< 2 Samuel 21 >

1 Now there was a famine in the days of David for three consecutive years, so David sought the face of the LORD. And the LORD said, "There is bloodguilt on Saul and on his house, because he murdered the Gibeonites."
Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.”
2 So the king summoned the Gibeonites, and spoke to them. (Now the Gibeonites were not of the children of Israel but of the remnant of the Amorites. And the children of Israel had sworn to them, but Saul sought to exterminate them in his zeal for the children of Israel and Judah.)
Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu).
3 And David said to the Gibeonites, "What can I do for you? And how can I make atonement, that you may bless the inheritance of the LORD?"
Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”
4 The Gibeonites said to him, "It is not a matter of silver or gold between us and Saul or his house, nor is it our place to put anyone to death in Israel." Then he said, "What do you want? For I will do it for you."
Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.” Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”
5 So they said to the king, "The man who opposed us and persecuted us, who meant to eradicate us from having a place anywhere in the territory of Israel,
Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli,
6 let seven of his sons be delivered to us, and we will hang them before the LORD at Gibeon on the mountain of the LORD." And the king replied, "I will do it."
mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”
7 But the king spared Mippibaal, the son of Jonathan, the son of Saul, because of the LORD's oath that was between them, between David and Jonathan the son of Saul.
Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova.
8 But the king took the two sons of Rizpah the daughter of Aiah, whom she bore to Saul, Armoni and Mippibaal; and the five sons of Merob the daughter of Saul, whom she bore to Adriel the son of Barzillai the Meholathite.
Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati.
9 And he delivered them into the hands of the Gibeonites, and they hanged them on the mountain before the LORD, and all seven of them fell together. And they were put to death in the first days of harvest at the beginning of barley harvest.
Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.
10 And Rizpah the daughter of Aiah took sackcloth and spread it for herself on a rock, from the beginning of harvest until it rained on them from the sky. And she did not allow the birds of the sky to rest on them by day, nor the wild animals by night.
Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku.
11 It was told David what Rizpah the daughter of Aiah, the secondary wife of Saul, had done.
Davide atawuzidwa zimene Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa, mzikazi wa Sauli anachita,
12 Then David went and obtained the bones of Saul and the bones of his son Jonathan from the citizens of Jabesh Gilead, who had stolen them from the public square of Beth Shan, where the Philistines had hung them on the day that the Philistines killed Saul on Gilboa;
anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa).
13 and he brought up from there the bones of Saul and the bones of Jonathan his son. And they gathered the bones of those who were hanged.
Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi.
14 And he buried the bones of Saul and Jonathan in the land of Benjamin in Zela, in the tomb of Kish his father. And they performed all that the king commanded. After that God responded to prayers for the land.
Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo.
15 The Philistines had war again with Israel; and David went down, and his servants with him, and fought against the Philistines. Now David became exhausted,
Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri.
16 and Dodo son of Joash, of the descendants of the Raphah, captured him. His spear weighed three hundred bronze shekels, and he was girded with a new sword, and he thought he could kill David.
Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide.
17 But Abishai the son of Zeruiah helped him and struck the Philistine, and killed him. Then the men of David took an oath, saying, "You must not go out to battle with us again, so that you do not extinguish the lamp of Israel."
Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.”
18 Now it came to pass after this that there was another battle with the Philistines at Gezer. Then Sibbekai the Hushathite killed Saph, a descendant of the Raphah.
Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai.
19 There was again war with the Philistines at Gob; and Elhanan the son of Jair the Bethlehemite killed the brother of Goliath the Gittite, the staff of whose spear was like a weaver's beam.
Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu.
20 There was another battle at Gath, where there was a man of great stature who had on six fingers on each hand, and six toes on each foot, twenty four in number, and he also was a descendant of Raphah.
Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa.
21 When he defied Israel, Jonathan the son of Shimeah, David's brother, killed him.
Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.
22 These four were descendants of Raphah in Gath; and they fell by the hand of David, and by the hand of his servants.
Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.

< 2 Samuel 21 >