< Revelation 20 >

1 I saw an angel coming down out of heaven, having the key of the abyss and a great chain in his hand. (Abyssos g12)
Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. (Abyssos g12)
2 He seized the serpent, the ancient snake, which is the devil and Satana, and bound him for a thousand years,
Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000.
3 and cast him into the abyss, and shut it, and sealed it over him, that he should deceive the nations no more, until the thousand years were finished. After this, he must be freed for a short time. (Abyssos g12)
Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe. (Abyssos g12)
4 I saw thrones, and they sat on them, and judgment was given to them. I saw the souls of those who had been beheaded for the testimony of Yeshua, and for the word of God, and such as did not worship the beast nor his image, and did not receive the mark on their forehead and on their hand. They lived, and reigned with Meshikha for a thousand years.
Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000.
5 The rest of the dead did not live until the thousand years were finished. This is the first resurrection.
(Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba.
6 Blessed and holy is he who has part in the first resurrection. Over these, the second death has no power, but they will be priests of God and of Meshikha, and will reign with him one thousand years.
Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.
7 And after the thousand years, Satana will be released from his prison,
Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake
8 and he will come out to deceive the nations which are in the four quarters of the earth, Gog and Magog, to gather them together to the war; the number of whom is as the sand of the sea.
ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
9 They went up over the breadth of the earth, and surrounded the camp of the saints, and the beloved city, and fire came down out of heaven and devoured them.
Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa.
10 The devil who deceived them was thrown into the lake of fire and sulfur, where the beast and the false prophet are also. They will be tormented day and night forever and ever. (aiōn g165, Limnē Pyr g3041 g4442)
Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya. (aiōn g165, Limnē Pyr g3041 g4442)
11 I saw a great white throne, and him who sat on it, from whose face the earth and the heaven fled away. There was found no place for them.
Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo.
12 I saw the dead, the great and the small, standing before the throne, and they opened books. Another book was opened, which is the Book of Life. The dead were judged out of the things which were written in the books, according to their works.
Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.
13 The sea gave up the dead who were in it. Death and Sheyul gave up the dead who were in them. They were judged, each one according to his works. (Hadēs g86)
Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. (Hadēs g86)
14 Death and Sheyul were thrown into the lake of fire. This is the second death, the lake of fire. (Hadēs g86, Limnē Pyr g3041 g4442)
Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. (Hadēs g86, Limnē Pyr g3041 g4442)
15 If anyone was not found written in the Book of Life, he was cast into the lake of fire. (Limnē Pyr g3041 g4442)
Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto. (Limnē Pyr g3041 g4442)

< Revelation 20 >