< Ezekiel 28 >

1 And the word of Yahweh came unto me, saying
Yehova anandiyankhula nati:
2 Son of man Say to the Prince of Tyre. Thus, saith My Lord. Yahweh— Because lofty, is thy heart and thou hast said A GOD, am I, In the seat of God, have I taken my seat In the heart of the seas; Whereas thou art a man, and not a GOD, But hast set thy heart as the heart of God:
“Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu; ndimakhala pa mpando wa mulungu pakati pa nyanja.’ Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu, ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
3 Lo! wiser, thou than Daniel, — No secret, have they hidden from thee:
Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli. Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
4 In thy wisdom and in thine understanding, hast thou gotten thee wealth, — And hast gotten gold and silver into thy treasuries:
Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako unadzipezera chuma ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zosungira chuma chako.
5 By the greatness of thy wisdom and by thy traffic, hast thou multiplied thy riches, -And thy heart hath become lofty in thy riches:
Ndi nzeru zako zochitira malonda unachulukitsa chuma chako ndipo wayamba kunyada chifukwa cha chuma chakocho.
6 Therefore, Thus saith My Lord Yahweh, — Because thou hast set thy heart as the heart of God,
“‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Popeza umadziganizira kuti ndiwe mulungu,
7 Therefore behold me! bringing upon thee aliens, The terrible ones of the nations, - And they shall unsheathe their swords over the beauty of thy wisdom, And profane thy splendour:
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza, kuti adzalimbane nawe. Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako, ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
8 To the pit, shall they take thee down, - And thou shalt die the deaths of one thrust through, In the heart of the seas.
Iwo adzakuponyera ku dzenje ndipo udzafa imfa yoopsa mʼnyanja yozama.
9 Wilt thou really say, God, am I, before him who is slaying thee; When, thou, art a man and not a God, in the hand of them who are piercing thee?
Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’ pamaso pa iwo amene akukupha? Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu, mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
10 The deaths of the uncircumcised, shalt thou die by the hand of aliens, — For I have spoken, Declareth My Lord Yahweh.
Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe mʼmanja mwa anthu achilendo. Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’”
11 And the word of Yahweh came unto me, saying:
Yehova anandiyankhula kuti:
12 Son of man Take thou up a dirge over the king of Tyre, — And thou shalt say to him Thus saith My Lord. Yahweh, Thou wast of finished proportions, Full of wisdom and Perfect in beauty:
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni, wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
13 In Eden the garden of God, thou wast. Of every precious stone, was thy covering-Sardius. topaz, and diamond, Chrysolite beryl, and jasper, Sapphire carbuncle and emerald, - And of gold, was the work of thy timbrels and thy flutes within thee, In the day thou wast created, were they prepared:
Iwe unkakhala ngati mu Edeni, munda wa Mulungu. Miyala yokongola ya mitundu yonse: rubi, topazi ndi dayimondi, kirisoliti, onikisi, yasipa, safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako. Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide. Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
14 Thou, wast the anointed cherub that covered, — When I appointed thee, in the holy mount of God, thou wast, Amid stones of fire, thou didst walk to and fro:
Ndinayika kerubi kuti azikulondera. Unkakhala pa phiri langa lopatulika, ndipo unkayendayenda pakati pa miyala ya moto.
15 Complete, wast thou in thy ways, from the day thou wast created, - Until perversity was found in thee.
Makhalidwe ako anali abwino kuyambira pamene unalengedwa mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
16 By the abundance of thy traffic, they filled thy midst with violence And thou didst sin, - So I cast thee as profane out of the mountain of God. And destroyed thee O covering cherub, from amid the stones of fire:
Unatanganidwa ndi zamalonda. Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu ndi kumachimwa. Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa kukuchotsa ku miyala yamoto.
17 Lofty, was thy heart in thy beauty, Thou didst corrupt thy wisdom, because of thy splendour, — Upon the earth, did I cast thee. Before kings, did I set thee That they might look at thee:
Unkadzikuza mu mtima mwako chifukwa cha kukongola kwako, ndipo unayipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kutchuka. Kotero Ine ndinakugwetsa pansi kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18 Owing to the abounding of thine iniquities. In the perversity of thy traffic, Thou didst profane thy sanctuaries, Therefore brought I forth fire out of thy midst. the same devoured thee, And I turned thee to ashes on the ground, Before the eyes of all beholding thee:
Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako. Motero unayipitsa malo ako achipembedzo. Choncho ndinabutsa moto pakati pako, ndipo unakupsereza, ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi pamaso pa anthu onse amene amakuona.
19 All that had known thee among the peoples were astounded over thee, — A terror, hast thou become, And, art not, Unto times age-abiding.
Anthu onse amitundu amene ankakudziwa akuchita mantha chifukwa cha iwe. Watheratu mochititsa mantha ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’”
20 And the word of Yahweh came unto me saying:
Yehova anandiyankhula nati:
21 Son of man, Set thy face towards Zidon, — And prophesy over it;
“Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti,
22 and thou shalt say— Thus saith My Lord. Yahweh, Behold me! against thee, O Zidon, Therefore will I get myself glory in thy midst, — [And they shall know that, I, am Yahweh, ] When I have executed against her judgments And hallowed myself in her.
‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe. Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti ndine woyera pakati pako.
23 So then I will send against her, pestilence and blood in her streets, And the wounded shall fall in her midst by the sword upon her from every side, — And they shall know that, I, am Yahweh.
Ndidzatumiza mliri pa iwe ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako. Anthu ophedwa ndi lupanga adzagwa mbali zonse. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
24 And the house of Israel shall no more have a stinging prickle or a wounding thorn, of any round about them who used to despise them, - So shall they know that, I, am The Lord Yahweh.
“‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25 Thus saith My Lord, Yahweh, When I gather together the house of Israel, from the midst of the peoples among whom they have been scattered, and shall hallow myself in them before the eyes of the nations Then shall they dwell upon their own soil, which I gave to my servant—to Jacob:
“‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo.
26 Yea they shall dwell thereupon securely, Yea shall build houses, and plant vineyards, and dwell securely, — When I have executed judgments on all that despised them on every side of them, So shall they know that, I, Yahweh am their God
Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’”

< Ezekiel 28 >