< 2 Chronicles 8 >

1 It happened at the end of twenty years, in which Solomon had built the house of YHWH, and his own house,
Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu ndi nyumba yake yaufumu,
2 that the cities which Hiram had given to Solomon, Solomon built them, and caused the children of Israel to dwell there.
Solomoni anamanganso midzi imene anapatsidwa ndi Hiramu, ndipo anakhazikamo Aisraeli.
3 Solomon went to Hamath Zobah, and prevailed against it.
Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba.
4 He built Tadmor in the wilderness, and all the storage cities, which he built in Hamath.
Iye anamanganso Tadimori ku chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anayimanga ku Hamati.
5 Also he built Upper Beth Horon, and Lower Beth Horon, fortified cities, with walls, gates, and bars;
Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira,
6 and Baalath, and all the storage cities that Solomon had, and all the cities for his chariots, and the cities for his horsemen, and all that Solomon desired to build for his pleasure in Jerusalem, and in Lebanon, and in all the land of his dominion.
pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
7 As for all the people who were left of the Hethites, and the Amorites, and the Perizzites, and the Hivites, and the Jebusites, who were not of Israel;
Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli).
8 of their descendants who were left after them in the land, whom the children of Israel did not destroy, of them Solomon conscripted for slave labor to this day.
Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino.
9 But of the children of Israel, Solomon made no slaves for his work; but they were men of war, and his commanders, and his captains, and rulers of his chariots and of his horsemen.
Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake.
10 These were the chief officers of king Solomon: five hundred fifty, who ruled over the people.
Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za mfumu Solomoni. Onse amene ankayangʼanira anthu analipo 250.
11 Solomon brought up the daughter of Pharaoh out of the City of David to the house that he had built for her; for he said, "My wife shall not dwell in the house of David king of Israel, because the places where the ark of YHWH has come are holy."
Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”
12 Then Solomon offered burnt offerings to YHWH on the altar of YHWH, which he had built before the porch,
Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera,
13 even as the duty of every day required, offering according to the commandment of Moses, on the Sabbaths, and on the new moons, and on the set feasts, three times in the year, in the feast of unleavened bread, and in the feast of weeks, and in the feast of tents.
monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa.
14 He appointed, according to the ordinance of David his father, the divisions of the priests to their service, and the Levites to their offices, to praise, and to minister before the priests, as the duty of every day required; the doorkeepers also by their divisions at every gate: for so had David the man of God commanded.
Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula.
15 They did not depart from the commandment of the king to the priests and Levites concerning any matter, or concerning the treasures.
Anthu sanapatukepo pa zimene mfumu inalamula ansembe kapena Alevi pa china chilichonse, kuphatikiza za chuma.
16 Now all the work of Solomon was carried out from the day of the foundation of the house of YHWH, until it was finished. So the house of YHWH was completed.
Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa.
17 Then went Solomon to Ezion Geber, and to Eilat, on the seashore in the land of Edom.
Kenaka Solomoni anapita ku Ezioni-Geberi ndi Eloti, mʼmbali mwa nyanja ku Edomu.
18 And Hiram sent him ships and servants who had knowledge of the sea by the hands of his servants; and they came with the servants of Solomon to Ophir, and fetched from there four hundred fifty talents of gold, and brought them to king Solomon.
Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.

< 2 Chronicles 8 >