< Isaiah 23 >

1 The burden of Tyre. Howl, you ships of Tarshish. For it is laid waste, so that there is no house, no entering in. From the land of Kittim it is revealed to them.
Uthenga wonena za Turo: Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi: pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa ndipo mulibe nyumba kapena dooko. Zimenezi anazimva pochokera ku Kitimu.
2 Be still, you inhabitants of the coast, you whom the merchants of Sidon, that pass over the sea, have replenished.
Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja, inu amalonda a ku Sidoni, iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
3 On great waters, the seed of the Shihor, the harvest of the Nile, was her revenue. She was the market of nations.
Pa nyanja zazikulu panabwera tirigu wa ku Sihori; zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda ndi anthu a mitundu ina.
4 Be ashamed, Sidon; for the sea has spoken, the stronghold of the sea, saying, "I have not travailed, nor brought forth, neither have I nourished young men, nor brought up virgins."
Chita manyazi, iwe Sidimu pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti, “Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana; sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
5 When the report comes to Egypt, they will be in anguish at the report of Tyre.
Mawuwa akadzamveka ku Igupto, iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.
6 Pass over to Tarshish. Wail, you inhabitants of the coast.
Wolokerani ku Tarisisi, lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
7 Is this your joyous city, whose antiquity is of ancient days, whose feet carried her far away to travel?
Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja, mzinda wakalekale, umene anthu ake ankapita kukakhala ku mayiko akutali?
8 Who has planned this against Tyre, the giver of crowns, whose merchants are princes, whose traffickers are the honorable of the earth?
Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina, mzinda umene amalonda ake ndi akalonga ndi otchuka pa dziko lapansi?
9 YHWH of hosts has planned it, to defile all the pride of glory, to shame all the honored of the earth.
Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi kuti athetse kunyada kwawo ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.
10 Cultivate your land like the Nile, daughter of Tarshish; there is no restraint any more.
Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo inu anthu a ku Tarisisi, pakuti mulibenso chokutetezani.
11 He has stretched out his hand over the sea. He has shaken the kingdoms. YHWH has ordered the destruction of Canaan's strongholds.
Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja ndipo wagwedeza maufumu ake. Iye walamula kuti Kanaani agwetse malinga ake.
12 He said, "You shall rejoice no more, you oppressed virgin daughter of Sidon. Arise, pass over to Kittim. Even there you will have no rest."
Iye anati, “Simudzakondwanso konse, inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa! “Ngakhale muwolokere ku Kitimu, kumeneko simukapezako mpumulo.”
13 Look, the land of the Chaldeans, these people who have become nothing. The Assyrians have made it a home for wild animals. They set up their siege towers, they tore down her palaces, they made her a ruin.
Onani dziko la Ababuloni, anthu amenewa tsopano atheratu! Asiriya asandutsa Turo kukhala malo a zirombo za ku chipululu; anamanga nsanja zawo za nkhondo, anagumula malinga ake ndipo anawasandutsa bwinja.
14 Howl, you ships of Tarshish, for your stronghold is laid waste.
Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi; chifukwa malinga ako agwetsedwa!
15 It will come to pass in that day that Tyre will be forgotten seventy years, according to the days of one king. After the end of seventy years it will be to Tyre like in the song of the prostitute.
Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
16 Take a harp; go about the city, you prostitute that has been forgotten. Make sweet melody. Sing many songs, that you may be remembered.
“Tenga zeze wako uzungulire mzinda, iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika; imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri, kuti anthu akukumbukire.”
17 It will happen after the end of seventy years that YHWH will visit Tyre, and she shall return to her wages, and will play the prostitute with all the kingdoms of the world on the surface of the earth.
Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi.
18 Her merchandise and her wages will be holiness to YHWH. It will not be treasured nor laid up; for her merchandise will be for those who dwell before YHWH, to eat sufficiently, and for durable clothing.
Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.

< Isaiah 23 >