, 'What saw they in thy house?' and Hezekiah saith, 'All that [is] in my house they saw; there hath not been a thing that I have not shewed them among my treasures.'
Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?” Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”
16 And Isaiah saith unto Hezekiah, 'Hear a word of Jehovah:
Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena:
17 Lo, days are coming, and borne hath been all that [is] in thy house, and that thy father have treasured up till this day, to Babylon; there is not left a thing, said Jehovah;
Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova.
18 and of thy sons who go out from thee, whom thou begettest, they take away, and they have been eunuchs in the palace of the king of Babylon.'
Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”
19 And Hezekiah saith unto Isaiah, 'Good [is] the word of Jehovah that thou hast spoken;' and he saith, 'Is it not — if peace and truth are in my days?'
Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’”
20 And the rest of the matters of Hezekiah, and all his might, and how he made the pool, and the conduit, and bringeth in the waters to the city, are they not written on the book of the Chronicles of the kings of Judah?
Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
21 And Hezekiah lieth with his fathers, and reign doth Manasseh his son in his stead.
Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.