< Judges 12 >

1 The men of Ephraim were gathered together, and passed northward; and they said to Jephthah, "Why did you pass over to fight against the people of Ammon, and did not call us to go with you? We will burn your house on you with fire."
Gulu la nkhondo la fuko la Efereimu linayitanidwa ndipo anawolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Nʼchifukwa chiyani unawoloka kukachita nkhondo ndi Aamoni osatiyitana kuti tipite nawe? Ife tikutenthera mʼnyumba mwakomu.”
2 And Jephthah said to them, "I and my people had a dispute, and the people of Ammon were oppressing me greatly; and when I called you, you did not save me out of their hand.
Yefita anayankha kuti, “Ine ndi anthu anga tinakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndinakuyitanani koma inu simunandipulumutse mʼmanja mwawo.
3 When I saw that you did not save me, I put my life in my own hands, and passed over against the people of Ammon, and YHWH delivered them into my hand. Why then have you come up to me this day, to fight against me?"
Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?”
4 Then Jephthah gathered together all the men of Gilead, and fought with Ephraim; and the men of Gilead struck Ephraim, because they said, "You are fugitives of Ephraim, you Gileadites, in the midst of Ephraim, and in the midst of Manasseh."
Choncho Yefita anasonkhanitsa anthu a ku Giliyadi ndi kuchita nkhondo ndi Aefereimu. Ndipo Agiliyadi anagonjetsa Aefereimu chifukwa Aefereimuwo amati, “Inu a Giliyadi ndinu othawa kuchokera ku Efereimu ndi pakati pa Amanase.”
5 The Gileadites took the fords of the Jordan against the Ephraimites. It was so, that when any of the fugitives of Ephraim said, "Let me go over," the men of Gilead said to him, "Are you an Ephraimite?" If he said, "No";
Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi”
6 then they said to him, "Now say 'Shibboleth;'" and he said "Sibboleth"; for he couldn't manage to pronounce it right: then they seized him, and killed him at the fords of the Jordan. There fell at that time of Ephraim forty-two thousand.
Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000.
7 Jephthah judged Israel six years. Then Jephthah the Gileadite died, and was buried in his city in Gilead.
Yefita anatsogolera Israeli zaka zisanu ndi chimodzi. Kenaka Yefita wa ku Giliyadi anamwalira, ndipo anayikidwa mu mzinda wake ku Giliyadi.
8 After him Ibzan of Bethlehem judged Israel.
Atamwalira Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu anatsogolera Israeli.
9 He had thirty sons; and thirty daughters he sent abroad, and thirty daughters he brought in from abroad for his sons. He judged Israel seven years.
Iye anali ndi ana aamuna makumi atatu ndi ana aakazi makumi atatu. Anakwatitsa ana ake akaziwo kwa anthu a fuko lina, ndipo ana ake aamuna aja anawabweretsera atsikana makumi atatu kuti awakwatire amenenso anali a fuko lina. Ibizani anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
10 Ibzan died, and was buried at Bethlehem.
Kenaka Ibizani anamwalira, ndipo anayikidwa mu Betelehemu.
11 After him Elon the Zebulunite judged Israel; and he judged Israel ten years.
Iye atamwalira, Eloni wa fuko la Zebuloni anakhala mtsogoleri wa Aisraeli, ndipo anatsogolera Aisraeli kwa zaka khumi.
12 Elon the Zebulunite died, and was buried in Aijalon in the land of Zebulun.
Kenaka Eloni anamwalira ndipo anayikidwa ku Ayaloni mʼdziko la Zebuloni.
13 After him Abdon the son of Hillel the Pirathonite judged Israel.
Iye atamwalira, Abidoni mwana wa Hilelo wochokera ku Piratoni, anatsogolera Israeli.
14 He had forty sons and thirty grandsons who rode on seventy donkey colts. And he judged Israel eight years.
Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu.
15 Abdon the son of Hillel the Pirathonite died, and was buried in Pirathon in the land of Ephraim, in the hill country of the Amalekites.
Ndipo Abidoni mwana wa Hilelo Mpiratoni uja anamwalira, nayikidwa ku Piratoni, mʼdziko la Efereimu, dziko lamapiri la Aamaleki.

< Judges 12 >