< Numbers 28 >
1 YHWH spoke to Moses, saying,
Yehova anawuza Mose kuti,
2 "Command the children of Israel, and tell them, 'My offering, my food for my offerings made by fire, of a pleasant aroma to me, you shall observe to offer to me in their due season.'
“Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’
3 You shall tell them, 'This is the offering made by fire which you shall offer to YHWH: male lambs a year old without blemish, two day by day, for a continual burnt offering.
Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema.
4 You shall offer the one lamb in the morning, and you shall offer the other lamb at evening;
Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo.
5 with the tenth part of an ephah of fine flour for a meal offering, mixed with the fourth part of a hin of beaten oil.
Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi.
6 It is a continual burnt offering, which was ordained in Mount Sinai for a pleasant aroma, an offering made by fire to YHWH.
Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova.
7 Its drink offering shall be the fourth part of a hin for the one lamb. You shall pour out a drink offering of strong drink to YHWH in the holy place.
Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova.
8 The other lamb you shall offer at evening: as the meal offering of the morning, and as the drink offering of it, you shall offer it, an offering made by fire, of a pleasant aroma to YHWH.
Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’”
9 "'On the Sabbath day two male lambs a year old without blemish, and two tenth parts of an ephah of fine flour for a meal offering, mixed with oil, and the drink offering of it:
“‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.
10 this is the burnt offering of every Sabbath, besides the continual burnt offering, and the drink offering of it.
Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’”
11 "'In the beginnings of your months you shall offer a burnt offering to YHWH: two young bulls, and one ram, seven male lambs a year old without blemish;
“Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema.
12 and three tenth parts of an ephah of fine flour for a meal offering, mixed with oil, for each bull; and two tenth parts of fine flour for a meal offering, mixed with oil, for the one ram;
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta;
13 and a tenth part of fine flour mixed with oil for a meal offering to every lamb; for a burnt offering of a pleasant aroma, an offering made by fire to YHWH.
ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova.
14 Their drink offerings shall be half a hin of wine for a bull, and the third part of a hin for the ram, and the fourth part of a hin for a lamb: this is the burnt offering of every month throughout the months of the year.
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka.
15 One male goat for a sin offering to YHWH; it shall be offered besides the continual burnt offering, and the drink offering of it.
Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.
16 "'In the first month, on the fourteenth day of the month, is YHWH's Passover.
“‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova.
17 On the fifteenth day of this month shall be a feast: seven days shall unleavened bread be eaten.
Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri.
18 In the first day shall be a holy convocation: you shall do no servile work;
Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
19 but you shall offer an offering made by fire, a burnt offering to YHWH: two young bulls, and one ram, and seven male lambs a year old; they shall be to you without blemish;
Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema.
20 and their meal offering, fine flour mixed with oil: you shall offer three tenth parts for a bull, and two tenth parts for the ram.
Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse.
21 You shall offer a tenth part for every lamb of the seven lambs;
Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja.
22 and one male goat for a sin offering, to make atonement for you.
Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu.
23 You shall offer these besides the burnt offering of the morning, which is for a continual burnt offering.
Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa.
24 In this way you shall offer daily, for seven days, the food of the offering made by fire, of a pleasant aroma to YHWH: it shall be offered besides the continual burnt offering, and the drink offering of it.
Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa.
25 On the seventh day you shall have a holy convocation: you shall do no servile work.
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
26 "'Also in the day of the first fruits, when you offer a new meal offering to YHWH in your feast of weeks, you shall have a holy convocation; you shall do no servile work;
“‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa.
27 but you shall offer a burnt offering for a pleasant aroma to YHWH: two young bulls, one ram, seven male lambs a year old;
Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova.
28 and their meal offering, fine flour mixed with oil, three tenth parts for each bull, two tenth parts for the one ram,
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri.
29 a tenth part for every lamb of the seven lambs;
Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi.
30 one male goat, to make atonement for you.
Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu.
31 Besides the continual burnt offering, and the meal offering of it, you shall offer them (they shall be to you without blemish), and their drink offerings.
Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema.