< 3 John 1 >
1 The elder to Gaius the beloved, whom I love in truth.
Ndine mkulu wampingo, kulembera: Gayo mnzanga wokondedwa, amene ndimamukonda mʼchoonadi.
2 Beloved, in all things I pray that thou mayst prosper and be in health, as thy soul prospereth.
Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.
3 For I rejoiced greatly, when brethren came and bore witness to thy truth, as thou walkest in truth.
Ine ndinali ndi chimwemwe chachikulu pamene abale ena anafika nʼkundifotokozera za kukhulupirika kwako pa choonadi ndiponso mmene umayendera motsata choonadi.
4 I have no greater joy than this, to hear that my children walk in the truth.
Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.
5 Beloved, thou doest a faithful thing whatever thou doest to the brethren, and that to strangers,
Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo.
6 who bore witness of thy love before the church; whom if thou send forward on their journey in a manner worthy of God, thou wilt do well.
Iwo anafotokozera mpingo za chikondi chako. Chonde uwathandize kupitiriza ulendo mʼnjira yokondweretsa Mulungu.
7 For in behalf of the Name they went forth, taking nothing of the gentiles.
Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira.
8 We therefore ought to sustain such persons, that we may be fellow-workers for the truth.
Ife tiyenera kumathandiza anthu oterewa, kuti tigwirizane nawo pa ntchito ya choonadi.
9 I wrote something to the church; but Diotrephes, who loveth to have the pre-eminence among them, receiveth us not.
Ndinalembera mpingo, koma Diotrefe, amene amafuna kukhala wotsogolera, sanafune kutimvera.
10 Wherefore, if I come, I will bring to remembrance his deeds which he doeth, prating against us with malicious words; and not content therewith, he himself doth not receive the brethren, and those that would he forbiddeth, and casteth them out of the church.
Tsono ndikabwera ndidzakumbutsa zimene iye amachita. Iye amafalitsa nkhani zabodza zonena ife. Ndipo sakhutira ndi zimenezo, komanso iyeyo amakana kulandira abale. Komanso amaletsa amene akufuna kutero, ndipo amawachotsa mu mpingo.
11 Beloved, do not imitate that which is evil, but that which is good. He that doeth good is of God; he that doeth evil hath not seen God.
Wokondedwa, usatsatire zinthu zoyipa koma zinthu zabwino. Aliyense amene amachita zinthu zabwino ndi wochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amachita zoyipa sanamuonepo Mulungu.
12 To Demetrius testimony hath been borne by all, and by the truth itself; yea, we also bear witness, and ye know that our witness is true.
Aliyense akumuchitira umboni wabwino wa Demetriyo. Ngakhale choona chomwe chimamuchitira umboni, ndipo iweyo ukudziwa kuti umboni wathu ndi woona.
13 I had many things to write to thee, but I do not wish to write to thee with ink and pen;
Ndili ndi zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata.
14 but I hope to see thee immediately, and we shall speak face to face. Peace be to thee. The friends salute thee. Salute the friends by name.
Ndiyembekezera kufika kwanuko posachedwapa, ndipo tidzakambirana pamaso ndi pamaso. Mtendere ukhale nawe. Abwenzi anu kuno akupereka moni. Upereke moni kwa abwenzi onse mmodzimmodzi.