< John 2 >

1 Two days later there was a wedding at Cana in Galilee, and the mother of Jesus was there,
Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko,
2 and Jesus also was invited and His disciples.
ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo.
3 Now the wine ran short; whereupon the mother of Jesus said to Him, "They have no wine."
Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
4 "Leave the matter in my hands," He replied; "the time for me to act has not yet come."
Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
5 His mother said to the attendants, "Whatever he tells you to do, do it."
Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
6 Now there were six stone jars standing there (in accordance with the Jewish regulations for purification), each large enough to hold twenty gallons or more.
Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
7 Jesus said to the attendants, "Fill the jars with water." And they filled them to the brim.
Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
8 Then He said, "Now, take some out, and carry it to the President of the feast."
Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.” Iwo anachita momwemo.
9 So they carried some to him. And no sooner had the President tasted the water now turned into wine, than--not knowing where it came from, though the attendants who had drawn the water knew--he called to the bridegroom
Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali
10 and said to him, "It is usual to put on the good wine first, and when people have drunk freely, then that which is inferior. But you have kept the good wine till now."
ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
11 This, the first of His miracles, Jesus performed at Cana in Galilee, and thus displayed His glorious power; and His disciples believed in Him.
Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
12 Afterwards He went down to Capernaum--He, and His mother, and His brothers, and His disciples; and they made a short stay there.
Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 But the Jewish Passover was approaching, and for this Jesus went up to Jerusalem.
Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu.
14 And He found in the Temple the dealers in cattle and sheep and in pigeons, and the money-changers sitting there.
Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.
15 So He plaited a whip of rushes, and drove all--both sheep and bullocks--out of the Temple. The small coin of the brokers He upset on the ground and overturned their tables.
Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo.
16 And to the pigeon-dealers He said, "Take these things away. Do not turn my Father's house into a market."
Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
17 This recalled to His disciples the words of Scripture, "My zeal for Thy House will consume me."
Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
18 So the Jews asked Him, "What proof of your authority do you exhibit to us, seeing that you do these things?"
Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
19 "Demolish this Sanctuary," said Jesus, "and in three days I will rebuild it."
Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
20 "It has taken forty-six years," replied the Jews, "to build this Sanctuary, and will you rebuild it in three days?"
Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?”
21 But He was speaking of the Sanctuary of His body.
Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.
22 When however He had risen from among the dead, His disciples recollected that He had said this; and they believed the Scripture and the teaching which Jesus had given them.
Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
23 Now when He was in Jerusalem, at the Festival of the Passover, many became believers in Him through watching the miracles He performed.
Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake.
24 But for His part, Jesus did not trust Himself to them, because He knew them all,
Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse.
25 and did not need any one's testimony concerning a man, for He of Himself knew what was in the man.
Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.

< John 2 >