< Revelation 13 >

1 And he stood on the sand of the sea. And I saw a beast coming up out of the sea, having ten horns and seven heads. On his horns were ten crowns, and on his heads, blasphemous names.
Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja. Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
2 The beast which I saw was like a leopard, and his feet were like those of a bear, and his mouth like the mouth of a lion. The serpent gave him his power, his throne, and great authority.
Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu.
3 One of his heads looked like it had been wounded fatally. His fatal wound was healed, and the whole earth was amazed and followed the beast.
Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho.
4 They worshiped the serpent, because he gave his authority to the beast, and they worshiped the beast, saying, "Who is like the beast? Who is able to make war with him?"
Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
5 A mouth was given to him speaking proud words and blasphemies. There was given to him authority to act for forty-two months.
Chirombo chija chinaloledwa kuyankhula mawu onyada ndi achipongwe kwa Mulungu. Chinapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42.
6 He opened his mouth for blasphemies against God, to blaspheme his name, and his dwelling, those who dwell in heaven.
Ndipo chinayamba kuyankhula mawu achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo okhalamo ndi onse amene amakhala kumwamba.
7 It was given to him to make war with the saints, and to overcome them. Authority over every tribe, people, language, and nation was given to him.
Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse.
8 All who dwell on the earth will worship him, everyone whose name has not been written from the foundation of the world in the Book of Life of the Lamb who has been killed.
Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.
9 If anyone has an ear, let him hear.
Iye amene ali ndi makutu, amve.
10 If anyone is to go into captivity, he will go into captivity. If anyone is to be killed with the sword, he must be killed with the sword. Here is the endurance and the faith of the saints.
“Woyenera kupita ku ukapolo, adzapita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga, adzafa ndi lupanga.” Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika.
11 I saw another beast coming up out of the earth. He had two horns like a lamb, and he spoke like a serpent.
Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka.
12 He exercises all the authority of the first beast in his presence. He makes the earth and those who dwell in it to worship the first beast, whose fatal wound was healed.
Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola.
13 He performs great signs, even making fire come down out of heaven to the earth in the sight of people.
Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu zodabwitsa, mpaka kumagwetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba anthu akuona.
14 He deceives those who dwell on the earth because of the signs he was granted to do in front of the beast; saying to those who dwell on the earth, that they should make an image to the beast who had been wounded by the sword and yet lived.
Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo.
15 It was given to him to give breath to it, to the image of the beast, that the image of the beast could both speak and cause those who would not worship the image of the beast to be killed.
Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo.
16 He causes all, the small and the great, the rich and the poor, and the free and the slave, to be given a mark on their right hand, or on their forehead;
Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi.
17 and that no one could be able to buy or to sell, unless he has that mark, the name of the beast or the number of his name.
Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake.
18 Here is wisdom. He who has understanding, let him calculate the number of the beast, for it is the number of a man. His number is six hundred sixty-six.
Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.

< Revelation 13 >