< John 5 >
1 After these things there was the feast of the Jews, and Jesus went up to Jerusalem.
Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda.
2 Now there is at Jerusalem, by the sheep-gate, a pool, which is called in Hebrew Bethzatha, having five porches.
Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu.
3 In these were lying a multitude of diseased persons, blind, lame, withered.
Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo.
Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.
5 And a certain man was there, who had had his infirmity thirty-eight years.
Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38.
6 Jesus saw this man lying there, and knowing that he had been for a long time diseased, saith to him, Dost thou wish to be made well?
Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
7 The diseased man answered him, Sir, I have no man, when the water is troubled, to put me into the pool; but while I am coming, another goeth down before me.
Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
8 Jesus saith to him, Rise, take up thy bed, and walk.
Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.”
9 And immediately the man was made well, and took up his bed, and walked. And that day was the sabbath.
Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda. Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata.
10 The Jews therefore said to him that was cured, It is the sabbath; and it is not lawful for thee to take up the bed.
Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
11 He answered them, He that made me well, the same said to me, Take up thy bed, and walk. T
Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’”
12 hey asked him, Who is the man that said to thee, Take up, and walk?
Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’”
13 But the diseased man knew not who it was; for Jesus had withdrawn himself, there being a crowd in the place.
Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
14 Afterwards Jesus found him in the temple, and said to him, Behold, thou art made well; sin no more, lest something worse befall thee.
Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.”
15 The man went away, and told the Jews that it was Jesus who had made him well.
Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
16 And on this account the Jews persecuted Jesus, because he did these things on the sabbath.
Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda.
17 But he answered them, My Father is working up to this time, and I work.
Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.”
18 On this account the Jews sought the more to kill him, because he not only broke the sabbath, but also said that God was his own Father, making himself equal with God.
Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
19 Then answered Jesus and said to them, Truly, truly do I say to you, The Son can do nothing of himself, but what he seeth the Father doing; for whatever He doeth, these things the Son also doeth in like manner;
Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso.
20 for the Father loveth the Son, and showeth him all things which he himself doeth; and greater works than these will he show him, so that ye will wonder.
Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa.
21 For as the Father raiseth up the dead, and giveth them life, so the Son also giveth life to whom he will.
Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna.
22 For neither doth the Father judge any one, but hath committed all judgment to the Son;
Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo,
23 that all may honor the Son, as they honor the Father. He that honoreth not the Son, honoreth not the Father, who sent him.
kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
24 Truly, truly do I say to you, He that heareth my word, and believeth him that sent me, hath everlasting life, and cometh not into condemnation, but hath passed out of death into life. (aiōnios )
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. (aiōnios )
25 Truly, truly do I say to you, The hour is coming and now is, when the dead will hear the voice of the Son of God; and they that hear will live.
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.
26 For as the Father hath life in himself, so did he give to the Son also to have life in himself.
Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana.
27 And he gave him authority to execute judgment, because he is a son of man.
Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
28 Marvel not at this; for the hour is coming, in which all that are in the tombs will hear his voice,
“Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake
29 and will come forth, they that have done good, to a resurrection of life; they that have done evil, to a resurrection of condemnation.
ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.
30 I can of myself do nothing. As I hear, I judge; and my judgment is just, because I seek not my own will, but the will of him that sent me.
Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
31 If I bear witness of myself, my witness is not true.
“Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona.
32 There is another who beareth witness of me; and ye know that the witness which he witnesseth of me is true.
Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
33 Ye have sent to John, and he hath borne witness to the truth.
“Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona.
34 But the testimony which I receive is not from man; but these things I say, that ye may be saved.
Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe.
35 He was the burning and shining lamp: and ye were willing for a season to rejoice in his light.
Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
36 But the testimony which I have, is greater than that of John; for the works which the Father hath given me to perform, the works themselves which I do, bear witness of me, that the Father hath sent me.
“Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine.
37 And the Father who sent me, he hath borne witness of me. Ye have neither heard his voice at any time, nor seen his form.
Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake,
38 And ye have not his word abiding in you; for whom he sent, him ye believe not.
kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma.
39 Ye search the Scriptures, because ye yourselves think that in them ye have everlasting life; and it is they which testify of me; (aiōnios )
Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. (aiōnios )
40 and ye are not willing to come to me, that ye may have life.
Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41 I receive not honor from men;
“Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu
42 but I know you, that ye have not the love of God in you.
koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu.
43 I have come in my Father's name, and ye receive me not; if another come in his own name, him ye will receive.
Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira.
44 How can ye believe while ye receive honor from one another, and seek not the honor that is from him who alone is God?
Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
45 Do not think that I shall accuse you to the Father; there is one that accuseth you, even Moses, in whom ye have placed your hope.
“Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu.
46 For if ye believed Moses, ye would believe me; for he wrote of me.
Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine.
47 But if ye do not believe his writings, how will ye believe my words?
Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”