< Revelation 6 >

1 And Y sai, that the lomb hadde openyd oon of the seuene seelis. And Y herde oon of the foure beestis seiynge, as a vois of thundur, Come, and se.
Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!”
2 And Y sai, and lo! a white hors; and he that sat on hym hadde a bouwe, and a coroun was youun to hym. And he wente out ouercomynge, that he schulde ouercome.
Nditayangʼana patsogolo pake ndinaona kavalo woyera! Wokwerapo wake anali ndi uta ndipo anapatsidwa chipewa chaufumu, ndipo anatuluka kupita kukagonjetsa anthu ena.
3 And whanne he hadde openyd the secounde seel, I herde the secounde beest seiynge, Come `thou, and se.
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!”
4 And another reed hors wente out; and it was youun to hym that sat on hym, that he schulde take pees fro the erthe, and that thei sle to gidere hem silf; and a greet swerd was youun to hym.
Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.
5 And whanne he hadde openyd the thridde seel, Y herde the thridde beest seiynge, Come thou, and se. And lo! a blak hors; and he that sat on hym hadde a balaunce in his hond.
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake.
6 And Y herde `as a vois in the myddil of the foure beestis, seiynge, A bilibre of wheete for a peny, and thre bilibris of barli for a peny; and hirte thou not wyn, ne oile.
Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!”
7 And whanne he hadde openyd the fourthe seel, Y herde a vois of the `foure beestis, seiynge, Come thou, and se.
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!”
8 And lo! a pale hors; and the name was Deth to hym that sat on hym, and helle suede hym. And power was youun to hym on foure partis of the erthe, for to sle with swerd, and with hungur, and with deth, and with beestis of the erthe. (Hadēs g86)
Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi. (Hadēs g86)
9 And whanne he hadde opened the fyuethe seel, Y say vndur the auter the soulis of men slayn for the word of God, and for the witnessing that thei hadden.
Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni.
10 And thei crieden with a geet vois, and seiden, Hou long thou, Lord, that art hooli and trewe, demest not, and vengest not oure blood of these that dwellen in the erthe?
Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”
11 And white stoolis, for ech soule a stoole, weren youun to hem; and it was seide to hem, that thei schulden reste yit a litil tyme, til the noumbre of her felowis and of her britheren ben fulfillid, that ben to be slayn, as also thei.
Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.
12 And Y say, whanne he hadde openyd the sixte seel, and lo! a greet erthe mouyng was maad; and the sunne was maad blak, as a sak of heire, and al the moone was maad as blood.
Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi,
13 And the sterris of heuene felden doun on the erthe, as a fige tre sendith his vnripe figis, whanne it is mouyd of a greet wynd.
ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba.
14 And heuene wente awei, as a book wlappid in; and alle munteyns and ilis weren mouyd fro her placis.
Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake.
15 And kingis of the erthe, and princis, and tribunes, and riche, and stronge, and ech bonde man, and freman, hidden hem in dennys and stoonys of hillis.
Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri.
16 And thei seien to hillis and to stoonys, Falle ye on vs, and hide ye vs fro the face of hym that sittith on the trone, and fro the wrath of the lomb;
Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa!
17 for the greet dai of her wraththe cometh, and who schal mowe stonde?
Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika ndipo ndi ndani angathe kulimbapo?”

< Revelation 6 >