< Luke 20 >
1 It happened on one of those days, as he was teaching the people in the temple and preaching the gospel, that the chief priests and scribes came to him with the elders.
Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
2 They asked him, "Tell us: by what authority do you do these things? Or who is giving you this authority?"
Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”
3 He answered them, "I also will ask you one question. Tell me:
Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe,
4 the baptism of John, was it from heaven, or from man?"
‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’”
5 They reasoned with themselves, saying, "If we say, 'From heaven,' he will say, 'Why did you not believe him?'
Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’
6 But if we say, 'From man,' all the people will stone us, for they are persuaded that John was a prophet."
Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”
7 They answered that they did not know where it was from.
Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”
8 Jesus said to them, "Neither will I tell you by what authority I do these things."
Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”
9 He began to tell the people this parable. "A man planted a vineyard, and rented it out to some farmers, and went on a journey for a long time.
Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali.
10 At the proper season, he sent a servant to the farmers to collect his share of the fruit of the vineyard. But the farmers beat him, and sent him away empty.
Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu.
11 He sent yet another servant, and they also beat him, and treated him shamefully, and sent him away empty.
Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu.
12 He sent yet a third, and they also wounded him, and threw him out.
Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.
13 The lord of the vineyard said, 'What am I to do? I will send my beloved son. It may be that they will respect him.'
“Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’
14 "But when the farmers saw him, they reasoned among themselves, saying, 'This is the heir. Let us kill him, that the inheritance may be ours.'
“Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’
15 They threw him out of the vineyard, and killed him. What therefore will the lord of the vineyard do to them?
Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha. “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?
16 He will come and destroy these farmers, and will give the vineyard to others." When they heard it, they said, "May it never be."
Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.” Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”
17 But he looked at them, and said, "Then what is this that is written, 'The stone which the builders rejected, the same was made the chief cornerstone?'
Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti, “‘Mwala umene omanga nyumba anawukana wasanduka mwala wa pa ngodya.
18 Everyone who falls on that stone will be broken to pieces; but on whomever it falls, it will crush him."
Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’”
19 The chief priests and the scribes sought to lay hands on him that very hour, but they feared the people—for they knew he had spoken this parable against them.
Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.
20 They watched him, and sent out spies, who pretended to be righteous, that they might trap him in something he said, so as to deliver him up to the power and authority of the governor.
Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza.
21 They asked him, "Teacher, we know that you say and teach what is right, and are not partial to anyone, but truly teach the way of God.
Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi.
22 Is it lawful for us to pay taxes to Caesar, or not?"
Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”
23 But he perceived their craftiness, and said to them,
Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti,
24 "Show me a denarius. Whose image and inscription are on it?" They answered, "Caesar's."
“Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”
25 He said to them, "Then give to Caesar the things that are Caesar's, and to God the things that are God's."
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”
26 They weren't able to trap him in his words before the people. And amazed at his answer, they fell silent.
Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.
27 Some of the Sadducees came to him, those who deny that there is a resurrection.
Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso.
28 They asked him, "Teacher, Moses wrote to us that if a man's brother dies having a wife, and he is childless, his brother should take the wife, and raise up children for his brother.
Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo.
29 There were therefore seven brothers. The first took a wife, and died childless.
Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana.
31 the third took her, and likewise the seven all left no children, and died.
ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana.
32 Afterward the woman also died.
Pa mapeto pake mkaziyo anafanso.
33 Therefore in the resurrection whose wife of them will she be? For the seven had her as a wife."
Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”
34 Jesus said to them, "The people of this age marry and are given to someone to marry. (aiōn )
Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa. (aiōn )
35 But those who are regarded as worthy of a place in that age and the resurrection from the dead neither marry nor are given to someone to marry. (aiōn )
Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. (aiōn )
36 For they cannot die any more, for they are like the angels, and are children of God, being children of the resurrection.
Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.
37 But that the dead are raised, even Moses showed at the bush, when he called the Lord 'The God of Abraham, and the God of Isaac, and the God of Jacob.'
Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’
38 Now he is not the God of the dead, but of the living, for all are alive to him."
Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”
39 Some of the scribes answered, "Teacher, you speak well."
Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!”
40 They did not dare to ask him any more questions.
Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.
41 He said to them, "Why do they say that the Messiah is David's son?
Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide?
42 David himself says in the scroll of Psalms, 'The Lord said to my Lord, "Sit at my right hand,
Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,
43 until I make your enemies the footstool of your feet."'
mpaka Ine nditasandutsa adani anu chopondapo mapazi anu?’
44 "David therefore calls him Lord, so how is he his son?"
Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”
45 In the hearing of all the people, he said to his disciples,
Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake,
46 "Beware of the scribes, who like to walk in long robes, and love greetings in the marketplaces, the best seats in the synagogues, and the best places at feasts;
“Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando.
47 who devour widows' houses, and for a pretense make long prayers: these will receive greater condemnation."
Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”