< Matthew 17 >
1 After six days, Yeshua took with him Kipha, Yaquv, and Yukhanan his brother, and brought them up into a high mountain by themselves.
Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali.
2 He was transfigured before them. His face shone like the sun, and his garments became as white as the light.
Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu.
3 And look, Mushe and Eliya appeared to them talking with him.
Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.
4 Kipha answered, and said to Yeshua, "Lord, it is good for us to be here. If you want, let us make three tents here: one for you, one for Mushe, and one for Eliya."
Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
5 While he was still speaking, look, a bright cloud overshadowed them. And look, a voice came out of the cloud, saying, "This is my beloved Son, in whom I am well pleased. Listen to him."
Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
6 When the disciples heard it, they fell on their faces, and were very afraid.
Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba.
7 Yeshua came and touched them and said, "Get up, and do not be afraid."
Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.”
8 And when they lifted up their eyes, they saw no one except Yeshua alone.
Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.
9 As they were coming down from the mountain, Yeshua commanded them, saying, "Do not tell anyone what you saw, until the Son of Man has risen from the dead."
Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
10 The disciples asked him, saying, "Then why do the scribes say that Eliya must come first?"
Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”
11 And he answered and said, "Eliya indeed comes, and will restore all things,
Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse.
12 but I tell you that Eliya has come already, and they did not recognize him, but did to him whatever they wanted to. Even so the Son of Man will also suffer by them."
Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.”
13 Then the disciples understood that he spoke to them of Yukhanan the Baptist.
Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.
14 When they came to the crowd, a man came to him, kneeling down to him, saying,
Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake.
15 "Lord, have mercy on my son, for he is epileptic, and suffers severely; for he often falls into the fire, and often into the water.
Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi.
16 So I brought him to your disciples, and they could not cure him."
Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
17 Yeshua answered, "Faithless and perverse generation. How long will I be with you? How long will I bear with you? Bring him here to me."
Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.”
18 Yeshua rebuked him, the demon went out of him, and the boy was cured from that hour.
Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
19 Then the disciples came to Yeshua privately, and said, "Why weren't we able to cast it out?"
Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”
20 So he said to them, "Because of your little faith. For truly I tell you, if you have faith as a grain of mustard seed, you will tell this mountain, 'Move from here to there,' and it will move; and nothing will be impossible for you."
Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.
Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”
22 While they were gathering together in Galila, Yeshua said to them, "The Son of Man is about to be delivered up into the hands of men,
Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.
23 and they will kill him, and the third day he will be raised up." They were exceedingly sorry.
Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.
24 When they had come to Kepharnakhum, those who collected the zuzeen coins came to Kipha, and said, "Does not your teacher pay the zuzeen?"
Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
25 He said, "Yes." When he came into the house, Yeshua anticipated him, saying, "What do you think, Shimon? From whom do the kings of the earth receive toll or tribute? From their children, or from strangers?"
Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.” Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”
26 And when he said, "From strangers." Yeshua said to him, "Therefore the children are exempt.
Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.” Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.”
27 But, lest we cause them to stumble, go to the lake, cast a hook, and take up the first fish that comes up. When you have opened its mouth, you will find a stater coin. Take that, and give it to them for me and you."
Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.