< Joshua 13 >
1 And Joshua is old, entering into days, and YHWH says to him, “You have become aged, you have entered into days; as for the land, very much has been left to possess.
Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.
2 This [is] the land that is left: all the circuits of the Philistines, and all Geshuri,
“Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri
3 from Sihor which [is] on the front of Egypt, and to the border of Ekron northward (it is reckoned to the Canaanite), five princes of the Philistines, the Gazathite, and the Ashdothite, the Eshkalonite, the Gittite, and the Ekronite, also the Avim;
kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto.
4 from the south, all the land of the Canaanite, and Mearah, which [is] to the Sidonians, to Aphek, to the border of the Amorite;
Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori.
5 and the land of the Giblite, and all Lebanon, at the sun-rising, from Ba‘al-Gad under Mount Hermon, to the going in to Hamath:
Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati.
6 all the inhabitants of the hill-country, from Lebanon to Misrephoth-Maim, all the Sidonians: I dispossess them before the sons of Israel; only, cause it to fall to Israel for an inheritance, as I have commanded you.
“Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira.
7 And now, apportion this land for an inheritance to the nine tribes, and half of the tribe of Manasseh.”
Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”
8 With [the other half], the Reubenite and the Gadite have received their inheritance, which Moses has given to them beyond the Jordan eastward, as Moses servant of YHWH has given to them;
Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.
9 from Aroer, which [is] on the edge of the Brook of Arnon, and the city which [is] in the midst of the brook, and all the plain of Medeba to Dihon,
Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni.
10 and all the cities of Sihon king of the Amorite, who reigned in Heshbon, to the border of the sons of Ammon,
Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni.
11 and Gilead, and the border of the Geshurite, and of the Maachathite, and all Mount Hermon, and all Bashan to Salcah;
Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka.
12 all the kingdom of Og in Bashan, who reigned in Ashtaroth and in Edrei; he was left of the remnant of the Rephaim, and Moses strikes them, and dispossesses them;
Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali.
13 and the sons of Israel did not dispossess the Geshurite, and the Maachathite; and Geshur and Maachath dwell in the midst of Israel to this day.
Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero.
14 Only, he has not given an inheritance to the tribe of Levi; fire-offerings of YHWH, God of Israel, [are] its inheritance, as He has spoken to it.
Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.
15 And Moses gives to the tribe of the sons of Reuben, for their families;
Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni.
16 and the border is to them from Aroer, which [is] on the edge of the Brook of Arnon, and the city which [is] in the midst of the brook, and all the plain by Medeba,
Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba.
17 Heshbon, and all its cities which [are] in the plain, Dibon, and Bamoth-Ba‘al, and Beth-Ba‘al-Meon,
Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni,
18 and Jahazah, and Kedemoth, and Mephaath,
Yahaza, Kedemoti, Mefaati.
19 and Kirjathaim, and Sibmah, and Zareth-Shahar, on the mountain of the valley,
Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa,
20 and Beth-Peor, and the Springs of Pisgah, and Beth-Jeshimoth,
Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti.
21 and all the cities of the plain, and all the kingdom of Sihon king of the Amorite, who reigned in Heshbon, whom Moses struck, with the princes of Midian, Evi, and Rekem, and Zur, and Hur, and Reba, princes of Sihon, inhabitants of the land.
Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni.
22 And the sons of Israel have slain Balaam, son of Beor, the diviner, with the sword, among their wounded ones.
Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga.
23 And the border of the sons of Reuben is the Jordan, and [its] border; this [is] the inheritance of the sons of Reuben, for their families, the cities and their villages.
Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.
24 And Moses gives to the tribe of Gad, to the sons of Gad, for their families;
Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili:
25 and the border to them is Jazer, and all the cities of Gilead, and half of the land of the sons of Ammon, to Aroer which [is] on the front of Rabbah,
Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba;
26 and from Heshbon to Ramath-Mispeh, and Betonim, and from Mahanaim to the border of Debir,
ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri.
27 and in the valley, Beth-Aram, and Beth-Nimrah, and Succoth, and Zaphon, the rest of the kingdom of Sihon king of Heshbon, the Jordan and [its] border, to the extremity of the Sea of Chinnereth, beyond the Jordan eastward.
Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto.
28 This [is] the inheritance of the sons of Gad, for their families, the cities and their villages.
Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi.
29 And Moses gives to the half-tribe of Manasseh; and it is to the half-tribe of the sons of Manasseh, for their families.
Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.
30 And their border is from Mahanaim, all Bashan, all the kingdom of Og king of Bashan, and all the small towns of Jair, which [are] in Bashan—sixty cities;
Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko.
31 and half of Gilead, and Ashteroth, and Edrei, cities of the kingdom of Og in Bashan, [are] to the sons of Machir, son of Manasseh, to the half of the sons of Machir, for their families.
Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.
32 These [are] they whom Moses caused to inherit in the plains of Moab beyond the Jordan, [by] Jericho, eastward;
Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani.
33 and Moses did not give an inheritance to the tribe of Levi; YHWH, God of Israel, Himself, [is] their inheritance, as He has spoken to them.
Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.