< Mark 3 >
1 And He went another time into a synagogue, where there was a man that had a withered hand:
Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo.
2 and they watched Him, whether He would heal him on the sabbath-day, that they might accuse Him.
Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata.
3 And He said to the man, that had the withered hand, Rise up into the midst:
Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”
4 then saith He to them, Is it lawful to do good on the sabbath, or to do evil? to save life, or to kill? but they were silent.
Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
5 And when He had looked round upon them with indignation, being grieved at the hardness of their hearts, He saith to the man, Stretch out thine hand: and he stretched it out, and his hand was made as sound as the other.
Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira.
6 And the pharisees went out, and immediately took counsel with the Herodians against Him, how to destroy Him:
Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.
7 but Jesus withdrew with his disciples to the sea.
Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata.
8 And a great multitude from Galilee followed Him, and from Judea, and from Jerusalem, and from Idumea, and from beyond Jordan; and those about Tyre and Sidon, a great number, hearing how great things He did, came unto Him.
Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni.
9 Therefore He spake to his disciples, that there might be a small vessel attending Him, because of the multitude, least they should throng Him: for He had healed many,
Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize.
10 so that whoever had any maladies, crouded upon Him to touch Him.
Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze.
11 And impure spirits, when they saw Him, fell down before Him, and cried out, saying, Thou art the Son of God:
Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!”
12 but He strictly charged them not to make Him known.
Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
13 Then going up into a mountain, He calleth for such as He saw fit, and they came to Him:
Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye.
14 and He appointed twelve to be with Him, and that He might send them forth to preach the gospel,
Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira
15 and to have power to heal diseases, and to cast out demons;
ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda.
16 even Simon, whom He surnamed Peter,
Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro);
17 and James the Son of Zebedee, and John the brother of James, (and He surnamed them Boanerges, which is to say, Sons of thunder, ) and Andrew,
Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu);
18 and Philip, and Bartholomew, and Matthew, and Thomas, and James the son of Alpheus, and Thaddeus,
Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote,
19 and Simon the Canaanite, and Judas Iscariot, even him who betrayed Him.
ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
20 And they went into a house, and the multitude came together again, so that they could not so much as eat.
Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye.
21 And when his friends heard of it, they went out to lay hold on Him; for they said He spends Himself too much.
Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
22 And the scribes that came down from Jerusalem said, He is in league with Beelzebub, and casts out demons by the help of the prince of demons.
Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
23 So He called them to Him, and said unto them in parables, How can Satan cast out Satan?
Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana?
24 If a kingdom be divided against itself, that kingdom cannot stand:
Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse.
25 and if a family be divided against itself, that family cannot stand: and if Satan oppose himself and be divided,
Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima.
26 he cannot stand, but his kingdom is at an end.
Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha.
27 No one can enter into the house of a strong man, and plunder his goods; unless he first bind the strong man, and then he may pillage his house.
Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera.
28 Verily I tell you, that all sins shall be forgiven to the sons of men, and blasphemies wherewith they may blaspheme:
Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa,
29 but whosoever blasphemeth against the holy Ghost never hath forgiveness, but is liable to eternal damnation: (aiōn , aiōnios )
koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.” (aiōn , aiōnios )
30 for they said, He hath an impure spirit.
Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
31 So his brethren and his mother came, and standing without sent to Him to call Him to them:
Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye.
32 and there was a multitude sitting about Him, and they said to Him, Behold, thy mother and thy brethren are without inquiring for thee.
Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
33 And He answered them, and said, Who is my mother, or my brethren?
Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”
34 And looking round on those that sat about Him, He said, Behold my mother, and my brethren:
Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga!
35 for whosoever doth the will of God, he is to me as my brother, my sister, and mother.
Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”