< 1 Chronicles 16 >

1 They brought in the ark of God, and set it in the midst of the tent that David had set up for it: and they offered burnt offerings and peace offerings before God.
Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu.
2 When David had made an end of offering the burnt offering and the peace offerings, he blessed the people in the name of YHWH.
Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.
3 He dealt to everyone of Israel, both man and woman, to every one a loaf of bread, and a portion of meat, and a cake of raisins.
Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.
4 He appointed certain of the Levites to minister before the ark of YHWH, and to celebrate and to thank and praise YHWH, the God of Israel:
Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli.
5 Asaph the chief, and second to him Zechariah, Jaaziel, and Shemiramoth, and Jehiel, and Mattithiah, and Eliab, and Benaiah, and Obed-Edom, and Jeiel, with stringed instruments and with harps; and Asaph with cymbals, sounding aloud;
Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,
6 and Benaiah and Jahaziel the priests with trumpets continually, before the ark of the covenant of God.
ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.
7 Then on that day David first ordained to give thanks to YHWH, by the hand of Asaph and his brothers.
Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:
8 Oh give thanks to YHWH. Call on his name. Make his deeds known among the peoples.
Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
9 Sing to him. Sing praises to him. Tell of all his marvelous works.
Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando; nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.
10 Glory in his holy name. Let the heart of those who seek YHWH rejoice.
Nyadirani dzina lake loyera; ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.
11 Seek YHWH and his strength. Seek his face forever more.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.
12 Remember his marvelous works that he has done, his wonders, and the judgments of his mouth,
Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita, zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,
13 you offspring of Israel his servant, you descendants of Jacob, his chosen ones.
inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.
14 He is YHWH our God. His judgments are in all the earth.
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.
15 Remember his covenant forever, the word which he commanded to a thousand generations,
Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse, mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,
16 the covenant which he made with Abraham, his oath to Isaac.
pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake.
17 He confirmed the same to Jacob for a statute, and to Israel for an everlasting covenant,
Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo, kwa Israeli monga pangano lamuyaya.
18 saying, "I will give you the land of Canaan, The lot of your inheritance,"
“Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani monga cholowa chimene udzachilandira.”
19 when you were but a few men in number, yes, very few, and foreigners were in it.
Ali anthu owerengeka, ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,
20 They went about from nation to nation, from one kingdom to another people.
iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina, ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.
21 He allowed no man to do them wrong. Yes, he reproved kings for their sakes,
Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze; chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:
22 "Do not touch my anointed ones. Do my prophets no harm."
“Musakhudze odzozedwa anga; musawachitire choyipa aneneri anga.”
23 Sing to YHWH, all the earth. Display his salvation from day to day.
Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi; lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
24 Declare his glory among the nations, and his marvelous works among all the peoples.
Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
25 For great is YHWH, and greatly to be praised. He also is to be feared above all gods.
Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.
26 For all the gods of the peoples are idols, but YHWH made the heavens.
Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba.
27 Honor and majesty are before him. Strength and gladness are in his place.
Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake; mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.
28 Ascribe to YHWH, you relatives of the peoples, ascribe to YHWH glory and strength.
Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,
29 Ascribe to YHWH the glory due to his name. Bring an offering, and come before him. Worship YHWH in holy array.
perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake; pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.
30 Tremble before him, all the earth. The world also is established that it can't be moved.
Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi! Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
31 Let the heavens be glad, and let the earth rejoice. Let them say among the nations, "YHWH reigns."
Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere; anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”
32 Let the sea roar, and its fullness. Let the field exult, and all that is in it.
Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!
33 Then the trees of the forest will sing for joy before YHWH, for he comes to judge the earth.
Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba, idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova, pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
34 Oh give thanks to YHWH, for he is good, for his loving kindness endures forever.
Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.
35 Say, "Save us, God of our salvation. Gather us together and deliver us from the nations, to give thanks to your holy name, to triumph in your praise."
Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu, mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina, kuti tiyamike dzina lanu loyera, kuti tikutamandeni.”
36 Blessed be YHWH, the God of Israel, from everlasting to everlasting. And all the people said, "Amen," and praised YHWH.
Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”
37 So he left there, before the ark of the covenant of YHWH, Asaph and his brothers, to minister before the ark continually, as every day's work required;
Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse.
38 and Obed-Edom with their brothers, sixty-eight; Obed-Edom also the son of Jeduthun and Hosah to be doorkeepers;
Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.
39 and Zadok the priest, and his brothers the priests, before the tabernacle of YHWH in the high place that was at Gibeon,
Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni
40 to offer burnt offerings to YHWH on the altar of burnt offering continually morning and evening, even according to all that is written in the law of YHWH, which he commanded to Israel;
kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli.
41 and with them Heman and Jeduthun, and the rest who were chosen, who were mentioned by name, to give thanks to YHWH, because his loving kindness endures forever;
Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
42 and with them Heman and Jeduthun with trumpets and cymbals for those that should sound aloud, and with instruments for the songs of God; and the sons of Jeduthun to be at the gate.
Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.
43 All the people departed every man to his house: and David returned to bless his house.
Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.

< 1 Chronicles 16 >