< 1 Samuel 20 >

1 Then David fled from the dwellings at Ramah, and came before Jonathan and said, "What have I done? What is my iniquity? What is my sin before your father, that he seeks my life?"
Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?”
2 He said to him, "Far from it; you shall not die. Look, my father does nothing either great or small, but that he discloses it to me; and why should my father hide this thing from me? It is not so."
Yonatani anayankha kuti, “Sizitheka! Iwe sufa ayi! Taona abambo anga sachita chinthu chilichonse chachikulu kapena chachingʼono wosandiwuza ine. Tsopano abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Sichoncho ayi.”
3 And David answered and said, "Your father knows well that I have found favor in your eyes; and he says, 'Do not let Jonathan know this, lest he be grieved:' but truly as YHWH lives, and as your soul lives, there is but a step between me and death."
Koma Davide analumbira kuti, “Abambo ako akudziwa bwino lomwe kuti iwe umandikonda ndipo iwo amaganiza kuti, Yonatani sayenera kudziwa zimenezi mwina adzamva chisoni kwambiri. Komabe, pali Yehova ndi pali iwe, imfa sinanditalikire.”
4 Then Jonathan said to David, "Whatever your soul desires, I will do for you."
Yonatani anawuza Davide kuti, “Chilichonse chimene iwe ukufuna kuti ndichite, ndidzakuchitira.”
5 So David said to Jonathan, "Look, tomorrow is the new moon, and I should not fail to sit with the king to eat. Instead, let me go so that I may hide myself in the field until evening.
Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo.
6 If your father missed me at all, then say, 'David urgently requested of me that he might run to Bethlehem his city, for it is the yearly sacrifice there for all the family.'
Ngati abambo ako akafunsa za ine, ukawawuze kuti, ‘Davide anandiwumiriza kuti ndimulole apite msanga kwawo ku Betelehemu, chifukwa akupereka nsembe yapachaka ya banja lonse.’
7 If he says, 'It is well;' your servant shall have peace: but if he be angry, then know that evil is determined by him.
Akanena kuti, ‘Wachita bwino,’ ndiye kuti zinthu zindiyendera bwino ine mtumiki wako. Koma ngati akapsa mtima, ndiye udziwe kuti iwo atsimikiza zondichita zoyipa.
8 Therefore deal kindly with your servant; for you have brought your servant into a covenant of YHWH with you: but if there is iniquity in me, kill me yourself; for why should you bring me to your father?"
Koma undikomere mtima ine mtumiki wako, pakuti unapangana nane pangano pamaso pa Yehova. Ngati ndine wolakwa undiphe ndiwe, koma usandipereke kwa abambo ako.”
9 Jonathan said, "Far be it from you; for if I should at all know that evil were determined by my father to come on you, then wouldn't I tell you that?"
Yonatani anati, “Sizitheka! Ndikanadziwa kuti abambo anga atsimikiza kuti akuchite choyipa, kodi sindikanakuwuza?”
10 Then David said to Jonathan, "Who will tell me if your father answers you harshly?"
Davide anafunsa kuti, “Adzandiwuza ndani ngati abambo ako akuyankhe mwaukali?”
11 Jonathan said to David, "Come, and let us go out into the field." They both went out into the field.
Yonatani anawuza Davide kuti, “Tiyeni tikayende ku mundako.” Ndipo anapita onse awiri.
12 Jonathan said to David, "YHWH, the God of Israel, is witness. When I have studied my father, about this time tomorrow, or the third day, look, if there is good toward David, shall I not then send to you, and disclose it to you?
Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe.
13 But should it please my father to do you harm, God do so to Jonathan and more also if I do not let you know and send you away, that you may go in safety. And may YHWH be with you, as he has been with my father.
Koma ngati abambo anga atsimikiza kukuchita choyipa, Yehova andilange ine Yonatani, ndipotu kwambiri ngati sindidzakudziwitsa ndi kukulola kuti upite mu mtendere. Yehova akhale nawe monga anakhalira ndi abambo anga.
