< Mark 6 >

1 And he went out from thence, and cometh into his own country; and his disciples follow him.
Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake.
2 And when the sabbath was come, he began to teach in the synagogue. And most people when they heard him were astonished, saying, Whence hath this man these things? And what is the wisdom which is given him? And how is it that such miracles are wrought by his hands?
Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa. Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa!
3 Is not this the carpenter, the son of Mary, and brother of James, and Joses, and Judah, and Simon? And are not his sisters here with us? And they took offence at him.
Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.
4 And Jesus said to them, A prophet is not without honor except in his own country, and among his own kindred, and in his own house.
Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.”
5 And he could not do any miracle there, except that he laid his hand upon a few sick persons, and cured them.
Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa.
6 And he wondered at their want of faith. And he went about the surrounding villages teaching.
Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo. Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa.
7 And he calleth to him the twelve, and began to send them forth by two and two; and gave them power over the unclean spirits;
Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.
8 and commanded them that they should take nothing for the way but a staff only; no bread, no bag, no money in their girdle;
Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama.
9 but to be shod with sandals; and, Do not put on two coats.
Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera.
10 And he said to them, Wherever ye enter a house, there abide fill ye leave that place.
Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo.
11 And whatever place shall not receive you, nor hear you, when ye go thence, shake off the dust under your feet as a testimony to them.
Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”
12 And they went out and preached that men should repent;
Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima.
13 and they cast out many demons, and anointed with oil many sick persons, and healed them.
Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa.
14 And king Herod heard of him (for his name was spread abroad), and he said, John the Baptizer hath risen from the dead, and therefore do these powers work in him. But others said, It is Elijah.
Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”
15 And others said, It is a prophet, as one of the prophets.
Ena anati, “Iye ndi Eliya.” Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.”
16 But Herod hearing of it said, John, whom I beheaded, hath risen again.
Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.”
17 For Herod himself had sent forth and seized John, and bound him in prison, on account of Herodias, his brother Philip's wife; for he had married her.
Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira.
18 For John had said to Herod, It is not lawful for thee to have thy brother's wife.
Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.”
19 And Herodias was enraged against him, and wished to put him to death, but could not.
Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero,
20 For Herod feared John, knowing that he was a righteous and holy man, and was regardful of him; and on hearing him, was in much anxiety, and listened to him gladly.
chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera.
21 And a convenient day having come, when Herod on his birthday made a supper for his nobles and chief captains and the principal men of Galilee,
Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya.
22 and the daughter of Herodias came in and danced, she pleased Herod and those at table with him; and the king said to the damsel, Ask of me whatever thou wilt, and I will give it thee.
Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo. Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.”
23 And he swore to her, Whatever thou shalt ask of me, I will give thee, to the half of my kingdom.
Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.”
24 And she went out and said to her mother, What shall I ask? And she said, The head of John the Baptizer.
Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?” Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.”
25 And she came in immediately with haste to the king, and asked, saying, I desire that thou wilt give me immediately on a platter the head of John the Baptist.
Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
26 And the king was exceedingly sorry; but on account of his oaths, and of those at table with him, he would not refuse her.
Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza.
27 And the king immediately sent one of his guards, and ordered his head to be brought. And he went and beheaded him in the prison,
Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende,
28 and brought his head on a platter, and gave it to the damsel; and the damsel gave it to her mother.
nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake.
29 And his disciples, when they heard of it, came and took up his body, and laid it in a tomb.
Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda.
30 And the apostles gather together to Jesus, and told him all which they had done and taught.
Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa.
31 And he saith to them, Come ye by yourselves apart into a desert place, and rest a while. For there were many coming and going; and they had no leisure, even to eat.
Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”
32 And they went away into a desert place in the boat apart.
Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha.
33 And many saw them departing, and knew them, and ran together on foot thither from all the cities, and arrived before them.
Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika.
34 And when he came forth, he saw a great multitude, and was moved with compassion for them, because they were as sheep not having a shepherd; and he began to teach them many things.
Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
35 And late in the day his disciples came to him, and said, This is a desert place, and it is now late;
Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo.
36 send them away, that they may go into the surrounding fields and villages, and buy themselves something to eat.
Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”
37 But he answering said to them, Give ye them to eat. And they say to him, Shall we go and buy two hundred denaries' worth of bread, and give them to eat?
Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.” Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”
38 He saith to them, How many loaves have ye? Go and see. And when they knew, they say, Five, and two fishes.
Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.” Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”
39 And he ordered them to make all lie down in companies upon the green grass.
Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira.
40 And they lay down in ranks, by hundreds, and by fifties.
Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu.
41 And taking the five loaves and the two fishes, he looked up to heaven and blessed, and broke the loaves, and gave them to the disciples to set before them; and the two fishes he divided among them all.
Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse.
42 And they all ate, and were filled.
Onse anadya ndipo anakhuta,
43 And they took up twelve baskets full of the fragments, and of the fishes.
ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri.
44 And they who ate of the loaves were five thousand men.
Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.
45 And he immediately constrained his disciples to get into the boat, and to go before to the other side to Bethsaida, while he sent the multitude away.
Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita.
46 And when he had taken leave of them, he went away into the mountain to pray.
Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.
47 And when evening came, the boat was in the midst of the lake; and he was alone on the land.
Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda.
48 And when he saw them toiling hard in rowing, for the wind was against them, about the fourth watch of the night he cometh to them, walking upon the lake. And he would have passed by them;
Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira,
49 but they, seeing him walking upon the lake, thought it was a spectre, and cried out.
koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula,
50 For they all saw him, and were terrified. But he immediately spoke with them, and saith to them, Be of good cheer; it is I, be not afraid.
pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha. Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.”
51 And he went up to them into the boat, and the wind ceased. And they were exceedingly astonished, beyond measure.
Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri,
52 For they did not consider the matter of the loaves; but their heart was hardened.
popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.
53 And crossing over, they came to land, to Gennesaret; and anchored there.
Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko.
54 And when they had come out of the boat, the people immediately knowing who he was,
Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu.
55 ran through all that region, and began to carry about on beds those that were sick to the place where they heard he was.
Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye.
56 And wherever he entered into villages or cities or the open country, they laid the sick in the market-places, and besought him that they might touch if it were but the fringe of his garment; and as many as touched him were made well.
Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.

< Mark 6 >