< Isaiah 50 >
1 The Lord seith these thingis, What is this book of forsakyng of youre modir, bi which Y lefte her? ether who is he, to whom Y owe, to whom Y seeld you? For lo! ye ben seeld for youre wickidnessis, and for youre grete trespassis Y lefte youre modir.
Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
2 For Y cam, and no man was; Y clepide, and noon was that herde. Whether myn hond is abreggid, and maad litil, that Y mai not ayenbie? ether vertu is not in me for to delyuere? Lo! in my blamyng Y schal make the see forsakun, `ether desert, Y schal sette floodis in the drie place; fischis without watir schulen wexe rotun, and schulen dye for thirst.
Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu? Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha? Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani? Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani? Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu, mitsinje ndinayisandutsa chipululu; nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi; ndipo zinafa ndi ludzu.
3 Y schal clothe heuenes with derknessis, and Y schal sette a sak the hilyng of tho.
Ndinaphimba thambo ndi mdima ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
4 The Lord yaf to me a lerned tunge, that Y kunne susteyne hym bi word that failide; erli the fadir reisith, erli he reisith an eere to me, that Y here as a maister.
Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka. Mmawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
5 The Lord God openede an eere to me; forsothe Y ayenseie not, Y yede not abak.
Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga, ndipo sindinakhale munthu wowukira ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
6 I yaf my bodi to smyteris, and my chekis to pulleris; Y turnede not a wei my face fro men blamynge, and spetynge on me.
Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
7 The Lord God is myn helpere, and therfor Y am not schent; therfor Y haue set my face as a stoon maad hard, and Y woot that Y schal not be schent.
Popeza Ambuye Yehova amandithandiza, sindidzachita manyazi. Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi, chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
8 He is niy, that iustifieth me; who ayenseith me? stonde we togidere. Who is myn aduersarie? neiye he to me.
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso amene adzandiyimba mlandu? Abwere kuti tionane maso ndi maso! Mdani wanga ndi ndani? Abweretu kuti tilimbane!
9 Lo! the Lord God is myn helpere; who therfor is he that condempneth me? Lo! alle schulen be defoulid as a cloth, and a mouyte schal ete hem.
Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza. Ndaninso amene adzanditsutsa? Onse adzatha ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
10 Who of you dredith the Lord, and herith the vois of his seruaunt? Who yede in dercnessis and liyt is not to hym, hope he in the name of the Lord, and triste he on his God.
Ndani mwa inu amaopa Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, popanda chomuwunikira, iye akhulupirire dzina la Yehova ndi kudalira Mulungu wake.
11 Lo! alle ye kyndlynge fier, and gird with flawmes, go in the liyt of youre fier, and in the flawmes whiche ye han kyndlid to you. This is maad of myn hond to you, ye schulen slepe in sorewis.
Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu, lowani mʼmoto wanu womwewo. Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa. Ndipo ine Yehova ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.