14 And if I am still alive, deal loyally with me. But if I die,
Ndikakhalabe ndi moyo udzandionetse kukoma mtima monga kwa Yehova nthawi yonse ya moyo wanga, kuti ine ndisaphedwe.
15 do not cut off your loyalty from my house forever. And when YHWH cuts off the enemies of David, each one from the face of the earth,
Ndipo usadzaleke kuchitira chifundo banja langa. Pamene Yehova adzawatha adani onse a Davide pa dziko lapansi.”
16 if the name of Jonathan be cut off from the house of David, then may YHWH require it at the hand of the enemies of David."
“Dzina la ine Yonatani lisadzafafanizidwe nawo pamodzi. Yehova alange adani onse a Davide.”
17 And Jonathan swore to David again, because he loved him, for he loved him as he loved his own soul.
Kenaka Yonatani anamulumbiritsanso Davide kuti asaleke kumukonda, pakuti ankamukonda monga ankadzikondera yekha.
18 Then Jonathan said, "Tomorrow is the new moon: and you will be missed, because your seat will be empty.
Kenaka Yonatani anawuzanso Davide kuti, “Mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Zidzadziwika kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu.
19 On the third day you should go down quickly, and come to the place where you hid yourself when this started, and stay by that mound.
Mkuja adzakufunafuna. Tsono udzapite pamalo pamene unabisala poyamba paja ndipo ukadikire pa mulu wa miyala uli apowo.
20 And as for me, on the third day I will shoot arrows to its side, aiming it toward a target.
Ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, ngati ndikulasa chinthu.
21 Look, I will send the boy, saying, 'Go, find the arrows.' If I tell the boy, 'Look, the arrow is on this side of you. Take it;' then come; for there is peace to you and no hurt, as YHWH lives.
Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse.
22 But if I say this to the boy, 'Look, the arrow is beyond you;' then go your way; for YHWH has sent you away.
Koma ndikadzati, ‘Taona mivi ili patsogolo pako,’ iwe udzachoke chifukwa Yehova ndiye walola kuti uchokepo.
23 Concerning the matter which you and I have spoken of, look, YHWH is a witness between you and me forever."
Tsono zimene tapanganazi Yehova ndiye mboni pakati pa iwe ndi ine mpaka muyaya.”
24 So David hid himself in the field. And when the new moon had come, the king sat at the table to eat.
Choncho Davide anakabisala mʼmunda ndipo nthawi ya chikondwerero cha mwezi watsopano itakwana mfumu Sauli anadzakhala pansi kuti adye.
25 The king sat on his seat, as at other times, even on the seat by the wall; and Jonathan sat opposite, and Abner sat by Saul's side: but David's place was empty.
Iye anakhala pa malo ake a nthawi zonse pafupi ndi khoma moyangʼanana ndi Yonatani, ndipo Abineri anakhala moyandikana ndi Sauli, koma pa malo a Davide panalibe munthu.
26 Nevertheless Saul did not say anything that day: for he thought, "Something has happened to him. He is not clean. Surely he is not clean."
Sauli sananene chilichonse tsiku limenelo pakuti ankaganiza kuti “Chilipo chimene chachitika ndi Davide. Mwina mwake ngosayenera za chipembedzo.”
27 It happened on the next day after the new moon, the second day, that David's place was empty. Saul said to Jonathan his son, "Why hasn't the son of Jesse come to the table, either yesterday or today?"
Koma pa tsiku lachiwiri la chikondwerero cha mwezi watsopano pamalo pa Davide panalibenso munthu. Kenaka Sauli anafunsa Yonatani kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwana wa Yese sanabwere kudzadya, dzulo ngakhale lero?”
28 Jonathan answered Saul, and said, "David earnestly asked leave of me to go to Bethlehem.
Yonatani anayankha kuti, “Davide anandiwumiriza kuti ndimulole kuti apite ku Betelehemu.
29 He said, 'Please let me go, for our family has a sacrifice in the city. And as for me, my brothers have ordered me to be there. Now, if I have found favor in your eyes, please let me go away and see my brothers.' Therefore he has not come to the king's table."
