< Psalms 52 >
1 For the chief musician. A maschil of David; when Doeg the Edomite came and told Saul, and said to him, “David has come to the house of Ahimelech.” Why are you proud of making trouble, you mighty man? The covenant faithfulness of God comes every day.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.” Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
2 Your tongue plans destruction like a sharp razor, working deceitfully.
Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena; lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nʼkunyenga.
3 You love evil more than good and lying rather than speaking righteousness. (Selah)
Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. (Sela)
4 You love all words that devour others, you deceitful tongue.
Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo!
5 God will likewise destroy you forever; he will take you up and pluck you out of your tent and root you out of the land of the living. (Selah)
Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
6 The righteous will also see it and fear; they will laugh at him and say,
Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,
7 “See, this is a man who did not make God his refuge, but he trusted in the abundance of his wealth, and he was strong when he destroyed others.”
“Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”
8 But as for me, I am like a green olive tree in God's house; I will trust in the covenant faithfulness of God forever and ever.
Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.
9 I will give you thanks forever for what you have done. I will wait for your name, because it is good, in the presence of your godly people.
Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.