< Zechariah 3 >

1 And he showed me Joshua the high priest standing before the angel of the LORD, and Satan standing at his right hand to resist him.
Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye.
2 And the LORD said to Satan, The LORD rebuke thee, O Satan; even the LORD that hath chosen Jerusalem rebuke thee: [is] not this a brand plucked out of the fire?
Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”
3 Now Joshua was clothed with filthy garments, and stood before the angel.
Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo.
4 And he answered and spoke to those that stood before him, saying, Take away the filthy garments from him. And to him he said, Behold, I have caused thy iniquity to pass from thee, and I will clothe thee with change of raiment.
Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, “Muvuleni zovala zake zalitsirizo.” Kenaka anawuza Yoswa kuti, “Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola.”
5 And I said, Let them set a fair miter upon his head. So they set a fair miter upon his head, and clothed him with garments. And the angel of the LORD stood by.
Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.
6 And the angel of the LORD protested to Joshua, saying,
Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti,
7 Thus saith the LORD of hosts; If thou wilt walk in my ways, and if thou wilt keep my charge, then thou shalt also judge my house, and shalt also keep my courts, and I will give thee places to walk among these that stand by.
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.
8 Hear now, O Joshua the high priest, thou and thy fellows that sit before thee: for they [are] men wondered at: for behold, I will bring forth my servant the BRANCH.
“‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi.
9 For behold, the stone that I have laid before Joshua; upon one stone [shall be] seven eyes; behold, I will engrave the graving of it saith the LORD of hosts, and I will remove the iniquity of that land in one day.
Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.
10 In that day, saith the LORD of hosts, shall ye call every man his neighbor under the vine and under the fig-tree.
“‘Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

< Zechariah 3 >