< Hebrews 9 >

1 And the former testament hadde iustefiyngis of worschip, and hooli thing duringe for a tyme.
Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
2 For the tabernacle was maad first, in which weren candilstikis, and boord, and setting forth of looues, which is seid hooli.
Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.
3 And after the veil, the secounde tabernacle, that is seid sancta sanctorum, that is, hooli of hooli thingis;
Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri.
4 hauynge a goldun cenrer, and the arke of the testament, keuered aboute on ech side with gold, in which was a pot of gold hauynge manna, and the yerde of Aaron that florischide, and the tablis of the testament;
Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.
5 on whiche thingis weren cherubyns of glorie, ouerschadewinge the propiciatorie; of whiche thingis it is not now to seie bi alle.
Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
6 But whanne these weren maad thus togidere, preestis entriden eueremore in the formere tabernacle, doynge the offices of sacrifices; but in the secounde tabernacle,
Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo.
7 the bischop entride onys in the yeer, not without blood, which he offride for his ignoraunce and the puplis.
Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira.
8 For the Hooli Goost signefiede this thing, that not yit the weie of seyntis was openyd, while the formere tabernacle hadde staat.
Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.
9 Which parable is of this present tyme, bi which also yiftis and sacrifices ben offrid, whiche moun not make a man seruynge perfit bi conscience, oneli in metis,
Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo.
10 and drynkis, and dyuerse waischingis, and riytwisnessis of fleisch, that weren sett to the tyme of correccioun.
Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
11 But Crist beynge a bischop of goodis to comynge, entride bi a largere and perfitere tabernacle, not maad bi hoond, that is to seye,
Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.
12 not of this makyng, nether bi blood of goot buckis, or of calues, but bi his owne blood, entride onys in to the hooli thingis, that weren foundun bi an euerlastinge redempcioun. (aiōnios g166)
Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. (aiōnios g166)
13 For if the blood of gootbuckis, and of boolis, and the aische of a cow calf spreynd, halewith vnclene men to the clensing of fleisch,
Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi,
14 hou myche more the blood of Crist, which bi the Hooli Goost offride hym silf vnwemmyd to God, schal clense oure conscience fro deed werkis, to serue God that lyueth? (aiōnios g166)
nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo. (aiōnios g166)
15 And therfor he is a mediatour of the newe testament, that bi deth fallinge bitwixe, in to redempcioun of tho trespassyngis that weren vndur the formere testament, thei that ben clepid take the biheest of euerlastinge eritage. (aiōnios g166)
Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija. (aiōnios g166)
16 For where a testament is, it is nede, that the deth of the testament makere come bitwixe.
Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi,
17 For a testament is confermed in deed men; ellis it is not worthe, while he lyueth, that made the testament.
chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo.
18 Wherfor nether the firste testament was halewid without blood.
Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi.
19 For whanne ech maundement of the lawe was red of Moises to al the puple, he took the blood of calues, and of buckis of geet, with watir, and reed wolle, and ysope, and bispreynde bothe thilke book and al the puple,
Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.
20 and seide, This is the blood of the testament, that God comaundide to you.
Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.”
21 Also he spreynde with blood the tabernacle, and alle the vessels of the seruyce in lijk maner.
Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo.
22 And almest alle thingis ben clensid in blood bi the lawe; and without scheding of blood remyssioun of synnes is not maad.
Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.
23 Therfor it is nede, that the saumpleris of heuenli thingis be clensid with these thingis; but thilke heuenli thingis with betere sacrificis than these.
Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
24 For Jhesus entride not in to hooli thingis maad bi hoondis, that ben saumpleris of very thingis, but in to heuene it silf, that he appere now to the cheer of God for vs;
Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
25 nether that he offre him silf ofte, as the bischop entride in to hooli thingis bi alle yeeris in alien blood,
Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
26 ellis it bihofte hym to suffre ofte fro the bigynnyng of the world; but now onys in the ending of worldis, to distruccioun of synne bi his sacrifice he apperide. (aiōn g165)
Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. (aiōn g165)
27 And as it is ordeynede to men, onys to die, but aftir this is the dom,
Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
28 so Crist was offrid onys, to auoyde the synnes of many men; the secounde tyme he schal appere with outen synne to men that abiden him in to heelthe.
momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

< Hebrews 9 >