Anati, ‘Undilole ndipite, chifukwa banja lathu likupereka nsembe mu mzindamo ndipo mʼbale wanga wandiwumiriza kuti ndikakhale nawo. Ngati wandikomera mtima, chonde ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.”
30 Then Saul's anger flared up at Jonathan, and he said to him, "You son of a rebellious slave girl, don't I know that you are the companion of the son of Jesse, to your own disgrace, and to the disgrace of your mother's nakedness?
Sauli anamupsera mtima Yonatani ndipo namuwuza kuti, “Iwe mwana wobadwa mwa mkazi wamakhalidwe oyipa ndi wowukira! Kodi ukuyesa kuti ine sindikudziwa kuti umagwirizana ndi mwana wa Yese, amene akufuna kukuchititsa manyazi iwe ndi amayi ako?
31 For as long as the son of Jesse lives on the earth, your kingdom will not be established. Therefore now send and bring him to me, for he shall surely die."
Mwana wa Yese akakhala ndi moyo pa dziko lapansi lino, iwe sudzakhala mfumu. Tsopano tumiza munthu akamutenge kubwera naye kwa ine, pakuti Davide ayenera kufa basi!”
32 But Jonathan answered Saul, "Why should he be put to death? What has he done?"
Yonatani anafunsa abambo ake kuti, “Nʼchifukwa chiyani mufuna kuti Davide aphedwe? Iye walakwa chiyani?”
33 Then Saul threw his spear at him to strike him, and Jonathan realized that this evil from his father to kill David was determined.
Apo Sauli anamuponyera mkondo wake kuti amuphe. Tsono Yonatani anadziwa kuti abambo ake atsimikiza mtima kuti aphe Davide.
34 So Jonathan sprang up from the table in fierce anger, and ate no food the second day of the month; for he was grieved for David, because his father had dishonored him.
Yonatani anachoka pa tebulopo ali wopsa mtima kwambiri. Tsiku lachiwiri la chikondwererocho Yonatani sanadye chakudya. Iye anawawidwa mtima chifukwa abambo ake anatsimikiza zakupha Davide.
35 It happened in the morning, that Jonathan went out into the field at the time appointed with David, and a little boy with him.
Tsono mmawa Yonatani anapita ku munda kumene anapangana ndi Davide. Anali ndi mnyamata wake.
36 He said to the boy, "Run, find now the arrows which I shoot." And as the boy ran, he shot an arrow, causing it to pass beyond, toward the city.
Tsono anawuza mnyamatayo kuti, “Thamanga ukatole muvi umene nditi ndiponye.” Mnyamatayo akuthamanga Yonatani anaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo.
37 When the boy had come to the place of the arrow which Jonathan had shot, Jonathan called after the youth, and said, "Isn't the arrow beyond you?"
Mnyamatayo atafika pamene muvi wa Yonatani unagwera,
38 Jonathan cried after the boy, "Go fast. Hurry. Do not delay." Jonathan's boy gathered up the arrows, and came to his master.
Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake.
39 But the boy did not know anything. Only Jonathan and David knew the matter.
(Mnyamatayo sanadziwe chimene chimachitika koma Yonatani ndi Davide ndiwo ankadziwa).
40 Jonathan gave his weapons to his boy, and said to him, "Go, carry them to the city."
Pambuyo pake Yonatani anapereka zida zake za nkhondo kwa mnyamatayo ndipo anati, “Pita, nyamula ubwerere nazo ku mzinda.”
41 As soon as the boy was gone, David arose from beside the mound, and fell on his face to the ground, and bowed himself three times. They kissed one another, and wept one with another, and David wept the most.
Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.
42 Then Jonathan said, "Go in peace, because we have both sworn in the name of YHWH, saying, 'YHWH shall be between me and you, and between my descendants and your descendants, forever.'" He arose and departed; and Jonathan went into the city.
Yonatani anawuza Davide kuti, “Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’” Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja.

< 1 Samuel 20 >