< 1 Chronicles 13 >

1 David consulted with the captains of thousands and of hundreds, even with every leader.
Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100.
2 David said to all the assembly of Israel, "If it seems good to you, and if there is a breakthrough from the LORD our God, let us send abroad everywhere to our brothers who are left in all the land of Israel, with whom the cohanim and Levites are in their cities that have suburbs, that they may gather themselves to us;
Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe.
3 and let us bring again the ark of our God to us. For we did not seek it in the days of Saul."
Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.”
4 All the assembly said that they would do so; for the thing was right in the eyes of all the people.
Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero.
5 So David assembled all Israel together, from the Shihor of Egypt even to Lebo Hamath, to bring the ark of God from Kiriath Jearim.
Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu.
6 And David went up, and all Israel, to Baalah, that is, to Kiriath Jearim, which belongs to Judah, to bring up from there the ark of God, which is called by the name of the LORD enthroned on the cherubim.
Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.
7 They carried the ark of God on a new cart, and brought it out of the house of Abinadab: and Uzza and Ahio drove the cart.
Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo.
8 David and all Israel played before God with all their might, even with songs, and with harps, and with stringed instruments, and with tambourines, and with cymbals, and with trumpets.
Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
9 When they came to the threshing floor of Nodan, Uzza put forth his hand to hold the ark; for the oxen stumbled.
Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa.
10 The anger of the LORD was kindled against Uzza, and he struck him, because he put forth his hand to the ark; and there he died before God.
Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.
11 David was displeased, because the LORD had broken forth on Uzza; and he called that place Perez Uzza, to this day.
Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
12 David was afraid of God that day, saying, "How can I bring the ark of God to me?"
Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?”
13 So David did not move the ark to him into the City of David, but diverted it to the house of Obed-Edom the Gittite.
Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.
14 The ark of God remained with the family of Obed-Edom in his house three months: and the LORD blessed the house of Obed-Edom, and all that he had.
Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho.

< 1 Chronicles 13 >