< Matthew 5 >

1 And having seen the multitudes, He went up to the mountain, and He having sat down, His disciples came to Him,
Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye,
2 and having opened His mouth, He was teaching them, saying,
ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,
3 “Blessed the poor in spirit—because theirs is the kingdom of the heavens.
“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
4 Blessed the mourning—because they will be comforted.
Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.
5 Blessed the meek—because they will inherit the land.
Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.
6 Blessed those hungering and thirsting for righteousness—because they will be filled.
Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa.
7 Blessed the kind—because they will find kindness.
Odala ndi amene ali ndi chifundo, chifukwa adzawachitira chifundo.
8 Blessed the clean in heart—because they will see God.
Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.
9 Blessed the peacemakers—because they will be called sons of God.
Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Blessed those persecuted for righteousness’ sake—because theirs is the kingdom of the heavens.
Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
11 Blessed are you whenever they may reproach you, and may persecute, and may say any evil thing against you falsely for My sake—
“Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine.
12 rejoice and be glad, because your reward [is] great in the heavens, for thus they persecuted the prophets who were before you.
Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.
13 You are the salt of the earth, but if the salt may lose savor, in what will it be salted? It is good for nothing from now on, except to be cast outside, and to be trodden down by men.
“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.
14 You are the light of the world, a city set on a mountain is not able to be hid;
“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.
15 nor do they light a lamp and put it under the measure, but on the lampstand, and it shines to all those in the house;
Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.
16 so let your light shine before men, that they may see your good works, and may glorify your Father who [is] in the heavens.
Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.
17 Do not suppose that I came to throw down the Law or the Prophets—I did not come to throw down, but to fulfill;
“Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa.
18 for truly I say to you, until the heaven and the earth may pass away, one iota or one tittle may not pass away from the Law, until all may come to pass.
Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.
19 Therefore whoever may loose one of these commands—the least—and may teach men so, he will be called least in the kingdom of the heavens, but whoever may do and may teach [them], he will be called great in the kingdom of the heavens.
Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.
20 For I say to you that if your righteousness may not abound above that of the scribes and Pharisees, you may not enter into the kingdom of the heavens.
Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.
21 You heard that it was said to the ancients: You will not murder, and whoever may murder will be in danger of the judgment;
“Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’
22 but I say to you that everyone who is angry at his brother without cause will be in danger of the judgment, and whoever may say to his brother, Stupid, will be in danger of the Sanhedrin, and whoever may say, Moron, will be in danger of the Gehenna of fire. (Geenna g1067)
Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena. (Geenna g1067)
23 If, therefore, you may bring your gift to the altar, and there may remember that your brother has anything against you,
“Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa,
24 leave there your gift before the altar, and go—first be reconciled to your brother, and then having come, bring your gift.
usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.
25 Be agreeing with your opponent quickly, while you are in the way with him, that the opponent may not deliver you to the judge, and the judge may deliver you to the officer, and you may be cast into prison;
“Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende.
26 truly I say to you, you may not come forth from there until you may pay the last penny.
Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti sudzatuluka mʼndende mpaka utalipira zonse.
27 You heard that it was said to the ancients: You will not commit adultery;
“Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’
28 but I say to you that everyone who is looking on a woman to desire her, already committed adultery with her in his heart.
Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.
29 But if your right eye causes you to stumble, pluck it out and cast from you, for it is good to you that one of your members may perish, and not your whole body be cast into Gehenna. (Geenna g1067)
Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. (Geenna g1067)
30 And if your right hand causes you to stumble, cut it off, and cast from you, for it is good to you that one of your members may perish, and not your whole body be cast into Gehenna. (Geenna g1067)
Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. (Geenna g1067)
31 And it was said that, Whoever may put away his wife, let him give to her a writing of divorce;
“Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’
32 but I say to you that whoever may put away his wife, except for the matter of whoredom, makes her to commit adultery; and whoever may marry her who has been put away commits adultery.
Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.
33 Again, you heard that it was said to the ancients: You will not swear falsely, but you will pay to the LORD your oaths;
“Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’
34 but I say to you not to swear at all; neither by Heaven, because it is the throne of God,
Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu.
35 nor by the earth, because it is His footstool, nor by Jerusalem, because it is [the] city of [the] great King,
Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu.
36 nor may you swear by your head, because you are not able to make one hair white or black;
Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi.
37 but let your word be, Yes, Yes, No, No, and that which is more than these is of the evil [one].
Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.
38 You heard that it was said: Eye for eye, and tooth for tooth;
“Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’
39 but I say to you not to resist the evil, but whoever will slap you on your right cheek, turn to him also the other;
Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo.
40 and whoever is willing to take you to law, and to take your coat—also permit to him the cloak.
Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako.
41 And whoever will impress you one mile, go with him two;
Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri.
42 to him who is asking of you be giving, and him who is willing to borrow from you, you may not turn away.
Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.
43 You heard that it was said: You will love your neighbor, and will hate your enemy;
“Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’
44 but I say to you, love your enemies, bless those cursing you, do good to those hating you, and pray for those accusing you falsely, and persecuting you,
Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani
45 that you may be sons of your Father in the heavens, because He causes His sun to rise on evil and good, and He sends rain on righteous and unrighteous.
kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’
46 For if you may love those loving you, what reward do you have? Do the tax collectors not also do the same?
Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi?
47 And if you may greet your brothers only, what do you do abundant? Do the nations not also do so?
Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi?
48 You will therefore be perfect, as your Father who [is] in the heavens is perfect.”
Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”

< Matthew 5 >