< Romans 15 >

1 But we saddere men owen to susteyne the feblenesses of sijke men, and not plese to vs silf.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha.
2 Eche of vs plese to his neiybore in good, to edificacioun.
Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa.
3 For Crist pleside not to hym silf, as it is writun, The repreues of men dispisynge thee, felden on me.
Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretsa yekha koma, monga kwalembedwa kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani chinagwera Ine.”
4 For what euere thingis ben writun, tho ben writun to oure techynge, that bi pacience and coumfort of scripturis we haue hope.
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
5 But God of pacience and of solace yyue to you to vndurstonde the same thing, ech in to othere aftir Jhesu Crist,
Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu,
6 that ye of o wille with o mouth worschipe God and the fadir of oure Lord Jhesu Crist.
kotero kuti ndi mtima umodzi ndi movomerezana mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
7 For which thing take ye togidere, as also Crist took you in to the onour of God.
Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke.
8 For Y seie, that Jhesu Crist was a mynystre of circumcisioun for the treuthe of God, to conferme the biheestis of fadris.
Chifukwa kunena zoona, Khristu wasanduka mtumiki wa Ayuda, kuonetsa kuti Mulungu ndi wokhulupirika pa malonjezo amene anachita kwa makolo awo
9 And hethene men owen to onoure God for merci; as it is writun, Therfor, Lord, Y schal knowleche to thee among hethene men, and Y schal synge to thi name.
kuti a mitundu ina atamande Mulungu chifukwa cha chifundo chake. Monga kwalembedwa kuti, “Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa a mitundu; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
10 And eft he seith, Ye hethene men, be ye glad with his puple.
Akutinso, “Kondwerani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.”
11 And eft, Alle hethene men, herie ye the Lord; and alle puplis, magnefie ye hym.
Ndipo akutinso, “Tamandani Ambuye, inu nonse a mitundu ina, ndi kuyimba zotamanda Iye, inu anthu onse.”
12 And eft Isaie seith, Ther schal be a roote of Jesse, that schal rise vp to gouerne hethene men, and hethene men schulen hope in hym.
Ndiponso Yesaya akuti, “Muzu wa Yese udzaphuka, wina amene adzauka kulamulira anthu a mitundu ina; mwa Iye mudzakhala chiyembekezo cha a mitundu ina.”
13 And God of hope fulfille you in al ioye and pees in bileuynge, that ye encrees in hope and vertu of the Hooli Goost.
Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.
14 And, britheren, Y my silf am certeyn of you, that also ye ben ful of loue, and ye ben fillid with al kunnyng, so that ye moun moneste ech other.
Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake.
15 And, britheren, more boldli Y wroot to you a parti, as bryngynge you in to mynde, for the grace that is youun to me of God,
Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine
16 that Y be the mynystre of Crist Jhesu among hethene men. And Y halewe the gospel of God, that the offryng of hethene men be acceptid, and halewid in the Hooli Goost.
kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.
17 Therfor Y haue glorie in Crist Jhesu to God.
Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga.
18 For Y dar not speke ony thing of tho thingis, whiche Crist doith not bi me, in to obedience of hethene men, in word and dedis,
Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita
19 in vertu of tokenes and grete wondris, in vertu of the Hooli Goost, so that fro Jerusalem bi cumpas to the Illirik see Y haue fillid the gospel of Crist.
mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu.
20 And so Y haue prechid this gospel, not where Crist was named, lest Y bilde vpon anotheres ground, but as it is writun,
Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake.
21 For to whom it is not teld of him, thei schulen se, and thei that herden not, schulen vndurstonde.
Koma monga kwalembedwa kuti, “Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona, ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”
22 For which thing Y was lettid ful myche to come to you, and Y am lettid to this tyme.
Ichi nʼchifukwa chake ine ndakhala ndikuletsedwa kawirikawiri kubwera kwa inu.
23 And now Y haue not ferthere place in these cuntrees, but Y haue desire to come to you, of many yeris that ben passid.
Koma tsopano popeza kulibenso malo anga woti ndigwire ntchito mʼmadera awa, ndakhala ndikufuna kukuonani kwa zaka zambiri.
24 Whanne Y bygynne to passe in to Spayne, Y hope that in my goyng Y schal se you, and of you Y schal be led thidur, if Y vse you first in parti.
Ine ndikukonza kuti nditero pamene ndipita ku Spaniya. Ine ndikuyembekeza kudzakuchezerani pamene ndikudutsa ndi kuti inu mudzathandize popitiriza ulendo wanga, nditasangalala ndi kukhala nanu kwa kanthawi.
25 Therfor now Y schal passe forth to Jerusalem, to mynystre to seyntis.
Koma tsopano, ine ndili pa ulendo wopita ku Yerusalemu potumikira oyera mtima akumeneko.
26 For Macedonye and Acaie han assaied to make sum yifte to pore men of seyntis, that ben in Jerusalem.
Pakuti kunakomera a ku Makedoniya ndi a ku Akaya kupereka thandizo kwa osauka pakati pa oyera mtima mu Yerusalemu.
27 For it pleside to hem, and thei ben dettouris of hem; for hethene men ben maad parteneris of her goostli thingis, thei owen also in fleischli thingis to mynystre to hem.
Iwo chinawakomera kuchita ichi, ndipo ndithu anali ndi ngongole kwa iwo. Pakuti ngati a mitundu ina anagawana ndi Ayuda madalitso auzimu, iwo ali ndi ngongole kwa Ayuda kuti agawane nawo madalitso awo a ku thupi.
28 Therfor whanne Y haue endid this thing, and haue asigned to hem this fruyt, Y schal passe bi you in to Spayne.
Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya.
29 And Y woot, that Y comynge to you, schal come `in to the abundaunce of the blessing of Crist.
Ine ndikudziwa kuti pamene ndidzabwera kwa inu, ndidzafika ndili wodzaza ndi madalitso a Khristu.
30 Therfor, britheren, Y biseche you bi oure Lord Jhesu Crist, and bi charite of the Hooli Goost, that ye helpe me in youre preyeris to the Lord,
Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu.
31 that Y be delyuerid fro the vnfeithful men, that ben in Judee, and that the offryng of my seruyce be acceptid in Jerusalem to seyntis;
Pempherani kuti ine ndilanditsidwe kwa osakhulupirira a ku Yudeya ndi kuti utumiki wanga mu Yerusalemu ukhale ovomerezeka ndi oyera mtima.
32 that Y come to you in ioye, bi the wille of God, and that Y be refreischid with you.
Kuti mwachifuniro cha Mulungu ndibwere kwa inu ndi chimwemwe kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu.
33 And God of pees be with you alle. Amen.
Mulungu wamtendere akhale ndi inu nonse. Ameni.

< Romans 15 >