< Matthew 21 >
1 When they drew near to Urishlim, and came to Beth-Pageh, to the Mount of Olives, then Yeshua sent two disciples,
Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri,
2 saying to them, "Go into the village that is opposite you, and immediately you will find a donkey tied, and a colt with her. Untie them, and bring them to me.
nawawuza kuti, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine.
3 And if anyone says anything to you, you are to say, 'Because the Lord needs them,' and he will send them at once."
Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.”
4 This took place that it might be fulfilled which was spoken through the prophet, saying,
Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:
5 Say to the daughter of Tsehyun, "Look, your King comes to you, humble, and riding on a donkey, on a colt, the foal of a donkey."
“Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
6 The disciples went, and did just as Yeshua directed them,
Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira.
7 and brought the donkey and the colt, and placed their clothes on them; and he sat on them.
Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo.
8 A very large crowd spread their clothes on the road. Others cut branches from the trees, and spread them on the road.
Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo.
9 The crowds who went before him, and who followed kept shouting, "Ushanna to the son of Dawid. Blessed is he who comes in the name of the Lord. Ushanna in the highest."
Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti, “Hosana Mwana wa Davide!” “Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!” “Hosana mmwambamwamba!”
10 When he had come into Urishlim, all the city was stirred up, saying, "Who is this?"
Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”
11 The crowds said, "This is the prophet Yeshua, from Natsrath of Galila."
Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.”
12 Yeshua entered into the temple, and drove out all of those who sold and bought in the temple, and overthrew the money changers' tables and the seats of those who sold the doves.
Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.
13 He said to them, "It is written, 'My house will be called a house of prayer,' but you have made it a den of robbers."
Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”
14 The blind and the lame came to him in the temple, and he healed them.
Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa.
15 But when the chief priests and the scribes saw the wonderful things that he did, and the children crying out in the temple and saying, "Ushanna to the son of Dawid." they were indignant,
Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.
16 and said to him, "Do you hear what these are saying?" Yeshua said to them, "Yes. Did you never read, 'Out of the mouth of children and infants you have prepared praise?'"
Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?” Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti, “Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda mwatuluka mayamiko?”
17 He left them, and went out of the city to Beth-Naiya, and lodged there.
Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona.
18 Now in the morning, as he returned to the city, he was hungry.
Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala.
19 Seeing a fig tree by the road, he came to it, and found nothing on it but leaves. He said to it, "Let there be no fruit from you forever." Immediately the fig tree withered away. (aiōn )
Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota. (aiōn )
20 When the disciples saw it, they were amazed, saying, "How did the fig tree immediately wither away?"
Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”
21 Yeshua answered them, "Truly I tell you, if you have faith, and do not doubt, you will not only do what was done to the fig tree, but even if you told this mountain, 'Be taken up and cast into the sea,' it would be done.
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.
22 All things, whatever you ask in prayer, believing, you will receive."
Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”
23 When he had come into the temple, the chief priests and the elders of the people came to him as he was teaching, and said, "By what authority do you do these things? Who gave you this authority?"
Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
24 Yeshua answered them, "I also will ask you one question, which if you tell me, I likewise will tell you by what authority I do these things.
Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi.
25 The baptism of Yukhanan, where was it from? From heaven or from people?" They reasoned with themselves, saying, "If we say, 'From heaven,' he will ask us, 'Why then did you not believe him?'
Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’
26 But if we say, 'From people,' we fear the crowd, for all hold Yukhanan as a prophet."
Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”
27 They answered Yeshua, and said, "We do not know." He also said to them, "Neither will I tell you by what authority I do these things.
Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.” Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”
28 But what do you think? A man had two sons, and he came to the first, and said, 'Son, go work today in the vineyard.'
“Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
29 He answered, 'I will not,' but afterward he changed his mind, and went.
“Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.
30 And he came to the other, and said the same thing. And he answered and said, 'I go, sir,' but he did not go.
“Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.
31 Which of the two did the will of his father?" They said, "The first." Yeshua said to them, "Truly I tell you that the tax collectors and the prostitutes are entering into the Kingdom of God before you.
“Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?” Anamuyankha nati, “Woyambayo.” Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.”
32 For Yukhanan came to you in the way of righteousness, and you did not believe him, but the tax collectors and the prostitutes believed him. When you saw it, you did not even repent afterward, that you might believe him.
Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
33 "Hear another parable. There was a landowner who planted a vineyard, set a hedge about it, dug a winepress in it, built a tower, leased it out to tenant farmers, and went on a journey.
“Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo.
34 When the season for the fruit drew near, he sent his servants to the tenants, to receive his fruit.
Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.
35 The tenants took his servants, beat one, killed another, and stoned another.
“Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo.
36 Again, he sent other servants more than the first: and they treated them the same way.
Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi.
37 But afterward he sent to them his son, saying, 'They will respect my son.'
Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.
38 But the tenants, when they saw the son, said among themselves, 'This is the heir. Come, let us kill him, and have his inheritance.'
“Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’
39 So they took him, and threw him out of the vineyard, and killed him.
Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.
40 When therefore the lord of the vineyard comes, what will he do to those tenants?"
“Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”
41 They told him, "He will utterly destroy those evil men, and will lease out the vineyard to other tenants, who will give him the fruit in its season."
Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”
42 Yeshua said to them, "Did you never read in the Scriptures, 'The stone which the builders rejected, this one was made the cornerstone. This was from the Lord. It is marvelous in our eyes?'
Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
43 "Therefore I tell you, the Kingdom of God will be taken away from you, and will be given to a nation bringing forth its fruit.
“Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake.
44 He who falls on this stone will be broken to pieces; but on whomever it will fall, it will crush him."
Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”
45 When the chief priests and the Pharisees heard his parables, they perceived that he spoke about them.
Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo.
46 When they sought to seize him, they feared the crowds, because they considered him to be a prophet.
Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.