< Romans 13 >

1 Let every soul be subject to the higher powers. For there is no power but from God: the powers that are, are ordained by God.
Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu.
2 Whoever therefore resisteth the power, resisteth the ordinance of God: and they that resist shall receive to themselves damnation.
Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango.
3 For rulers are not a terror to good works, but to the evil. Wilt thou then not be afraid of the power; do that which is good, and thou shalt have praise from the same:
Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani.
4 For he is the minister of God to thee for good. But if thou doest that which is evil, be afraid; for he beareth not the sword in vain: for he is the minister of God, an avenger to [execute] wrath upon him that doeth evil.
Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa.
5 Wherefore [ye] must needs be subject, not only for wrath, but also for conscience sake.
Nʼchifukwa chake ndi koyenera kugonjera olamulira, osati chifukwa choopa kulangidwa kokha komanso chifukwa cha chikumbumtima.
6 For, for this cause ye pay tribute also: for they are God's ministers, attending continually upon this very thing.
Ichi nʼchifukwa chakenso inu mumapereka msonkho. Pakuti olamulira ndi atumiki a Mulungu amene amapereka nthawi yawo yonse kulamulira.
7 Render therefore to all their dues: tribute to whom tribute [is due]; custom to whom custom; fear to whom fear; honor to whom honor.
Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.
8 Owe no man any thing, but to love one another: for he that loveth another hath fulfilled the law.
Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.
9 For this, Thou shalt not commit adultery, Thou shalt not kill, Thou shalt not steal, Thou shalt not bear false witness, Thou shalt not covet; and if [there is] any other commandment, it is briefly comprehended in this saying, namely, Thou shalt love thy neighbor as thyself.
Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”
10 Love worketh no ill to one's neighbor: therefore love [is] the fulfilling of the law.
Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.
11 And this, knowing the time, that now [it is] high time to awake out of sleep: for now [is] our salvation nearer than when we believed.
Ndipo chitani ichi pozindikira nthawi ino. Nthawi yafika yoti inu mudzuke kutulo, chifukwa chipulumutso chathu chili pafupi tsopano kuposa pamene tinayamba kukhulupirira.
12 The night is far spent, the day is at hand: let us therefore cast off the works of darkness, and let us put on the armor of light.
Usiku watsala pafupifupi kutha. Kwatsala pangʼono kucha. Tiyeni tsono tichotse ntchito zamdima ndipo tivale chovala chakuwunika.
13 Let us walk honestly, as in the day; not in rioting and drunkenness, not in chambering and wantonness, not in strife and envying.
Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje.
14 But put ye on the Lord Jesus Christ, and make not provision for the lusts of flesh.
Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.

< Romans 13 >